
Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akunena kuti:
Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu) pamene adali bwanamkubwa wa Shaam, Asilamu adachita Jihaad ndipo adapambana, motero adapeza chuma cholanda kwa adani.
Mkatikati mwa katundu ameneyo mudalinso mtsikana okongola yemwe adaperekedwa kwa msilikali wina wachisilamu ngati gawo lake. Msilikaliyu atangolandira gawo lakeli (mtsikananayu), Yazid bin Abi Sufyaan (radhwiyallahu ‘anhu), mkulu wa gulu lankhondo, adatenga mtsikanayo molanda.
Panthawiyo, Abu Zar Ghifaari (radhwiyallahu ‘anhu) anali ku Shaam ndipo msilikali uyu adapita kwa iye kukapempha thandizo kuti abwezeredwe mtsikanayo kuchokera kwa Yazid bin Abi Sufyaan (radhwiyallahu ‘anhu).
Choncho, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu), atatenga msilikaliyo, ndikupita naye limodzi kwa Yazid bin Abi Sufyaan (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adamulangiza iye katatu kuti abweze mtsikanayo kwa msilikaliyo.
Pambuyo pake Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) adamuuza kuti, “Tamvetsera! Ndikumbira mwa Allah! Ngati utenga mtsikanayu mopondereza dziwa kuti ndidamva Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) akunena kuti, ‘Munthu oyamba kusintha Sunnah yanga adzakhala munthu ochokera ku fuko la Banu Umayyah.” (ndipo m’nkhani zina, zimatchulidwanso kuti Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) adati, “Munthu ochokera mu Banu Umayyah amene adzasintha Sunnah yanga, dzina lake lidzakhala Yazeed.” Musnad Abi Ya’la #871).
Atalankhula izi, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anatembenuka nayamba kuyenda kubwelera kwawo.
Yazid bin Abi Sufyaan (radhwiyallahu ‘anhu) nthawi yomweyo anabweza mdzakadziyo kwa msilikaliyo ndipo adamulondora m’mbuyo Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) ndikumufunsa kuti, “Ndikukupempha m’dzina la Allah! Chonde ndiuze, ukuganiza kuti ndine munthu amene Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) anatchula mu hadith iyi?” Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Ayi, si iwe munthu ameneyo.”
Pambuyo pofotokoza zomwe zili pamwambazi, Imaam Bayhaqi (rahimahullah) adati, “Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu), Sahaabi wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), adali mtsogoleri wa magulu ankhondo aku Shaam m’nthawi ya Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ndi Umar Radhwiyallahu ‘anhu) pamene Rasulullah swallallahu alaihi wasallam ankanena za Yazeed ochojera mu Banu Umayyah kusintha Sunnah yake yodalitsika, Yazid bin sanatanthauze Abi Sufyaan (Radhiyallahu ‘anhu) (popeza kuti adali Sahaabi wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ndipo ankakhala moyo olungama wotsatira Sunnah).
Komabe, Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akufotokozanso kuti panali munthu wina ochokera ku Banu Umayyah yemwe anali ndi dzina lomweli. Iye anali Yazid bin Mu’aawiyah, mwana wa Mu’aawiyah (Radhwiyallahu ‘anhu), ndipo zikuoneka kuti iye ndi amene akutchulidwa mu Hadith ya Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) (popeza iye ndi amene ankabweretsa mavuto aakulu mchisilamu mu ulamuliro wa Banu Umayyah). (Dolaa’il-un-Nubuwwah 6/410)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu