Anthu amene asonkhana ndikuma werenga Durood akutidwa ndi chifundo cha Allah

عن أنس رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: إن لله سيارة من الملائكة يطلبون حلق الذكر فإذا أتوا عليهم حفوا بهم ثم بعثوا رائدهم إلى السماء إلى رب العزة تبارك وتعالى فيقولون ربنا أتينا على عباد من عبادك يعظمون آلاءك ويتلون كتابك ويصلون على نبيك صلى الله عليه وسلم ويسئلونك لآخرتهم وديناهم فيقول تبارك وتعالى: غشوهم رحمتي فيقولون يا رب إن فيهم فلانا الخطاء إنما أعتقناهم إعتاقا فيقول تبارك وتعالى: غشوهم رحمتي فهم الجلساء لا يشقى بهم جليسهم (مسند البزار، الرقم: 6494 وسنده حسن كما في القول البديع صـ 267)

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki sallallahu alaih wasallam adati pali gulu la Angelo la Allah lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang’anaya yang’ana gulu la anthu omwe akupanga Dhikr, akakumana ndi gulu lachoncholo amalizungukira akatero amatumiza gulu lina la Angelo kupita kumwamba kukamudziwitsa Allah zomwe anthuwa akuchitazi, angelowa amauza Allah kuti “oh Allah, takumana ndi gulu la akapolo anu omwe akuutenga mtendere wanu kukhala chinthu chapamwamba kwambiri, a kuwerenga bukhu lanu, a kumuwerengera Durood Mtumiki wanu ndipo akukupemphani zosowa zawo za padziko lapansi komanso ku Aakhirah”.Allah amayankha ndikunena kuti, akutileni mu chifundo changa”ndipo angelowa amachita chomwecho ndipo amapitiliza kunena mgululi muli uje ndi uje, amene ndi ochimwa kwambiri, komanso wangobwera kumapeto kwa zonse “Allah amayankha kuti, akutileni anthu onse mchifundo changa kuphatikizapo iyeyo popeza wina aliyense amene anakutiridwa mgululi alibe tsoka lirilonse komanso samanidwa chisomo changa.”

Sayyiduna Abu Bakr (Radhwiyallahu Anhu) Kuphanga Lotchedwa Thaur

Adakali muphanga muja paulendo wa Hijra (kupita ku Madina) zanenedwa kuti Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) nkhawa zake zonse zinali zoti pasapezeke chilichonse chotuluka mudzenje chomwe chingapeleke vuto kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), kotero adayamba kutseka mayenje onse omwe anali mphangamo ndi zigamba zachovala chake chakumusi, komano padatsalira mayenje awiri omwe sadatsekedwe chifukwa chosowekera zotsekera, ndipo Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adatseka mayenjewo ndimapazi ake, kenaka Nabi (sallallahu alaih wasallam) adaika mutu wake odalitsika pantchafu za Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) mpaka anagona tulo.

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adakali ntulo chomwecho, Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adanva kulumidwa phazi lake ndinjoka yomwe idali kudzenje kuja, posafuna kumusokoneza Nabi (sallallahu alaih wasallam) mpang’ono pomwe, Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adapilira ku ululu omwe ankauva ndipo sadasunthe mpang’ono pomwe, komano chifukwa cha kunva kwambiri ululu ndikukanika kupilira, misozi idayamba kuyendelera pamasaya ake ndipo idagwera pankhope yodalitsika ya Nabi (sallallahu alaih wasallam).

Nabi (sallallahu alaih wasallam) mwadzidzidzi adadzuka ndikufunsa Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) kuti chachitika ndichani Sayyiduna Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) adayankha nati, “ndalumidwa ndinjoka, makolo anga apelekedwe nsembe chifukwa chainu oh Nabi (sallallahu alaih wasallam),” Nabi (sallallahu alaih wasallam) adapaka malovu ake pamalo olumidwawo ndipo nthawi yomweyo ululu udatha. (Mishkatul Masabeeh #6034)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …