Hazrat Uqbah bin Aamir radhiyallahu anhu akusimba kuti Hazrat Rasulullah adati: “Ndithu, Misikiti ili ndi zikhomo (omwe ndi anthu odzipereka ku musjid, ochita ibaadah, monga ngati zikhomo zimakhomeredwa pansi). anthu oterowo, ngati atachoka ku Musjid, angelo amawasowa, ndipo ngati ali odwala, angelo amawachezetsa, ndipo angelo akawaona amawalandira, ndipo ngati angafunike, angelo amawathandiza kukwaniritsa zosowa zawo (Pamene ali (m’Msikiti kukumbukira Allah), kuwerenga kwa Duroud ndi zina zotero), Angelo amawazungulira kuyambira Kumiyendo yawo mpaka Kumwamba. Manja awo amene akulembera Duruud (yomwe ikuwerengedwa ndi anthu awa) Wonjezerani (zikr ndi Duruud) Allah akuonjezereni (zabwino)!” Pamene anthu awa ayamba kupanga zikr ya Allah, makomo akumwamba amatsekulidwa kwa iwo, mapemphelo awo amayankhidwa, anamwali aku Jannah akusuzumira pansi pawo, ndipo Allah amawaikira Chifundo Chake chapadera pokhapokha ngati Sachita china chilichonse, ndipo sakuchoka. Akachoka munzikiti , angelo amadzuka ndi kufunafuna Misonkhano ina ya zikr.
Read More »Anthu amene asonkhana ndikuma werenga Durood akutidwa ndi chifundo cha Allah
Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki sallallahu alaih wasallam adati pali gulu la Angelo la Allah lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang'anaya yang'ana gulu la anthu omwe akupanga Dhikr, akakumana ndi gulu lachoncholo amalizungukira akatero amatumiza gulu lina la Angelo kupita kumwamba kukamudziwitsa Allah zomwe anthuwa akuchitazi, angelowa amauza Allah kuti "oh Allah, takumana ndi gulu la akapolo anu omwe akuutenga mtendere wanu kukhala chinthu chapamwamba kwambiri, a kuwerenga bukhu lanu, a kumuwerengera Durood Mtumiki wanu ndipo akukupemphani zosowa zawo za padziko lapansi komanso ku Aakhirah".Allah amayankha ndikunena kuti, akutileni mu chifundo changa"ndipo angelowa amachita chomwecho ndipo amapitiliza kunena mgululi muli uje ndi uje, amene ndi ochimwa kwambiri, komanso wangobwera kumapeto kwa zonse "Allah amayankha kuti, akutileni anthu onse mchifundo changa kuphatikizapo iyeyo popeza wina aliyense amene anakutiridwa mgululi alibe tsoka lirilonse komanso samanidwa chisomo changa."
Read More »Mngelo Amene Amayima pa Manda Odalitsika a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti Apereke Durood ya Ummah kwa Rasulullah Ummah
Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood.
Read More »Angelo ayenda dziko lonse kutolera Durood
Sayyiduna Abdullah bin Masuud (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "ndithu Allah ali ndi gulu la Angelo lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang'anaya yang'ana duruud ya ummah wanga ndipo amaifikitsa kwa ine."
Read More »Nkhani Yabwino Yochoka Kwa Allah Ta’ala Kwa Awo Amene Amawerenga Durood
Hazrat Abu Talhah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti: Tsiku lina m'mawa, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adabwera kwa ife ali wosangalala, mpaka chisangalalo chake chinawala kuchokera ku nkhope yake yodalitsika. Swahabah wina adafunsa: "E, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! Taona kuti lero mwakondwa kwambiri. Chisangalalocho chikuwoneka bwino pa nkhope yanu yodalitsika."Mtumiki (sallallahu alaih wasallam ) adayankha: "Inde, Mtumiki wochokera kwa Mbuye wanga anabwera ndi uthenga wonena kuti: " Munthu Amene adzakuwerengere Durood mwa ummah wako kamodzi, Allah adzamulembera zabwino khumi, ndi kufafaniza ndi kukhululukira machimo ake okwana khumi, ndi kukweza udindo wake ku Jannah m’magawo khumi, ndikumuyankha Duruud yake mofanananso (ndiye kuti Allah amutumizira chifundo ndi madalitso khumi).
Read More »Zofunika za Dunya ndi Aakhirah Zikwaniritsidwa chifukwa chowerenga Durood tsiku la Jumuah
Hazrat Anas bun Maalik (radhiyallahu ‘anhu) akusimba kuti Hazrat Mtumiki (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati: “Iwo mwa inu amene amawerengera duruud kwambiri mu dunya adzakhala oyandikira kwa ine pa tsiku la Qiyaamah nthawi iliyonse. Munthu amene? Munthu amene angandiwelengere Durood Usiku ndi usana wa lachisanuJumuah, Mulungu adzamkwaniritsilira zosoweka zake kwa zana limodzi, zofunika makumi asanu ndi awiri za Aakhirah ndi zofunika makumi atatu za dunya. Duruud ikatha kuwerengedwa Allah amaipeleka kwa mngelo yemwe adzaibweretse mmanda ndikadzamwalira ngati mmene mphatso imaperekedwera kwa inu, mngelo amandidziwitsa za muntbu amene wapanga duruud dzina lake komanso la bambo ake ndipo kenako ndimaisamala.
Read More »Kupeza nawo chiombolo cha Mtumiki sallallahu alaih wasallam
عن رويفع بن الثابت قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى على محمد وقال: اللهم أنزله المقعد المقرب عندك يوم القيامة، وجبت له شفاعتي (المعجم الكبرى للطبراني، الرقم: 4480 ،وإسناده حسن كما في مجمع الزوائد، الرقم: 17304) Olemekezeka Ruwaifidh (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) …
Read More »Kuonjezereka kwa ma riziqi
عن سهل بن سعد رضي الله عنه قال: جاء رجل إلى النبي صلى الله عليه وسلم فشكا إليه الفقر وضيق العيش أو المعاش فقال له رسول الله صلى الله عليه وسلم: إذا دخلت منزلك فسلم إن كان فيه أحد أو لم يكن فيه أحد ثم سلم علي واقرأ قل هو …
Read More »Sawabu zofanana ndikupereka sadaqah ukawerenga Duruud
Olemekezeka Abu Sa'eed khudri (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "Msilamu amene alibe kena kalikonse kuti apereke sadaqah adziwerenga duruud iyi mkatikati mwa duwa yake popeza idzampezetsa iyeyo sawabu zoti wapeleka sadaqah ndikumuyeretsa ku machimo.
Read More »Sawabu zapaderadera ukawerenga Durood ka 100
عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من صلى علي عشرا صلى الله عليه مئة ومن صلى علي مئة صلى الله عليه ألفا ومن زاد صبابة وشوقا كنت له شفيعا وشهيدا يوم القيامة (أخرجه أبو موسى المديني بسند قال الشيخ مغلطاى لا بأس به، …
Read More »