عن أبي طلحة الأنصاري رضي الله عنه قال أصبح رسول الله صلى الله عليه وسلم يوما طيب النفس يرى في وجهه البشر قالوا يا رسول الله أصبحت اليوم طيب النفس يرى في وجهك البشر قال أجل أتاني آت من ربي عز وجل فقال من صلى عليك من أمتك صلاة كتب الله له عشر حسنات ومحا عنه عشر سيئات ورفع له عشر درجات ورد عليه مثلها (سنن النسائى، الرقم: 1283، ورجاله موثقون كما في القول البديع صـ 248)
Hazrat Abu Talhah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti: Tsiku lina m’mawa, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adabwera kwa ife ali wosangalala, mpaka chisangalalo chake chinawala kuchokera ku nkhope yake yodalitsika. Swahabah wina adafunsa: “E, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! Taona kuti lero mwakondwa kwambiri. Chisangalalocho chikuwoneka bwino pa nkhope yanu yodalitsika.”
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam ) adayankha: “Inde, Mtumiki wochokera kwa Mbuye wanga anabwera ndi uthenga wonena kuti: ” Munthu Amene adzakuwerengere Durood mwa ummah wako kamodzi, Allah adzamulembera zabwino khumi, ndi kufafaniza ndi kukhululukira machimo ake okwana khumi, ndi kukweza udindo wake ku Jannah m’magawo khumi, ndikumuyankha Duruud yake mofanananso (ndiye kuti Allah amutumizira chifundo ndi madalitso khumi).
Chikondi cha Hazrat Uthmaan (radhiyallahu anhu) pa Hazrat Rasulullah (sallallahu alaih wasallam)
Nthawi ya Hudaybiyah, Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adatumidwa ndi Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kukakambirana ndi ma Quraish ku Makka Mukarramah. Pamene Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adanyamuka kupita ku Makka Mukarramah, ena mwa maswahabah adamchitira kaduka Uthmaan (radhiyallahu anhu) chifukwa chokwanitsa kuchita tawaaf ya nyumba ya Allah (ka’bah). Komano mthenga wa Allah (sallallahu alaih wasallam) adati, “Sindikuganiza kuti angakwanitse kuchita twawaaf popanda ine.”
Pamene Uthmaan (radhiyallahu anhu) adalowa munzinda wa Makkah Mukarramah, Abaan bin Said adamutenga ndikumuteteza ndipo adati kwa iye: “Ukhoza kuyenda momasuka kulikonse kumene ungafune. Palibe amene angakugwire pano.”
Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adachita zokambilana zake ndi Abu Sufyaan ndi nduna zina za Makkah Mukarramah mmalo mwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndipo pamene adatsala pang’ono kubwelera, ma Quraish adamuuza okha kuti: “Tsopano ukakhala kuno ku Makkah Mukarramah ukhoza kuchita tawaaf usanabwerere.” Uthmaan adayankha: “Zingatheke bwanji kwa ine kuchita tawaaf (popanda Hazrat Rasulullah)?”
Yankho limeneli silidawasangalatse ma Quraish ndipo adaganiza zomutsekera Uthmaan ku Makkah Mukarramah. Nkhani idawafikira Asilamu kuti Hazrat Uthmaan waphedwa. Pankhani imeneyi yomwe idafika kwa Hazrat Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam), adalumbirira Maswaabah onse kuti amenyane ndi dontho lomaliza la magazi awo. Akuraishi atamva izi khutu lidawagonjetsa ndipo nthawi yomweyo adammasula Uthmaan (radhiyallahu anhu). (Musnad Ahmed, 18910, Kunzul Umaal, 30152)