
Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adafotokoza nkhani iyi:
Rasulullah (swallallahu ‘alayhi wasallam) ankakonda kulankhula ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) akamaliza kuswali Esha ndikukambirana naye zokhuza Asilamu. Usiku wina, atamilza swalah ya Esha, Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) adayamba kuyankhula ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) (zokhudza Asilamu) ndipo inenso ndidali nawo pomwepo. Pambuyo pokambirana, Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) adayimirira ndikutuluka mnyumba mwa Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) ndipo nafenso tinatsagana naye.
Tikuyenda, tinadutsa pafupi ndi mzikiti, ndipo tidamva mawu a munthu akuwerenga Quraan pa swalaah mu Musjid. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adayima kuti amvetsere kuwerenga kwa Swahaabiyo. Ife sitidathe kuzindikira kuti amene akuwerengayo ndi ndani kufikira Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adati kwa ife.
من سره أن يقرأ القرآن رطبا كما أنزل فيقرأه على قراءة ابن أم عبد
“Amene akufuna kuwerenga Qur’an mmene idavumbulutsidwira (kuchokera kwa Allah), aziwerenga (Quraan) ngati momwe Abdullah bin Mas’uud akuiwerengera.
Pambuyo pake Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu) adakhala pansi kuti amalizitse Swalah yake ndipo kenako adachita dua. Atayamba dua yakeyo, choyamba anatamanda Allah Ta’ala, kenako anawerenga duruud kumupemhera zabwino Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), kenako anayamba kupempha kwa Allah Ta’ala zosowa zake. Atamva momwe adachitira duayo ( poyamba ndi kuyamika Allah Ta’ala kenako n’kuwerenga durood asanapemphe zosowa zake), Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anati kawiri, “Pempha! Chilichonse chomwe ukufuna upatsidwa.”
Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) sanamve zomwe Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adanena zokhudza kuwerenga kwake Quraan ndi kuti dua yake iyankhidwa ndi Allah Ta’ala.
Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adati mumtima mwake, “Ndipita kukakumana naye m’mawa ndikumuuza nkhani yabwino ya zomwe Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) adanena zokhudza iye.
M’mawa otsatira Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anapita kwa iye kukamuuza nkhani yabwino, koma atafika kunyumba kwakeko, adapeza kuti Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) anali atatuluka kale m’nyumba ya Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu). Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’nyumba ya Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) ndikumuuza za uthenga wabwino, ndipo Abdullah bin Mas’uud adamuuza kuti, “Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) wangondiuza kumene za izi pompanoso (usanabwere).”
Kenako Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adati, “Allah awonetse chifundo chapadera pa Abu Bakr! Nthawi iliyonse ndikayesa kupikisana naye pochita zabwino, nthawi zonse amandiposa!”
Zinanenedwa m’nkhani zina kuti Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adafunsanso Abdullah bin Mas’ood (radhwiyallahu ‘anhu) kuti dua yomwe adachita usiku inali Duwa yanji.
Abdullah bin Mas’uud adamuuza kuti, “Dua yomwe adachita usiku inali,
اللهم إني أسألك إيمانا لا يرتد، ونعيما لا ينفد، ومرافقة محمد في أعلى جنة الخلد
O Allah, ndikukupemphani kuti mundidalitse ndi imaan yomwe pambuyo pake sipadzakhala kubwerera m’mbuyo, ndipo mundidalitse ndi zabwino zomwe sizidzatha, komanso mundidalitse ndi ubwenzi wa Nabi Muhammad (sallallahu ‘alaihi wasallam) m’magawo apamwamba a Jannah (m’tsogolo), chonchi. jannah imene moyo wake udzakhala opitirira ndi kwamuyaya.
Abdullah bin Masuud (Radhwiyallahu anhu) adatchulakonso dua iyi yomwe ankachita akamaswali usiku:
اللهم لا إله إلا أنت، وعدك حق، ولقاوك حق، وكتابك حق، والنَّبيُّون حق، ومحمد صلى الله عليه وسلم – حق والجنة حق والنار حق، ورسلك حق
O Allah! Palibe mulungu wina kupatula Inu, lonjezo Lanu ndi loona, kukumana Kwathu (m’tsogolo) ndi koona, Buku Lanu (Quraan Majeed) ndi loona, Ambiyaa onse ndi oona, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) ndi owona, Jannah ndi yoona, Jahannum ndi yoona ndipo Atumiki Anu onse ndi oona (timakhulupirira kuti zonse ndi zenizeni). (Musnad Abi Ya’la #194, Musnad Ahmad #4338, Sunan Tirmizi #593, Majmauz Zawaaid #15551 & 15557)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu