Kulandila Mphotho Zokwana Makumi Asanu Ndi Ziwiri

عن عبد الرحمن بن مريح الخولاني قال سمعت أبا قيس مولى عمرو بن العاص يقول: سمعت عبد الله بن عمرو يقول: من صلى على رسول الله صلى الله عليه وسلم صلاة صلى الله عليه وملائكته سبعين صلاة فليقل عبد من ذلك أو ليكثر (مسند أحمد، الرقم: ٦٦٠٥، وإسناده حسن وحكمه الرفع إذ لا مجال للإجتهاد فيه كما في القول البديع صـ ٢٣٧)

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aas (radhwiyallahu anhuma) akufotokoza kuti, munthu amene angamfunile zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) kamodzi, Allah amanchitira chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70, angelo amamupemphera chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70 komanso ndi madalitso kukhala ngati malipilo a kumfunila mtumiki zabwino kamodzi. Choncho munthu amene akufuna kuti achulukitse kumfunila zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) ayenera kutero, komanso amene akufuna kuti achepetse akhonzanso kutero (ngati akufuna kuti apeze malipilo ochuluka akuyenera kuchulukitsa kumfunila zabwino Nabiiyo).

Kukhudzidwa Kwa Mzimayi Wachi Answaari Pa Nkhani Ya Nabi (Sallallahu Alaih Wasallam)

Ku nkhondo ya Uhud asilamu adavutika kwambiri ndi kugonja komanso asilamu ambiri adaphedwa. Pamene nkhani yokhudzana ndi asilikali akunkhondo aja inawapeza anthu a ku Madina, amayi adatuluka m’nyumba zawo kufuna kudziwa m’mene nkhondo imayendera.

Pamene anthu ena adakasonkhana pa malo ena ake mzimayi m’modzi wachi Ansaar adafunsa modandaula kuti kodi Nabi (sallallahu alaih wasallam) ali bwanji? Pamene mzimaiyu adauzidwa kuti bambo ake aphedwa adalankhula mawu oti “innaa lillaahi wa innaa ilaihi ra jiuun” ndipo mosaugwira mtima anabwerezanso funso lija lokhudzana ndi Nabi (sallallahu alaih wasallam).

Pamenepa adauzidwa kuti mamuna wake waphedwa, m’chimwene wake waphedwa komanso mwana wake wadulidwa dulidwa. Mosaugwira mtima, mzimayi uja anafunsabe za Nabi (sallallahu alaih wasallam).

Adauzidwa kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) alibwino bwino, komabe sanaupeze mtima, ndipo adakakamira kuti amuone Nabiiyo yekha ndi maso ake. Pamapeto pake maso ake atakhutitsidwa pomuona Nabi (sallallahu alaih wasallam), adayankhula kuti:

كل مصيبة بعدك جلل

O Nabi wa Allah! chifukwa cha madalitso okuonani inu nkhawa zonse zatha komanso mavuto onse atha. (Al-Kaamil Fit Taarikh 2/52)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …