Tafseer Ya Surah Bayyinah

بِسْمِ اللّٰهِ الرَّحْمٰنِ الرَّحِيمِ

لَمْ يَكُنِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ وَٱلْمُشْرِكِينَ مُنفَكِّينَ حَتَّىٰ تَأْتِيَهُمُ ٱلْبَيِّنَةُ ‎﴿١﴾‏ رَسُولٌ مِّنَ ٱللَّهِ يَتْلُوا صُحُفًا مُّطَهَّرَةً ‎﴿٢﴾‏ فِيهَا كُتُبٌ قَيِّمَةٌ ‎﴿٣﴾‏ وَمَا تَفَرَّقَ ٱلَّذِينَ أُوتُوْا ٱلْكِتٰبَ إِلَّا مِن م بَعْدِ مَا جَآءَتْهُمُ ٱلْبَيِّنَةُ ‎﴿٤﴾‏ وَمَآ أُمِرُوٓا إِلَّا لِيَعْبُدُوْا ٱللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُوْا ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤْتُوْا ٱلزَّكَوٰةَ ۚ  وَذٰلِكَ دِينُ ٱلْقَيِّمَةِ ‎﴿٥﴾‏ إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوْا مِنْ أَهْلِ ٱلْكِتٰبِ وَٱلْمُشْرِكِينَ فِى نَارِ جَهَنَّمَ خٰلِدِينَ فِيهَآ ۚ  أُوْلَٰٓئِكَ هُمْ شَرُّ ٱلْبَرِيَّةِ ‎﴿٦﴾ إِنَّ الَّذِينَ اٰمَنُوْا وَعَمِلُوْا الصّٰلِحٰتِ أُولَٰٓئِكَ هُمْ خَيْرُ الْبَرِيَّةِ ‎﴿٧﴾‏ جَزَآؤُهُمْ عِنْدَ رَبِّهِمْ جَنّٰتُ عَدْنٍ تَجْرِىْ مِن تَحْتِهَا الْأَنْهٰرُ خٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًا ۖ رَّضِىَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ ۚ ذٰلِكَ لِمَنْ خَشِىَ رَبَّهُۥ ‎﴿٨﴾‏

Anthu okanira mwa eni bukhu komanso ma Mushrikiin (opembedza mafano) sadafune kusiyana ndi umbuli wawo komanso zikhalidwe zawo kufikira chisonyezo chidawafikira amene ndi Mtumiki wa Allah kwawerengera makalata oyeretsedwa. M’mene mukupezeka malamulo olongosoredwa mom eka bwino. Omwe adapatsidwa mabukhu sadalekane/sadasemphane ndikugawanikana kufikira pomwe zisonyezo zoonekera poyera zidawadzera. Ndipo adangolamuridwa kumpembedza Allah kuchokera pansi pa mtima kukupanga kupembedza kukhala kwa Allah yekha osamphatikiza ndi zina. Ndikuswali komanso kupeleka Zakaat nthawi zonse ndikuti imeneyo ndiye dini yoongoka komanso.

Ndithu onse omwe adakanira (Mtumiki) mwa eni bukhu komanso ma Mushrikiin adzalowetsedwa ku moto komwe adzakhale mpaka muyaya, ndipo iwo ndiye zolengedwa zoipitsitsa, ndithu iwo amene adakhulupilira (mwa Allah ndi Mtumiki wake) ndikumachita ntchito zabwino, Iwo ndiye zolengedwa zabwino.

Malipiro awo kwa mbuye wawo ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje, adzakhala m’menemo muyaya, Allah adasangalatsidwa nawo ndipo nawonso adasangalatsidwa ndi Allah, zimenezo ndi za yemwe angaope mbuye wake (Allah).

Nthawi imene utumiki wa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) udali usadafike idali nyengi ya mdima mu Mbiri ya munthu, eni bukhu, Ayuda, Akhiristu komanso anthu opembedza mafano adali mu mdima waukulu konena kuti sizidali zotheka kuti akanatha kubweleranso. Adali mu mdima kwa nthawi yaitali kufikira mpaka umboni weniweni udawafikira poyera, umboni umenewu siunalinso wina koma Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwawerengera ma Ayah ochokera M’bukhu lomekezeka la Qur’an.

Pamene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawabweretsera Qur’an yolemekezeka komanso chipembedzo choonadi, adamuzindikira kuti ndi Mtumiki wa Allah monga m’mene ankamuzindimilira mwana wawo odzibelekera. Adalibe chikaiko chilichonse pa za utumiki wake ndipo adadziwa bwino lomwe kuti iye ndi Mtumiki otsiriza amene za kubwera kwake zidali zitanenedwa ndikulosedwa mabukhu awo. Komanso ankawauza ma Mushrikiin kuti posachedwapa Mtumiki awafikira. Ankanena kuti akabwera adzakhala oyambilira kumukhulupilira ndikumuthandizira kulimbana ndi ma Mushrikiin, ankachita kupanga duwa kupempha madalitso ndi thandizo kudzera mwa Mtumiki ameneyu, komano Mtumiki atabwera adamkana.

 

وَمَا تَفَرَّقَ ٱلَّذِينَ أُوتُوْا ٱلْكِتٰبَ إِلَّا مِن م بَعْدِ مَا جَآءَتْهُمُ ٱلْبَيِّنَةُ ‎﴿٤﴾‏ وَمَآ أُمِرُوٓا إِلَّا لِيَعْبُدُوْا ٱللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُوْا ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤْتُوْا ٱلزَّكَوٰةَ ۚ  وَذٰلِكَ دِينُ ٱلْقَيِّمَةِ ‎﴿٥﴾

Ndipo sadakhale osemphana anthu amemene adalandila mabukuh (Ayudandi akhristu) (nagawikana ) Mpakana zizindikiro zoonekera poyera zinabwera kwa iwo. Ndipo iwo analamuridwa kuti azimpembedza Allah Taala yekha modziyeretsa.Adzipanga mapemphero awo mozipereka kwa Mulungu yekha basi popanda kumuphatikiza ndichili chonse, Ndiponso kuti azipemphera swalat munthawi yake moyenera komanso kuti adzipereka chopereka chaulere (zakat) ndipo chimenecho ndicho chipembedzo cholungama ndichoyenera.

Adalamuridwa kuti atsatire Mtumiki (sallallahu alayhi wasalama), koma mwatsoka adasiya njira yowongoka nakhala osatsatira mavesi ofotokoza momveka bwino amu Quran yolemekezeka.

اِنَّ الَّذِیۡنَ کَفَرُوۡا مِنۡ اَہۡلِ الۡکِتٰبِ وَ الۡمُشۡرِکِیۡنَ فِیۡ نَارِ جَہَنَّمَ خٰلِدِیۡنَ فِیۡہَا ؕ اُولٰٓئِکَ ہُمۡ شَرُّ الۡبَرِیَّۃِ ؕ﴿۶﴾

Ndithu amene sadakhulupilire kuchokera mwa anthu amene adalandira mabukhu kale (ayuda ndi akhristu) komanso opembedza mafano (Mushirikiin), onsewa adzakhala ku moto wa Gehena mpaka Muyaya, ndipo iwowo ndiye zilengedwe zoyipitsitsa.

Maziko achipulumutso ndiye kukhala ndi imaan (Chikhulupiliro). Amene ali ndi Imaan (chikhulupiliro mwa Allah) akalowa ku paradiso ndipo adzakhala kumeneko mpaka muyaya. Chimodzimodzinso, amene sali okhulupilira mwa Allah (Opanda imaan) adzaponyedwa m’moto wa Gehena ndipo azidzavutika umoyo wonse ndi zilango.

Vesi imeneyi ikufotokoza momveka bwino kwambiri kuti Ayuda ndi a Khristu akakhala kumoto wagehena mpaka muyaya. Anthu ena ochuluka amaganiza kuti; Ayuda ndi a khristu amatsatira mabukhu ovumbulutsidwa akale Taurat (chipangano chakale) komanso Injil (chipangano chatsopano) amene adabvumbulutsidwa ndi Allah Taala ndiye kuti adzapeza Chipulumutso patsiku lachiweruzo ndikukalowa ku Paradiso. Choncho Mu ndime imeneyi, Allah Taala akuonetseratu poyera kuti maziko achipulumutso ndikubweretsa Imaani kukhulupilira mwa Allah Taala ndi Mtumiki wake (sallallahu alayhi wasallam) ndi dini yokwanilira ya Muhammad (sallallah alayhi wasallam).

