عن عائشة قالت قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من سره أن يلقى الله وهو عليه راض فليكثر الصلاة علي (الكامل في ضعفاء الرجال ٦/٣٢، وإسناده ضعيف كما في القول البديع صـ ٢٦٧)
Sayyiduna Aishah (radhwiyallahu anha) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, amene angafune kudzakumana ndi Allah Allayo ali osangalatsidwa naye, akuyenera kuchulukitsa kundiwerengera Durood.
Chikondi Cha Sahabah Wina Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasalla)
Munthu wina adafunsa Aliy (radhwiyallahu anhu) kuti, ndi Chikondi chochuluka bwanji chomwe masahabah adali nacho pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)?
Aliy (Radhwiyallahu anhu) adayankha nati, ndikulumbira mwa Allah, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adali okondeka kwambiri kwa ife kuposa munthu wachuma, ana athu ndi amayi athu, ndipo kukhala limodzi ndi iye kunali kokoma kuposa kumwa madzi ozizira pamene uli ndi ludzu kwambiri. (As-Shifaa Pg, 52/2)