Kufunira Ena Zabwino

Kuchokera mu dongosolo lonse la makhalidwe abwino la Chisilamu, makhalidwe onse omwe Chisilamu chimalimbikitsa ndi odzadza ndi zokopa ndipo amawalitsa kukongola. Kaya ndi kulemekeza okalamba, kapena kuchitira chifundo achinyamata, kapena kukwaniritsa ufulu wa makolo ndi abale anu, zonse zimasonyeza ulemerero wapadera wa Chisilamu.

Komabe, moyo wa makhalidwe onse apamwambawa uli mu Hadith imodzi. Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: Dini ndi kufunira zabwino aliyense.

Ife ngati Asilamu, timaphunzitsidwa kuti monga momwe timazifunira zabwino ife eni – tiyeneranso kufunira zabwino ena. Monga momwe timafunira kuti ena ationetsere mtima wachikondi ndi chifundo, tiyeneranso kuonetsetsa kuti tikuchita chimodzimodzi kwa ena. Mu Hadith ina, Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati “Kondani ena zomwe mumakonda nokha.”

Kufunira anthu zabwino ndi kuwachitira chifundo ndi zina mwa mfundo zikuluzikulu za Imaan. Nthawi ina Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adayankhula ndi maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) nati: “Simungakhale ndi Imaan yangwiro kufikira mutachitira zabwino ndi kuinetsa mtima wa chifundo ku zolengedwa zina.”

Ma Swahaabah (radhwiyallah anhum) adayankha nati: “E, Mtumiki wa Allah!! Tonsefe timaonetsa chikondi tikamachita zinthu ndi anthu ena.”

Kenako Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati, “Sindikunena za inu kusonyeza kukoma mtima kwapadera ndi chifundo kwa anzanu apamtima kapena omwe mumawakonda kwambiri. M’malo mwake, ndikukhumba kuti muzionetsa kukoma mtima kwapadera ndi chifundo ku zolengedwa zonse momwe mumachitira kwa anzanu apamtima kapena omwe mumawakonda kwambiri.”

Ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) anatsatira uphungu wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) mmitima mwawo ndipo anautsatira mwachidwi kwambiri kotero kuti anaupanga kukhala maziko a miyoyo yawo. Chifukwa chake, tapeza kuti ena mwa iwo adalonjeza kukhulupirika pamaso pa Rasulullah swallallahu alaihi wasallam kuti nthawi zonse azifunira zabwino ena ndikusunga chidwi chawo mumtima nthawi zonse. ”

Mwa ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) amene adalumbira kukhulipilira mwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kufunira zabwino Ummah onse ndikuchita nawo zinthu mwa njira yabwino nthawi zonse anali Olemekezeka Jareer bin Abdillah Al-Bajali (radhwiyallahu anhu).

M’munsimu muli nkhani zochepa za moyo wa Sahaabi otchukayu zomwe zimaunikira khalidwe lokongola la Chisilamu lomwe linali chizindikiro m’moyo wake ndipo linawonekera padziko lonse lapansi.

Kugula Hatchi

Olemekezeka Jareer (radhwiyallahu anhu) tsiku lina anapita kumsika kukagula kavalo ndi kapolo wake omasuridwa. Jareer (radhiyallahu anhu) ataiona Hatchi imene anaikonda, anatumiza kapolo wake kwa mwiniwake kuti akamugulire.

Kapoloyo atapita kwa mwiniwakeyo ndi kumuuza kuti alipire ma dirham 300, koma mwiniwakeyo anakana chifukwa ankaona kuti kavaloyo anali wabwino kuposa mtengowo. Kapolo omasulidwayo anayamba kukambirana naye, ndipo pamapeto pake atalepherana mtengo, anamubweretsa mwiniwakeyo kuti akalankhule ndi mwini wake Jareer (radhwiyallahu anhu).

Atafika kwa Jareer (radhwiyallahu anhu) kapoloyo anafotokoza kuti anapempha kugula kavaloyo pa mtengo ma dirham 300, koma mwiniwakeyo akuiona kuchepa chifukwa amaona kuti kavaloyo ndi wabwino kwambiri.

Kenako ogulitsa uja adamufunsa Jareer (radhwiyallahu anhu) “Kodi ukuganiza kuti hatchiyi ikugwirizana ndi mtengo wa 300 dirhamu?” Jareer (radhwiyallahu anhu) adayankha: “Ayi, kavalo wako ndi wabwino kwambiri kuposa mtengo ukunenedwawo.” Kenako Jareer (radhwiyallahu anhu) adamufunsa kuti kavaloyo ndi ndalama zingati, ndipo pambuyo pake adagwirizana kuti alipira 700 kapena 800 dirham.

Kugulitsanako kutafika kumapeto, Olemekezeka Jareer radhwiyallahu anhu adadzudzula kapolo wakeyo chifukwa chofuna kugula chinthucho pamtengo ocheperapo, nati: “Bwanji umamubweretsa kwa ine uku akudandaula za Mtengo umene iye amafuna pomwe ine ndidamlonjeza Mtumiki swallallahu alaihi wasallam kuti ndidzamfunira zabwino Msilamu aliyense?”

Kupereka mwayi kwa Amene Anachita Nawe malonda

Imaam Abu Zur’ah rahimahullah mdzukulu wa Olemekezeka Jarir rahimahullah akusimba nkhani yotsatirayi yokhudza agogo ake Olemekezeka Jariir radhwiya-Allah anhu ndi kukhala ndi mtima owonetsa kufunikira kokwaniritsa lonjezo kudzera mu lonjezo lomwe adachita pamaso pa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam lowafunira zabwino nthawi zonse asilamu ena, Iye akuti:

“Nthawi zonse Jariir radhwiyallahu anhu akagulitsa kapena kugula chinthu, akamaliza malondawo, ankamuyankhula munthu amene akuchita naye malondayo kuti: ‘Zimene tatenga kwa inu ndi zabwino kwa ife kuposa zomwe takupatsani, pa chifukwa chimenechi tikukupatsani mwayi osintha chiganizo ngati mutafuna kubweza mutha kutero.’

Check Also

Kufunikira Koti Mwana Adzicheza Ndi Anthu Abwino

Mu kulera mwana, ndi zofunika kwambiri kuti makolo azionetsetsa kuti mwana wawo nthawi zonse apezeka …