
Farwah bin Nawfal akufotokoza kuti nthawi ina yake, Abdullah bin Masud (radhwiyallahu anhu) adalankhula za Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ankamuyamikira kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe anali nazo. Iye adati:
إن معاذا كان أمة قانتا لله حنيفا
“Ndithu, Muaaz (bin Jabal) adali ummah (mtsogoleri wlotsogolera ena kunjira yoongoka), pomwe iye mwini anali odzipereka kwathunthu pa kulambira ndi kumvera Allah Ta’ala, ndipo aakhanzikika panjira yoongoka, osapatuka panjira iliyonse.”
Farwah bin Nawfal (rahimahullah) atamva kuyamikidwa kwakukuluku kwa Hazrat Abdullah bin Masud (radhwiyallahu ‘anhu) kumuyamikira Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu), adadabwa. Iye anati, “Ndinaganiza ndekha kuti mwina Abdullah bin Masud (radhwiyallahu anhu) walakwitsa (m’mawu ake poyamikira za Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu)), popeza kuyamikira kotere kukupezeka mu Quraan Majid kwa Ebrahim (‘alaihis salaam). Mu Quraan Majiid, Allah Ta’ala akumuyamikira Ebrahim (alaihis salaam) ponena kuti,
إن إبراهيم كان أمة قانتا لله حنيفا
Mwina, Abdullah bin Masud (radhwiyallahu ‘anhu) adaona kudabwa kwa Farwah bin Nawfal, kotero adamuuza kuti, “Kodi ukudziwa zomwe mawu onena kuti “Ummah” ndi “Qaanit” zimatanthauza (momwe zanenedweranso pomuyamika Ebrahim (alaihis salaam) mu Quraan Majid?” Ndinayankha kuti, “Allah ndiye akudziwa bwino.”
Abdullah bin Masud (radhwiyallahu ‘anhu) kenako anandiuza kuti, “Ummah kutanthauza munthu amene amaphunzitsa anthu zabwino (ndi kuwatsogolera ku dini); ndipo Qaanit imatanthauza munthu amene amamvera Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallahu alaihi wasallam) nthawi zonse. Makhalidwe amenewa amapezeka mwa Muaaz bin Jabal. Nthawi zonse ankaoneka kuti ankaphunzitsa anthu dini, pomwe nthawi zonse anali omvera komanso ogonjera mwa Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallahu alaihi wasallam).”
Kunena za mawu awa, Abdullah bin Masud (radhwiyallahu ‘anhu) adamufotokozera Farwah bin Nawfal kuti Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu anhu) adali ofanana ndi Nabi Ebrahim (‘alaihis salaam) m’makhalidwe awiri okongolawa, kotero anali oyenera kuyamikiridwa chifukwa chokhala ndi makhalidwe awiri okongolawa m’moyo mwake.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu