Allah akunena m’bukhu lake lolemekezeka la Qur’an kuti,
وَالسَّابِقُونَ الْأَوَّلُونَ مِنَ الْمُهَاجِرِين وَالْأَنصَارِ وَالَّذِينَ اتَّبَعُوهُم بِإِحْسَانٍ رَّضِيَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ وَأَعَدَّ لَهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي تَحْتَهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ ﴿١٠٠﴾.
Ndipo amene adatsogolera poyamba, ochokera m’gulu la ma Muhajirina ndi Answari, ndi omwe adawatsatira Iwo mwaubwino, Allah adzakondwa Nawo. Naonso adzakondwera Naye (pa Zomwe adzapatsidwe ndi Allah.) Ndipo wawakonzera minda yomwe mitsinje lkuyenda pansipake; adzakhala M’menemo muyaya. Uko ndikupambana Kwakukulu.
Pamene mgwirizano wa ku Hudayibiyah unali kukambilanidwa,olemekezeka Urwa bin Masud (radhiyallahu anhu) yemwe anali mthumwi yama Qurayish (kenako adadzalowa chisilamu) anali ndi mwayi owonesetsa ndikuzindikira chikharidwe cha Maswahabah (radhiyallahu anhum) chomwe amamuwonetsera Mtumiki wa Allah (swallallah alayhi wasallam).
Pamene anabwerera kwa anthu ake anati kwaiwo: “Inu ma Qurayish ndakhala ndikukhala mthumwi kumafumu akulu akulu ambiri. Ndaonapo mabwalo a Mfumu Qayisala, Mfumu chosroes komanso mfumu Negus.Ndikulumbilira mwa Mulungu palibe kulikonse ndinaonapo anthu atazungulira mfumu yawo kapena mtsogoleri wawo mwaulemu wotheratu kwamfumu yawoyo ngati mmene ndawawonera maswahabah a Muhammad (swallallahu alayhi wasallama) .
Pamene Muhammad (swallallah alayhi wasallam) walavula malovu, maswahaba ake amathamangira mopikisana kukatenga malovuwo ndimanja awo asadagwere pansi nazipaka kunkhope kwawo ndi thupi lawo. Pamene wapereka langizo lililonse, onse akumfulumira kukwaniritsa.
Pamene akupanga wudhu, akumapikisana wina ndimnzake kukatenga madontho amadzi ochokera pachiwalo chamtumiki (swallallahu alayhi wasallam) asadagwere pansi.Ngati wina walephera kupeza madziwo akumagwira manja onyowa amnzake amene wakwanitsa kupeza madziwo nazipaka nawo nkhope ndimikono yake.
Pamene akuyankhula pamaso pa Mtumiki Muhammad (swallallahu alayhi wasallama), akumayankhula motsitsa kwambiri mawu awo ndiponso sakumuyang`anitsitsa pankhope pake, zonsezitu chifukwa chomupatsa ulemu kwambiri.Tsitsi lothothoka lammutu kapena lamundevu zake akumalisunga maswahaba ake kuti apezepo mdalitso ndipo akumasamala kwambiri mwaulemu.
Mwachidule sindinaonepo gulu la anthu lililonse lomwe limakonda bwana wawo ndiponso lozipereka kwambiri kwa bwana wawoyo ngati mmene ndawawonera maswahaba a Muhammad (swallallahu alayhi wasallam) pomukonda iye ndikuonetsera kuzipereka kwawo kwa Iye.
Tikupempha Allah kuti atidalitse ife ndichikondi chenicheni pa Mtumiki (swallallahu alayhi wasallam) ndi maswahabah ake (radhwiyallahu anhum) ndikutinso atipatse mwayi ndi kuthekera umoyo wathu onse.