Tsiku lina Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa kwa ma Swahaabah (radhwiyallahu “anhum) kuti: “Ndani mwa inu amene akusala kudya lero?” Hazrat Abu Bakr (radhiyallahu anhu) adayankha: “Lero ndasala.
Kenako Nabiy (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa. “Ndani mwa inu amene wayendera munthu wodwala lero?”
Harrat Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) adayankha: “Lero ndayendera munthu wodwala.” Nabiy (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsanso kuti: “Ndani mwa inu amene watenga nawo gawo pa maliro lero?” Hazrat Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) adayankha: “Lero ndinatengako gawo pa maliro .”
Kenako Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa: “Ndani mwa inu lero wadyetsa wosauka?”
Hazrat Abu Bakr (radhayallahu ‘anhu) anayankha: “Lero ndadyetsa munthu wosauka.” Pambuyo pake, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Amene ali ndi makhalidwe onsewa adzakalowa ndithu ku Jannah”