1. Ndi Sunnah kuwerenga Qunuut mu rakah yachiwiri ya Swalah ya Fajr. Qunuut idzawerengedwa mu rakah yachiwiri akaweramuka kuchokera pa Ruku. Adzayambe wawerenga tahmeed (ربنا لك الحمد) kenako adzayamba kuwerenga Qunut.
2. Powerenga Qur’an, munthu adzakweza manja ake mpaka pa chifuwa chake ndikuwerengaa dua monga momwe munthu amanyamulira manja ake pachifuwa chake akamawerenga duwa pambuyo pa Swalaah. Komabe, munthu sangayendetse manja ake pankhope pake pambuyo pa Qunuutu. Qunuut ya Swalah ya Fajr ndi:
اَللّٰهُمَّ اهْدِنِيْ فِيْمَنْ هَدَيْتَ وَعَافِنِيْ فِيْمَنْ عَافَيْتَ وَتَوَلَّنِيْ فِيْمَنْ تَوَلَّيْتَ وَبَارِكْ لِيْ فِيْمَا أَعْطَيْتَ وَقِنِيْ شَرَّ مَا قَضَيْتَ إِنَّكَ تَقْضِيْ وَلَا يُقْضٰى عَلَيْكَ إِنَّهُ لَا يَذِّلُّ مَنْ وَّالَيْتَ وَلَا يَعِزُّ مَنْ عَادَيْتَ تَبَارَكْتَ رَبَّنَا وَتَعَالَيْتَ فَلَكَ الْحَمْدُ عَلٰى مَا قَضَيْتَ أَسْتَغْفِرُكَ وَأَتُوْبُ إِلَيْكَ وَصَلّٰى اللهُ عَلٰى النَّبِيِّ وآلِهِ
E, Allah Nditsogolereni pamodzi ndi amene mudawaongola, Ndipatseni ndifewetsereni pamodzi ndi amene mudawafewetsera, Ndithandizeni pa zinthu zanga (ndipo ndithandizeni) pamodzi ndi amene mudawasamalira (ndikuwathandizira). Ndipatseni mabaraka (madalitso) m’zimene mwandipatsa, Ndipulumutseni ku zoipa zomwe mudandikhanzikitsira. Ndithu, Inu nokha ndi amene mumaweruza, ndipo palibe woweruza pa Inu. Amene ali pansi pa chitetezo Chanu, sanganyozedwe, ndipo amene Mwawachita kukhala mdani Wanu, sadzapatsidwa ulemu. Mbuye wathu. Ndinu wodzadza ndi madalitso ndi Wammwambamwamba. Kuyamikidwa konse ndi kwa Inu nokha chifukwa cha ziganizo zomwe mumapanga. Ndikukupemphani chikhululuko ndipo ndikulapa kwa Inu, ndipo madalitso a Allah atsitsidwe kwa Mtumiki Muhammad swallallahu alaih wasallam ndi banja lake lodalitsika.