Chonchotu, Ayuda ndi akhristu akukanira utumiki wa Muhammad ndi chipembembedzo cha Muhammad (sallallah alayhi wasalllam) choncho iwowo akhozeredwa moto wa gehena ndipo adzakhalako mpaka muyaya. Ena mwamaziko akulu achikuhulupiliro ndiye kukhulupilira mwa atumiki onse a Mulungu. Kukanira Mtumiki mmodzi wa Allah ndichimodzimodzi kukanira atumiki onse a Allah. Choncho chifukwa choti a Yuda ndi a khristu akukanira utumiki wa Muhammad (sallallahu alayhi wasallam), ndiye kuti akanira atumiki onse a Allah (Popezanso atumiki onsewo adawawuza anthu awo zokhudza utumiki wa Muhammad (sallallah alayhi wasallam)) ndipo iwo awonetsera kukhala osamukhulupilira.

Ndichifukwa chake Allah Taala mu ndime imeneyi akulengezetsa kuti iwowo akakhala kumoto wa gehena mpaka muyaya.
ndiponso wawatchula iwowo kuti ndizolengedwa zoyipitsitsa muzolengedwa zonse. Kuchokera muzolengedwa zonse tikudziwa kuti anthu, nyama, njoka, ziwanda etc, anthu osakhulupililawa (ayuda ndi akhristu) ndi anthu oyipitsitsa kuposa chirichonse chimene timachidziwa kuti choipitsitsacho. Ngakhalebe iwowo adalandira mabukhu kale, koma chifukwa choti iwowo adagawikana nakanira choonadi, kumeneku ndiko kunyozeka kwawo, kuchoka kwa ulemerero kwawo pamaso pa Allah Taala.

إِنَّ الَّذِينَ اٰمَنُوْا وَعَمِلُوْا الصّٰلِحٰتِ أُولَٰٓئِكَ هُمْ خَيْرُ الْبَرِيَّةِ ‎﴿٧﴾‏ جَزَآؤُهُمْ عِنْدَ رَبِّهِمْ جَنّٰتُ عَدْنٍ تَجْرِىْ مِن تَحْتِهَا الْأَنْهٰرُ خٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًا ۖ رَّضِىَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ ۚ ذٰلِكَ لِمَنْ خَشِىَ رَبَّهُۥ ‎﴿٨﴾‏

Malipiro awo kwa mbuye wawo ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje, adzakhala m’menemo muyaya, Allah adasangalatsidwa nawo ndipo nawonso adasangalatsidwa ndi Allah, zimenezo ndi za yemwe angaope mbuye wake (Allah).

Pa tsiku la Qiyamah Allah Ta’ala adzawaitana anthu a ku Jannah ndikuwafunsa kuti, “kodi mwasangalatsidwa nane?” adzayankha kunena kuti, Oh Allah tusasangalale nanu bwanji kumachita kuti mwatidalitsa ndi mtendere umene palibenso wina amene mudamudalitsako ndi mtendere ngati umenewu? kenako Allah adzanane kuti, Tsopano ndakupanga ku sangalala nanu kwanga kukhala kwamuyaya ndipo sindidzakhumudwa nanunso.

Uwu udzakhala mtendere waukulu ku Jannah, Allah kuwakondetsetsa anthu a ku Jannah monena kuti kuyambira pamenepo Allah sadzakhumudwa nawonso anthu amenewo chisangalalo chomwe anthu amenewa adzakhale nacho chokwera chifukwa cha chisangalalo cha Allah chidzaposa chimwemwe China chilichonse chomwe angadzachipeze ku Jannako.

Sawabu zimenezi zokilowera ku Jannazi ndikusangalatsidwa ndi Allah chotere ndi zosavuta kuzipeza kwa munthu amene ali ndi Imaan (chikhulupiliro), chikufunika ndi Taqwa yokha basi kumuopa Allah kuchokera pansi pa Mtima, ngati Nsilamu nthawi zonse angamalingalire zodzaima pamanso pa Allah pa tsiku lachiweruzo ndithu munthu ameneyo adzakonza umoyo wake ndi kudzitalikitsa ku machimo, komano chomwe chingampangitse munthu kusiya njira yoongoka ndiye kusalabadira za zomwe zidzachitike pa tsiku lachiweruzo komanso kusalabadira zoti udzaima pamanso pa Allah ndi kuyankha mafunso.
Mtima wa munthungati ungakhudzike ndi malingaliro oti tsiku linalake adzakaima pamanso pa Allah ndipo liwu lina lirilonse lomwe adayankhula adzakafunsaidwa, komanso kena kalikonse kamene angachite adzayankha komanso kuti adzakafunsaidwa za malamulo a Allah komanso ma Ufulu a anthu ena, munthu ameneyo adzakinzekera za umoyo umene uli nkudza ndi kukonza umoyo wake wa kakhalidwe ka padziko lapansi pano.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …