Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).
Read More »Yearly Archives: 2021
Kuikonzekera Ramadhan 1
1. Ikonzekereni bwino Ramadhan isanayambe, anthu m’mbuyomo ankaukonzekera mwezi umenewu patatsala miyezi isanu ndi umodzi. 2. Mwezi wa Rajab ukayamba mudzwelenga duwa iyi: اَللّٰهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْ رَجَبٍ وَّشَعْبَان وَبَلِّغْنَا رَمَضَان Oh Allah tidalitseni m’mwezi umenewu wa Rajab ndi Sha’baan, ndipo tiloreni kuti tifike mwezi wa Ramadhan. عن أنسٍ رضي …
Read More »Kupeza Chisangalaro Cha Allah Ta’ala
Sayyiduna Aishah (radhwiyallahu anha) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, amene angafune kudzakumana ndi Allah Allayo ali osangalatsidwa naye, akuyenera kuchulukitsa kundiwerengera Durood.
Read More »Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachiwiri
4. Sambitsani m'manja katatu.
Sayyiduna Humraan (rahimahullah) kapolo omasuridwa wa Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: Sayyiduna Uthman (radhwiiyallahu anhu) anapempha madzi (kuti awaonetse anthu kapangidwe ka wudhu. kenaka anayama kupanga wudhu posambitsa manja ake (mpaka molumikizanirana dzanja) katatu (izi zafotokozedwazi zomwe zikupezeka mu sahihul bukhari sayyiduna Uthman (Radhwyallahu anhu) anati: ndidamuona Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) akupanga wudhu motere)."
Read More »Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo
Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).
Read More »Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu – Gawo loyamba
1. Mukamapanga wudhu, yang’anani ku qiblah komanso mukhale malo okwera (e.g. pampando kuti madzi omwe agwiritsidwa kale ntchito asakudonthokereni), malo omwe mukupangira wudhu akhale oyera.
Read More »Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo
Sayyiduna Abdullah bin Mas´ud (radiyallah anhuma) akusimba kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallama) adati: ´Munthu amene adzakhale moyandikana kwambiri ndi ine (komanso oyenera kulandila chiombolo changa) patsiku lachiweruzo adzakhala amene amachulukitsa kunditumizira Durood padziko pano”
Read More »Ma Ubwino A Wudhu
1. Wudhu ndi chiyeretso chamachimo ang’ono ang’ono.
Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akuti; Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Amene angachite-wudhu, ndipo nawuchita wudhuwo mkachitidwe kabwino kwambiri, Machimo ake (ang´onoang´ono) amafudutidwa (ndipo amatsukidwa) kuchokera mthupi mwake mpakana amagwa machimo kudzera pansi pa-zikhadabo.
Read More »Kulandila Mphotho Zokwana Makumi Asanu Ndi Ziwiri
Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aas (radhwiyallahu anhuma) akufotokoza kuti, munthu amene angamfunile zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) kamodzi, Allah amanchitira chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70, angelo amamupemphera chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70 komanso ndi madalitso kukhala ngati malipilo a kumfunila mtumiki zabwino kamodzi. Choncho munthu amene akufuna kuti achulukitse kumfunila zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) ayenera kutero, komanso amene akufuna kuti achepetse akhonzanso kutero (ngati akufuna kuti apeze malipilo ochuluka akuyenera kuchulukitsa kumfunila zabwino Nabiiyo).
Read More »Masaail (Nfundo) Zina Zokhudza Kuzithandiza Kuchimbudzi
1. Funso: kodi ndizoloredwa munthu kuwerenga mabukhu monga nyuzi ndi magazini, kapena kugwiritsa ntchito foni, kapenanso kuseweretsa intaneti pamene ali m’nchimbudzi?
Yankho: Chimbudzi ndi malo amene munthu amazithandizirako, Choncho sizabwino kwa munthu kugwiritsa ntchito foni yake kapena kuwerenga uthenga uliwonse kapena kuwerenga nkhani m'nchimbudzi.
Read More »