Uncategorized

Qunuut

3. Ndi sunnah kuswali Swalah ya Witr tsiku lililonse m’chaka chonse. Swalah ya Witri idzachitika mukatsiriza kuswali Fardh ndi Sunnah za Swalah ya Esha. M’chaka chonse, munthu akaswali Witr sangawerenge Qurnuot. Komabe zili sunnah kuwerenga Ounoot mu pa swala ya Witr mu theka lachiwiri la mwezi wa Ramadhaan (kuyambira pa …

Read More »

Qunuut

1. Ndi Sunnah kuwerenga Qunuut mu rakah yachiwiri ya Swalah ya Fajr. Qunuut idzawerengedwa mu rakah yachiwiri akaweramuka kuchokera pa Ruku. Adzayambe wawerenga tahmeed (ربنا لك الحمد) kenako adzayamba kuwerenga Qunut. 2. Powerenga Qur’an, munthu adzakweza manja ake mpaka pa chifuwa chake ndikuwerengaa dua monga momwe munthu amanyamulira manja ake …

Read More »

Zul Hijjah – Mwezi wa Haji ndi Qurbaani

Zul Hijjah ndi mwezi womaliza wa kalendala ya Chisilamu. Ngakhale mwezi wonse wa Zul Hijjah ndi wopatulika komanso wodalitsika, masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah ali ndi kupatulika kwakukulu ndi ubwino. Ponena za masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam wasallam) adati: “Masiku abwino kwambiri padziko lapansi …

Read More »

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa ulendowu, nthawi zina Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) ankayenda kutsogolo kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), ndipo nthawi zina ankayenda kumbuyo kwake, nthawi zina kumanja kwake ndipo nthawi zina kumanzere kwake. Nabi (sallallahu alaih wasallam) atazindikira machitidwe …

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani)

17. Mukuyenera kuigoneka nyama yanu chakumanzere kwanu itayang'ana ku Qiblah.

Olemekezeka Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adazinga ndi manja akenkhosa ziwiri yakuda ndiyoyera komanso zokhala ndi minyanga uku akuwerenga Tasmiyah ndi Takbeer ndipo adaika mwendo wake m'mbali mwake (chinyamacho chidagonekedwa chakumanzere ndicholinga choti chiyang'ane ku Qiblah).

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 3

Olemekezeka Aliyy (radhiyallahu anhu) akusimba kuti tsiku la Idi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza bibi Faatimah (radhiyallahu anha) uchitire umboni pamene chinyama chako chikuzingidwa (uwonelere). Pamene dontho la magazi oyamba likugwa pansi machimo akonso amakhululukidwa, nyama ndi magazi ake zidzaikidwa pasikelo ya ntchito zako zabwino ndikuchulukitsidwa ka 70, Abu Sa'eed khudri (radhiyallahu anhu) adamufunsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti, Oh Mthenga wa Allah kodi malipilo amenewa adzapelekedwa kwa akubanja lanu lokha chifukwa banja lanu limatchuka ndikukhala ndi madalitso kapena sawabu zimenezi ndi za asilamu onse? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati zavumbulutsidwa kwa akubanja langa komano sawabu zake ndi za nsilamu wina aliyense.

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 2

6.Ndi sunnah osadya chinachirichonse kummawa kwa tsiku la Eidul Adha kufikira mpakana utabwerako ku swalah ya Eid.

Sayyiduna Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku la Eidul Fitr Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankapita kukaswali Eid pokhapokha atadya kenakake, koma tsiku la Eidul Adha sankadya kalikonse pokhapokha atabwerako (kuchokera ku swalah ya Eidul Adha, akabwera ko koswali chinthu choyambilira kudya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe anazinga).

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama(qurbaani)

1. Qurbaani ndi sunna yomwe ili yaikulu kwambiri komanso ubembedzi wapamwamba kwambiri mu Deen. Mu Quraan yotamandika, zatchuridwa mwapaderadera zokhudzana ndi Qurbaani, komanso maubwino ochuluka ndi kufunikira kwake zalimbikitsidwa mma hadeeth a olemekezeka Rasulullaah (sallallahu alaihi wasallam). Allah ta’ala wanena kuti      لَن يَنَالَ اللَّـهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَاؤُهَا وَلَـٰكِن …

Read More »