Mu Quraan Majid, Tsiku la Qiyaamah latchulidwa ndi mayina osiyanasiyana. Mayina ena mwa awa ndi “Tsiku la Mphotho ndi Kubwezera”, “Tsiku losonkhana”, “Tsiku la Kutayika ndi Kupindula” (lodzataika kwa osakhulupirira ndi la phindu kwa okhulupirira), ndi “Tsiku la Kukumana” (kutanthauza kukumana ndi Allah Talaa.
Tikayang’ana mayina awa, timapeza kuti dzina lililonse likumaonetsa momwe zinthu zidzakhalire pa Tsiku la Qiyaamah.
Mkakati mwa maina a Tsiku la Qiyaamah palinso “Tsiku la Chisoni”. Tsikuli lidzakhala tsiku lachisoni chachikulu kwa osakhulupirira, monga momwe Allah Talaa akufotokozera mu Quraan Majid:
وَانْذِرْهُمْ يَوْمَ الْحَسْرَةِ إِذْ قُضِيَ الْأَمْرُ
(0h Muhammad (swallahu alyhi wasallam) ! Achenjeze (osakhulupirira) za Tsiku la Madandaulo, pamene chigamulo chidzaperekedwe (kuti akalowe ku moto wa Jahannum ndikukhalamo kwamuyaya).
Kuchokera pa izi, tikuzindikira kuti Tsiku la Qiyaamah lidzakhala tsiku lodandaula mosaganizirika kwa osakhulupirira. Komabe, monga momwe lidzakhalire tsiku lachisoni kwa osakhulupirira, lidzakhalanso, pamlingo wina, tsiku la chisoni ndi lodandauritsa kwa okhulupirira ena.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu