1. Qurbaani ndi sunna yomwe ili yaikulu kwambiri komanso ubembedzi wapamwamba kwambiri mu Deen. Mu Quraan yotamandika, zatchuridwa mwapaderadera zokhudzana ndi Qurbaani, komanso maubwino ochuluka ndi kufunikira kwake zalimbikitsidwa mma hadeeth a olemekezeka Rasulullaah (sallallahu alaihi wasallam). Allah ta’ala wanena kuti
لَن يَنَالَ اللَّـهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَاؤُهَا وَلَـٰكِن يَنَالُهُ التَّقْوَىٰ مِنكُمْ
Sikuti ndi nyama kapena magazi (a nyama zomwe mukuzingazo) zomwe zimakanika kwa Allah, koma ndi kuyeretsedwa kwa mitima yanu (kupanga chifukwa Allah ) ndi kumene kumamufika Allah. (surah hajj v. 37)
عن زيد بن أرقم رضي الله عنه قال قال أصحاب رسول الله صلى الله عليه وسلم : يا رسول الله ما هذه الأضاحي ؟ قال : سنة أبيكم إبراهيم عليه السلام. قالوا : فما لنا فيها يا رسول الله ؟ قال : بكل شعرة حسنة . قالوا : فالصوف يا رسول الله ؟ قال : بكل شعرة من الصوف حسنة (سنن ابن ماجة، الرقم 3127)
Hazrat Zaid bin Arqam (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti ma swahaba nthawi ina anamufunsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti O Mtumiki wa Allah, kodi tsinde la mchitidwe wa Qurbaani ndi liti? Rasulullah (sallallahu alaih wasallam anayankha kuti ndi mchitidwe wa agogo anu Ibrahim (alaihis salaam). Ma swahaba anafunsanso kuti ndi malipilo anji amene tingapeze mukupanga mchitidwe umenewu? Rasulullaah (sallallahu alaih wasallam) anayankha tuti ka bweya kena kali konse komwe kali pathupi la ngamila muzipezelapo zabwino. Maswahaba anafunsanso kuti nanga ubweya wa nkhosa? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anayankhanso kuti pa ubweya uliwonse wa nkhosa muzipezelapo zabwino.
2. Pa tsiku la idi ntchito yomwe imakhala yokondedwa kwambiri kwa Allah ndi kukhetsa mwazi (kuzinga nyama).
عن عائشة أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال: ما عمل آدمي من عمل يوم النحر أحب إلى الله من إهراق الدم، إنه ليأتي يوم القيامة بقرونها وأشعارها وأظلافها، وأن الدم ليقع من الله بمكان قبل أن يقع من الأرض، فطيبوا بها نفسا (سنن الترمذي، الرقم 1493)
Hazrat Aisha (radhiyallahu anha) akulongosora kuti Rasulullaah (swallallaahu alaihi wasallam) anati, palibe ntchito iliyonse Imene kapolo wa Allah angagwire mmasiku a Qurbaani imene imakhala yokondedwa kwambiri kwa Allah yoposa kukhetsa mwazi (nsembe ya zinyama). Chinyama chomwe chinazingidwa Chidzabwera tsiku la qiyaamah chili ndi nyanga zake, ubweya wake ndi zikhatho zake. Nsembe ya nyama imalandiridwa ndi Allah magazi ake asanadonthere pansi. Choncho perekani nsembe mwa nsangala (mmtima wanu uli osangalala komanso okondwera kukwaniritsa chilamulo cha Allah.)
3. Isanati Qurbaani komanso panthawi yopanga Qurbaani munthu siukuyenera kukhala wankhanza kuchipangira chinyamacho. Ayenera kuchimvera chisoni komanso ubwino.
عن شداد بن أوس عن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال : إن الله تبارك وتعالى كتب الإحسان على كل شيء فإذا قتلتم فأحسنوا القتلة وإذا ذبحتم فأحسنوا الذبح وليحد أحدكم شفرته وليرح ذبيحته.(صحيح مسلم، الرقم 1955)
Hazrat Shaddaad bin Aus (radhiyallahu anhu) anati Allaah ta’ala wakakamiza kumvera chisoni zolengedwa zonse. Mukamapha mdani ku nkhondo kumapha Mu njira yabwino, (osalidula thupilo mtiziduswa ziduswa) mukamazinganso nyama zingani mwa ubwino komanso kumanora kwambiri mpeni ndi kuchilola chinyamacho kuti chife mosavuta.
4. Ngati munthu ali ndi kuthekera ndi zabwino kuti azinge mmalo mwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ma swahaba ndi anthu Ena onse olumngama.
عن علي رضي الله عنه أنه كان يضحى بكبشين أحدهما عن النبي صلى الله عليه و سلم والآخر عن نفسه فقيل له فقال أمرني به يعني النبي صلى الله عليه و سلم فلا أدعه أبدا (سنن الترمذي، الرقم 1495)
Zafotokozedwa zokhudzana ndi hazrat Ali (radhiyallahu anhu) kuti (chaka chilichonse munthawi ya qurbaani) ankazinga nkhosa ziwiri, ina yake ndipo inayo mmalo mwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Atafunsidwa pankhani imeneyi anayankha kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anandiuza kuti ndizipanga zimenezo ndipo sindidzasiya ngati ndingakhalabe ndiri moyo.
5. Munthu ayenera kuyesetsa kuti akwaniritse chikakamizo cha Qurbaani. Kupanga qurbaani tsiku loyambilira ndi zabwino kwambiri kusiyana ndi tsiku lachiwiri. Ndipo Kupanga mutsiku la chiwiri ndi zabwino kwambiri kusiyana ndi Kupanga tsiku la chitatu.
عن جابر بن عبد الله قال : شهدت مع النبي صلى الله عليه و سلم الأضحى بالمصلى فلما قضى خطبته نزل عن منبره فأتى بكبش فذبحه رسول الله صلى الله عليه و سلم بيده وقال بسم الله والله أكبر هذا عني وعمن لم يضح من أمتي (سنن الترمذي، الرقم 1521)
Hazrat Jaabir akulongosola kuti ndinalipo kumalo kopemphelera idi pamene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamaliza khutbah anatsika pa nthanthi za mimbar ndipo nkhosa inabweretsedwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ya qurbaani. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankazinga nkhosa ija ndi manja ake olemekezeka uku akuwerenga takbeer yoti بسم الله والله اكبر komanso ankanena kuti iyi ndi qurbaani imene ndikuzizingira ndekha komanso anthu a ummah wanga amene sangakwanitse kupeza chinyama choti azinge pa qurbaani.