Masunnah Ochita Mumzikiti

4. Pitani kumzikiti modekha ndi mwa ulemu. musapite mukuthamanga. [1]

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول إذا أقيمت الصلاة فلا تأتوها تسعون وأتوها تمشون عليكم السكينة فما أدركتم فصلوا وما فاتكم فأتموا (صحيح البخاري، الرقم: 908)

Olemekezeka Abu Hurayrah (radhiyallah anhu) adati; ndinamumva Mtumiki wa Allah (sallallah alayhi wasallam) akunena kuti; Pamene iqqamah yachitidwa, musapite kukapemphera swala pamene mukuthamanga, Mmalo mwake, Mukuyenera kuyenda modekha ndi mwaulemu. Gawo laswalah limene mwalipeza ndi Imaam, pempherani. Ndipo gawo lomwe lakudutsani kwanirisani. (pamene imaam watsiriza swalah)

5. Lowani mumzikiti pamene muli ndi wudhu. Ndipo sizabwino (makruhu)kulowa mumzikiti mulibe wudhu.[2]

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال لا يزال العبد في صلاة ما كان في مصلاه ينتظر الصلاة وتقول الملائكة اللهم اغفر له اللهم ارحمه حتى ينصرف أو يحدث قلت ما يحدث قال يفسو أو يضرط (صحيح مسلم، الرقم: 649)

Olemekezeka Abu hurayrah (radhiyallah anhu) akusimba kuti; Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adati; Pamene munthu wakhala pamalo opemphelera swalah podikilira kuti apemphere swalah, amalandira malipilo ofanana ndi munthu amene akupemphera swalah, ndipo angelo amapitiriza kumupemphera maduwa ponena kuti; O Allah mukukhululukireni ameneyi,O Allah muchitireni chifundo, ndipo amakhalabe akulandiera malipiro {sawabu) mpaka pa nthawi yomwe watuluka mumnzikitimo kapena pa nthawi yomwe wadula wudhu wake pamene ali munzikitimo. Swahaba wina anafunsa nati; Kodi munthu angadule bwanji wudhu? Mtumiki (sallallah alayhi wasalllam) adati ´´ngati munthuyo watulutsa mpweya kuchokera kumbuyo (kuphwisa) pamenepo wudhu wake umaduka.


[1] قال المصنف رحمه الله (ويستحب لمن قصد الجماعة أن يمشي إليها وعليه السكينة والوقار) … قد ذكرنا أن مذهبنا أن السنة لقاصد الجماعة أن يمشي بسكينة سواء خاف فوت تكبيرة الإحرام أم لا (المجموع شرح المهذب 4/73)

ولو خاف فوت التكبيرة لو لم يسرع لم يسن له الإسراع بل يمشي بسكينة كما لو أمن فوتها لخبر إذا أقيمت الصلاة فلا تأتوها تسعون وأتوها تمشون وعليكم السكينة والوقار فما أدركتم فصلوا وما فاتكم فأتموا (نهاية المحتاج 2/144-145)

[2] ويكره كما في الإحياء دخول المسجد من غير وضوء (نهاية المحتاج 2/120)

ويكره أن يدخل المسجد بغير وضوء (مغني المحتاج 1/510)

Check Also

Masunnah Ochita Mumzikiti

27. Khalani mwaulemu ndi modekha pamene muli mumzikiti musakhale moiwala kulemekezeka kwa mzikiti. Anthu ena …