Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

عن أبي أمامة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم أكثروا علي من الصلاة في كل يوم جمعة فإن صلاة أمتي تعرض علي في كل يوم جمعة فمن كان أكثرهم علي صلاة كان أقربهم مني منزلة (شعب الإيمان، الرقم: ٢٧٧٠، وإسناده حسن كما في الترغيب والترهيب، الرقم: ٢٥٨٣)

Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).

Ansaari (Mzika Yakumadina) Agwetsa Nyumba Yake

Sayyiduna Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) tsiku lina ankadutsa mumsewu wa m’madina munawwarah ndipo adaona nyumba yaitali (idali ndi domu pamwamba pake). Adawafunsa masahabah radiyallah anhu kuti: Kodi chimenechi mchiyani?  Masahabah (radhwiyallahu anhum) adati “Imeneyi ndi nyumba imene yamangidwa ndi m’modzi wa ma Ansaar (Mzika yakumadinah). Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) adangokhala chete.

Nthawi ina Ansaar amene adamanga nyumba yaitali uja (yokhala ndi domu pamwamba) adadzabwera kwa Rasulullah ndipo adapereka salaam kwa Iye. Komano, Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) adatembenuzira nkhope yake kumbali osamuyang´ana. Adabwereza (Ansaar uja) salaam komano Rasulullah (salallah alaih wasallama) adayankha. Sahabah ameneyi adali okhudzidwa kwambiri poona kuti Rasulullah (salallah alaih wasallama) sadamuyankhe salaam yake.

Pamene adawafunsa masahabah anzake, adamuuza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) anadutsa pa yumba yatsopano imene adamanga ndipo adafunsa zokhudza nyumbayo. Ndipo mwansangansanga adapita (Ansari uja) nakagumula nyumbayo ndiponso sadamuuze Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) zokhudza zomwe adachitazi.

Nthawi ina patadutsa nthawi, Rasulullah (salallah alaih wasallama) zidangochitika kudutsira njira imeneyo kachikenanso. Ndipo adafunsa, “Ili kuti nyumba imene idali ndi domu pamwamba ija, ndikukumbukira kuti nthawi ina ndidaiwona pamene ndimadutsa pamalo ano.?” Masahabah (radhwiyallahu anhum) adamuuza Nabiiyo zokhudza Ansaar kuti adaigumura poona kuti idam’kwiyitsa Rasulullah (sallallahu alaih wasallam). Panthawi imeneyo, Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) adati  “Chomangidwa chilichonse (chimene chamangidwa popanda kufunikira kwenikweni) udzakhala mtolo olemetsa wamunthuyo, kupatula chomanga chomwe chamangidwa pali zofunikira zenizeni.”

Chikhalidwe cha masahabah (radhwiyallahu anhum) chimaonetseratu poyera chikondi chenicheni komanso kudzipereka. Masahabah sadapilire Ndi mkwiyo wa Nabi (sallallahu alayihi wasallama) ndipo ngakhale mpang´ono pomwe, sadafune kumukwiyitsa Rasulullah (salallah alaih wasallama) kudzera m’machitidwe aliwonse, Iwo mwachanguchangu amasiya m’chitidwe omukwiyitsa. (Sunan Abi Dawood, #5237)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …