عن عبد الله قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: إن لله ملائكة سياحين في الأرض يبلغوني من أمتي السلام (سنن النسائي، الرقم: 1282، صحيح ابن حبان، الرقم: 913)
Sayyiduna Abdullah bin Masuud (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “ndithu Allah ali ndi gulu la Angelo lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang’anaya yang’ana duruud ya ummah wanga ndipo amaifikitsa kwa ine.”
Chikondi Cha Sahabah wina pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)
Sahabah wina adabwera kwa Mtumiki sallallahu alaih wasallam ndikufuna kuti :oh Mthenga wa Allah kodi Qiyamah idzafika liti?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam adayankha pomufunsa kuti ndichani chomwe wachita sochinyeza kuikonzekera tsikulo? Sahabah adayankha nati, Oh Mthenga wa Allah sindikudzitenga kuti ndiri ndi swalah Saum kapena sadaqah zochuluka zomwe ndapanga komanso ndimakonda Allah kwambiri komanso Mtumiki wake mu mtima mwanga, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kenako adati, “ndithu pa tsiku lachiweruzo udzakhala limodzi ndi omwe umawakonda.”
Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akulongosora, “Palibe chidawangondweretsa maswahabah radhiyallahu anhum kuposa mawu amenewa.” (Sunan Tirmizi, 2385)