Makolo Kutsogolera Mwa Chitsanzo

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anali olemekezeka kwambiri pa zolengedwa za Allah, Allah adamusankha kukhala Mtumiki Wake omaliza ndipo adamudalitsa ndi dini yolemekezeka kwambiri – dini ya Chisilamu yomwe ndi malamulo abwino kwambiri a moyo kuti munthu atsatire.

Munthu akalingalira pa umunthu odalitsika wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) amapeza kuti Allah adamudalitsa ndi khalidwe lapamwamba kwambiri komanso ulemu kotero kuti akhale chitsanzo chabwino kwambiri cha anthu kuti atengere mpaka kumapeto kwa nthawi.

Choncho, gawo lililonse la moyo odalitsika wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) linali lachitsanzo komanso lapadera. Kaya ali panyumba, pamene akuchita zinthu monga mwamuna kwa mkazi wake ndi bambo kwa ana ake, kapena mu mzikiti, ngati imaam wa mpingo, kapena m’dera monga mtsogoleri wa Asilamu, iye ankachita zinthu mwangwiro kwambiri ndipo anakhazikitsa muyezo wabwino kwambiri kwa anthu onse kuti atsatire.

Kotero, polera mwana, kufikira makolo atati asatengere moyo odalitsika ndi khalidwe la Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam), kubweretsa sunnah yake m’miyoyo yawo ndi m’nyumba mwawo, sadzaona ndikupeza zotsatira zomwe akufuna pakulera mwana wawo.Kungophunzitsa mwana mwa kumuphunzitsa Chisilamu ndi kumulangiza pakamwa za makhalidwe abwino ndi makhalidwe abwino sikungathandize ngati zochita za makolo, khalidwe lawo ndi moyo wawo zikutsutsana ndi mawu awo.

Chitani Zimene Mumalalikira

Munthu akamaphunzira miyoyo ya ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) ndi momwe adaphunzitsira ana awo ndikuwatsogolera ku makhalidwe ndi machitidwe abwino, mbali yoonekera bwino yomwe imaonekera ndi yakuti ankachita zomwe ankalalikira ndipo zochita zawo zinali umboni wa mawu awo.

Kudzera makolo kukhala ndi moyo odzipereka ndi olungama, momwemonso kukhala zitsanzo zabwino kwa ana awo, ayeneranso kuphunzitsa ana awo kukwaniritsa ufulu wa Allah ndi ufulu wa zolengedwa.

Ayenera kuwatsogolera pankhani ya ukhondo wa pakamwa, wakuthupi ndi wauzimu, ndipo kulimbikitsidwa kwakukulu kuyenera kuyikidwa pa kukhala ndi anthu ndi makhalidwe abwino. Pamene Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ankaphunzitsa ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) deen, ziphunzitso zake zidali zonse zokhuza mbali zonse za moyo wa munthu.

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) Kutumikira Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam)

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) adali otumikira wapadera wa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) yemwe adapatsidwa mwayi omutumikira Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kwa zaka khumi kufikira kumwalira kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam).

M’nthawi imeneyi ya zaka khumi, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ankakhala naye mwachikondi ndipo adamphunzitsa dini. Iye Akunena: “Ndidamutumikira Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kwa zaka khumi. Kwa nthawi yonseyi sadandimenye, kundilankhula mwaukali, kundilalatira ngakhale kundiyang’ana mwaukali.”

Mwa malangizo ndi ziphunzitso zomwe Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamupatsa ndi izi:

Maphunziro okhuza Kukwaniritsa Ufulu wa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndi zolengedwa zina.

‎Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati kwa Anas (radhwiyallahu anhu) Oh mwana wanga okondedwa! Sunga zinsinsi zanga, ndipo udzakhala okhulupirira weniweni.

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) akuti, “ Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) atandipatsa malangizo amenewa sindidaulure zinsinsi zake kwa wina aliyense ngakhale mayi anga ndi akazi olemekezeka a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kundifunsa zomwe wandiuza (pomwe iwo sadali kudziwa kuti zomwe Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adandiuza zidali zachinsinsi).

Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adatinso: “Oh mwana wanga okkndeka! Ngati uli ndi mwayi onditumizira duruud nthawi zonse panga zimenezo popeza angelo adzakupemphera kwa Allah chikhululuko.”

Maphunziro okhudza Ukhondo Wapathupi ndi Mkamwa komanso Kufunikira kwakukulu Kwa Ukhondo

Anas (radhwiyallahu anhu) adatinso: Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anandiuzanso kuti, “Oh mwana wanga okondedwa! Onetsetsa kuti wapanga wudhu okwanira. Ngati ungatero, angelo awiri (omwe amalemba zochita zako) adzakukonda ndipo udzapatsidwa barakah m’moyo wako.

“Eh Anas! Ukasamba podzichotsa umve waukulu sambitsa thupi lako mosamaritsa. Kupyolera mukusamba mosamaritsa, udzayeretsedwa ku machimo ako ang’onoang’ono.”

Kenako ndinamufunsa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti: “Kodi ndiwonetsetse bwanji kuti ndasamba thupi langa bwinobwino?” Adayankha Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam): “Posamba, onetsetsa kuti wanyowetsa mizu ya tsitsi lako ndikulitsuka bwinobwino khungu la thupi lako.”

Nayenso Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mwana wanga okondedwa! Khala ndi wudhu nthawi zonse ngati ungathe, pakuti amene angamwalire ali ndi wudhu amatengedwa kuti ndi shahid (ofera chikhulupiriro).

Maphunziro Okhudza Kukwaniritsa Ufulu wa Allah Tabaaraka Wataala kudzera Mu kuswali

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati kwa Anas (radhwiyallahu anhu) mwana wanga okondedwa! Yesetsanso kupemphera swala (za nafl) m’nyumba mwako. O Anas! Ukapanga ruku, onetsetsa kuti wagwira mawondo ako mwamphamvu, tambasura zala zako ndikusiya zigongono zako kutali ndi nthiti zako.

“O mwana wanga okondedwa! Ukaweramuja kuchokera pa ruku, lola ziwalo zako zonse kuti zikhanzikike ndikudekha (usanayambe kupita pa sajdah), chifukwa pa Tsiku la Chiweruzo, Allah sadzayang’ana ndi chifundo munthu amene saongora msana wake akaweramuka kuchoka pa ruku.

“O mwana wanga okondedwa! Ukapanga sajdah, ika mutu wako ndi manja ako pansi mokhanzikika, ndipo usapange sajdah mwachangu kwambiri kukhala ngati kujompha kwa tambala, ndipo usaike mikono yako pansi pomwe uli pa sajdah, ngati momwe amakhalira galu kapena nkhandwe. Pewa kuyang’ana uku ndi uku pamene uli pa swalaah, popeza izi ndi njira yowonongera (malipiro a) salaah yako.”

Kuphunzitsa Zokhudza kaKhalidwe ndi Anthu ndi Kuganizira Zabwino Msilamu Aliyense

Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati kwa Anas (radhwiyallahu anhu) “E mwana wanga okondedwa! Ukatuluka m’nyumba mwako (kupita kunja) pereka salamu kwa Msilamu aliyense amene ungakumane naye, chifukwa ngati ungatero, udzabwerera kunyumba utayeretsedwa ku machimo ako ang’onoang’ono.

“E mwana wanga okondedwa! Ukalowa m’nyumba mwako, pereka salaamu ku banja lako.”

Mu nkhani ina, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati, “Ukamutuluka m’nyumba mwako, ukakumana ndi Msilamu aliyense, uyenera kumva mumtima mwako kuti iyeyo ndi wabwino

Kaleredwe ka Ana

Anas (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati, “Tsiku lachisanu ndi chiwiri chibadwireni mwana aqiiqah iyenera kuchitidwa, ayenera kupatsidwa dzina la Chisilamu ndipo mutu wake uyenera kumetedwa.

“Mwana akafika zaka zisanu ndi ziwiri ayenera kuphunzitsidwa zamakhalidwe achisilamu. Akafika zaka zisanu ndi zinayi, malo ake ogona azikhala osiyana ndi alongo ake. Akafika zaka khumi ndi zitatu, azilangizidwa ndi kumenyedwa ngati sakuswali kapena kusala kudya.

“Akafika zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi kapena khumi ndi zisanu ndi ziwiri, abambo ake amukwatitse. Pambuyo pake, abambo ake amugwire dzanja ndikumuuza kuti, ‘Ine ndakuphunzitsa Chisilamu njira ya makhalidwe abwino, ndakuphunzitsa Dini ndipo ndakukwatitsa. Ndikufunafuna chitetezo mwa Allah kuti usakhale fitnah ndi mayesero kwa ine padziko lapansi komanso njira ya chilango kwa ine mu umoyo uli mkudza.

Maphunziro Okhudza Kusunga Sunnah Iliyonse ndi Njira Yokalowera ku Jannah

Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati kwa Anas radhwiyallahuanhu”Eh mwana wanga okondedwa! Ngati ungathe kukhala usana ndi usiku popanda kukhala ndi mtima wa sanje kwa aliyense mumtima mwako, chita zimenezo, chifukwa izi zidzapangitsa kuti hisaab yako (kuyankha mlandu m’bwalo la Allah) idzakhale yosavuta.”

Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anatinso, “Eh mwana wanga! Izi ( kusunga mtima wako oyera nthawi zonse) ndi Sunnah yanga. Munthu amene amakonda Sunnah yanga amandikonda, ndipo amene amandikonda adzakhala nane ku Jannah. Eh mwana wanga okondedwa! Ngati utsatira malangizo angawa ndiye kuti sipadzakhala chokondedwa kwa iwe kuposa imfa.”

Kuchokera pa zomwe zili pamwambazi, titha kumvetsetsa kufunikira kwakukulu kopereka malangizo ndi kuzindikira dini kwa mwana, komanso njira yachikondi, yodekha ndi yachifundo yomwe Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adagwiritsa ntchito pomuphunzitsa Anas radhwiyallahuanhu.

Mwana akaphunzitsidwa dini, chikondi ndi chisamaliro chotere, adzakhala ndi chidwi ndikukhala olimbikira pa dini mumtima mwake, ndipo pambuyo pake adzakhala moyo wake mogwirizana ndi malamulo a dini.

Check Also

Kufunikira Koti Mwana Adzicheza Ndi Anthu Abwino

Mu kulera mwana, ndi zofunika kwambiri kuti makolo azionetsetsa kuti mwana wawo nthawi zonse apezeka …