Ma ubwino omwe munthu yemwe amakaswalira kunzikiti amapeza

4. Kupitapita kumzikiti ndi njira yokhayo yomwe ingateteze Dini ya munthu.

عن معاذ بن جبل رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال إن الشيطان ذئب الإنسان كذئب الغنم يأخذ الشاة القاصية والناحية فإياكم والشعاب وعليكم بالجماعة والعامة والمسجد (الترغيب والترهيب، الرقم: 499)[1]

Sayyiduna Mu’adh bin Jabal (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, ndithudi satana ndi nkhandwe ya munthu (yomwe imansaka munthu kuti idye) monga m’mene nkhandwe ya ziweto imachitira yomwe imapezelera mbuzi yomwe ili yokhayokha, Pewani kukhala panokhanokha (kapena kutsata maganizo a okha) ndipo gwiritsitsani gulu la Ahlus-sunnah wal jamaa’ah ndikukhala limodzi ndi ummah komanso kulumikizana ndi mzikiti”.

5. Kupitapita kumzikiti ndi chizindikiro cha Imaan (Taqwa).

عن أبي سعيد رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا رأيتم الرجل يعتاد المسجد فاشهدوا له بالإيمان قال الله تعالى إنما يعمر مساجد الله من آمن بالله واليوم الآخر (سنن الترمذي، الرقم: 3093)[2]

Sayyiduna Abu Sa’eed khudri (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, mukaona kuti munthu wina wake akupitapita kumzikiti chitirani umboni za Dini yake, Allah Ta’ala akufotokoza mu Qur’an kuti, nyumba za Allah zimapitidwapitidwa okhawo omwe ali ndi chikhulupiliro chenicheni mwa Allah komanso tsiku lachiweruzo .”

6. Onse omwe amapita kumzikiti mu mdima apatsidwa nkhani yosangalatsa kuti adzalandira kuwala kokwanilira pa tsiku lachiweruzo.

عن بريدة الأسلمي رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال بشر المشائين في الظلم إلى المساجد بالنور التام يوم القيامة (سنن الترمذي، الرقم: 223)[3]

Sayyiduna Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, muuzeni nkhani yabwino munthu uyo amene mkatikati mwa mdima amapita kumzikiti kuti Allah adzamupatsa Nuur (kuwala) pa tsiku lachiweruzo.

7. Nthawi zonse munthu akamapita ku mzikiti m’mawa ndi madzulo Allah amamukonzera malo ku Jannah.

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من غدا إلى المسجد وراح أعد الله له نزله من الجنة كلما غدا أو راح (صحيح البخاري، الرقم: 662)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene amapita ku mzikiti m’mawa ndi madzulo, nthawi zonse akamayenda kupita ku mzikiti Allah amamukonzera malo ku Jannah.


[1] قال المنذري: رواه أحمد من رواية العلاء بن زياد عن معاذ ولم يسمع منه

[2] قال أبو عيسى: هذا حديث حسن غريب

[3] قال أبو عيسى: هذا حديث غريب

Check Also

Masunnah Ochita Mumzikiti

27. Khalani mwaulemu ndi modekha pamene muli mumzikiti musakhale moiwala kulemekezeka kwa mzikiti. Anthu ena …