Sunna Za Msikiti

37. Ulumikizitseni mtima wanu nthawi zonse ndiku mzikiti. Mwachitsanzo pamene mukuchoka mumzikiti pomwe mwatsiriza swalah yanu, pangani niya kuti mubweranso kumzikitiko paswala yotsatirayo ndipo idikireni swalayo ndimtima onse.[1]

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال ألا أدلكم على ما يمحو الله به الخطايا ويرفع به الدرجات قالوا بلى يا رسول الله قال إسباغ الوضوء على المكاره وكثرة الخطا إلى المساجد وانتظار الصلاة بعد الصلاة فذلكم الرباط (صحيح مسلم، الرقم: 251)

Olemekezeka Abuu Hurayrah (radhwiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallah alayhi wasallama) adawafunsa maswahaba (radhwiyallah anhumu) nati; Kodi ndikuuzeni ntchito imene Allah angakukhululukireni nayo machimo ndikukukwezani nyota zanu (ku jannah)? Maswahabah (radhwiyallahu anhum) adayankha nati; Inde tiwuzeni oh Inu Mtumiki wa Mulungu (swallallah alayhi wasallama). Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) adati; Pangani wuzu wokwanilila ngakhale kuli kovuta kutero, yendani mapazi ochuluka popita kumzikiti ndiponso dikilirani swalah ina pambuyo popemphera swalah ina. Ntchito zimenezi zikufanana ndi ntchito Malile adziko lachislamu kwa adani achisilamu.(kudzera mmachitidwe amenewa munthu amadziteteza mwini kuchokera kumanong´onong´o oipa amwini wakeyo komanso a satana, chimodzimodzi amene amayang´anira malire adziko la asilamu poteteza kwa adani achisilamu)

38. Osakongoletsa mizikiti (monga ngati kujambula pokongoletsa mmakoma). Mchitidwe umenewu ndi Makrooh.[2]

عن ابن عباس رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم ما أمرت بتشييد المساجد قال ابن عباس لتزخرفنها كما زخرفت اليهود والنصارى (سنن أبي داود، الرقم: 448)[3]

Olemekezeka Ibn Abbas (radhwiyallahu anhumaa) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alayhi wasallama) adati: Sindinalamulidwe kukweza mnyumba yamzikiti (popanda kufunikira pongofuna kukongoletsa basi). Olemekezeka Ibn Abbas (radhiyallahu anhuma) adati: Idzafika nthawi imene mudzakhale mukukongoletsa kwambiri mizikiti moposera muyeso wake wa shariyah mofanana ngati mmene a Yuda ndi a Khristu adakongoleletsera malo awo opembedzeramo.


[1] عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال سبعة يظلهم الله تعالى في ظله يوم لا ظل إلا ظله إمام عدل وشاب نشأ في عبادة الله ورجل قلبه معلق في المساجد ورجلان تحابا في الله اجتمعا عليه وتفرقا عليه ورجل دعته امرأة ذات منصب وجمال فقال إني أخاف الله ورجل تصدق بصدقة فأخفاها حتى لا تعلم شماله ما تنفق يمينه ورجل ذكر الله خاليا ففاضت عيناه (صحيح البخاري، الرقم: 1423)

[2] عن أنس رضي الله عنه أن النبي صلى الله عليه وسلم قال لا تقوم الساعة حتى يتباهى الناس في المساجد (سنن أبي داود، الرقم: 449)

يكره زخرفة المسجد ونقشه وتزيينه للأحاديث المشهورة (المجموع شرح المهذب 2/144)

[3] هذا الحديث سكت عنه أبو داود والمنذري (مختصر سنن أبي داود 1/189)

Check Also

Masunnah Ochita Mumzikiti

26 Osaipitsira mumzikiti. mwachitsanzo kulavulira mumzikiti kapena kumina mumzikiti mpaka zoipazo maminawo kapena malovuwo mkugwera …