
Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) pomutumiza Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) ku Yemen, adamufunsa kuti, “Ndi njira yanji yomwe udzatsatire ukamakapereka chigamulo pa nkhani za Asilamu?”
Mu’aaz (Radhwiyallahu ‘anhu) adayankha kuti: “Ndidzagwiritsa ntchito Qur’aan.”
Kenako Nabi (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adamufunsa kuti: “Ngati lamulo silikupezeka mu Qur’aan udzatani?”
Iye adayankha kuti, “Ndidzagwiritsa nctchito mahaadith a Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam).”
Kenako Nabi (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adamufunsa kuti: “Ngati lamulo silikupezeka mu mmahadith, udzachita chiyani?”
Iye anayankha kuti: “Ndidzagwiritsa ntchito luso langa kulingalira (Ijtihaad) kuti ndithane ndi vuto.”
Atamva izi, Nabi (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adati: “Kuyamikidwa konse kukhale kwa Allah yemwe waiuzira Mthumwi ya Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) ( Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu)) ndi chitsogozo cholondola.” 1 (Sunan Tirmizi #1327)
Cholinga cha Nabi (Swallallahu ‘alaihi wasallam) kumufunsa Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) mwanjira yomwe ili pamwambapa chinali chakuti anthu azindikire kuthekera kwake ndikumudalira. Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) ankafuna kuti anthu aku Yemen azikafusa nkhani zawo za Dini kwa Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu), ndipo pambuyo pake azitsatira chigamulo chake mopanda kuka
ikira. (Al-Kawkabud Durri 2/344)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu