
Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) anali mnyamata wamng’ono, akuweta mbuzi za Uqbah bin Abi Mu’ait m’chigawo cha Makkah Mukarramah. Tsiku lina ali kuweta mbuzi, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adadutsa pamene ankathawa ma mushrikiin.
Popeza chinali chizolowezi cha Aarabu kupereka mkaka kwa odutsa mnjira, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ataziona mbuzizo, adamupempha kuti awapatseko mkaka.
Iwo adamufunsa kuti, “Iwe m’myamata! Kodi uli ndi mkaka oti ungatipatseko?” Iye anayankha kuti, “Eya, ulipo, komabe mbuzi izi ndi zomwe ndimangosungitsidwa, ndipo sindingathe kukupatsani mkaka wake.”
Kenako Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) anamuuza kuti, “Ndibweretsere mbuzi yaikazi yomwe siinayambe kutulutsa mkaka (ilibe mkaka).” Ndinabweretsa mbuzi yaikazi yaing’ono kwa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam).
Olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) anagwira mbuziyo pamaso pa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam). Kenako Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anayamba kusisita manja ake odalitsika pa bere la mbuziyi uku akuwerenga gawo la Qur’aan Majiid ndikupempha kwa Allah Ta’ala kuti apereke mkaka. Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) atachita zimenezi, bere linayamba kudzadza mkaka mozizwitsa.
Olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adabweretsa mwala okhala ndi bowo kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), kenako adakama mkakawo, adagwiritsa ntchito mwalawo ngati chiwiya. Atamaliza kukamako, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ndi Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) onse adamwa mkakawo.
Pambuyo pake, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adalamula bere la nyamayo kuti libwerere m’mene lidaliri poyamba kukhala losatulutsa mkaka, ndipo nthawi yomweyo lidabwerera mwakale.
Ataona chozizwitsachi pamaso pake, mtima wa Abdullah bin Mas’uud unadzazidwa ndi chikondi cha Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam). Patatha masiku angapo, adabwera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) ndipo adalowa Chisilamu.
Nthawi yolowa Chisilamu, anamuuza Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), “Ndiphunzitseni mawu omwe mudawerenga nthawi yomwe munkakama mkaka ku nyama yomwe inalibe mkaka m’mabere mwake.” Kenako Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaika dzanja lake lodalitsika pamutu pake nati:
يرحمك الله فإنك غليم معلم
“Allah Ta’ala akuchitire chifundo. Ndiwe mnyamata amene udzakhale ndi tsogolo labwino pankhani ya maphunziro.” (Musnad Ahmad #3598)
Mu nkhani ina, zanenedwanso kuti Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adapempha Allah Ta’ala kuti amupatse barakah yapadera. (Saheeh Ibnu Hibbaan #6504, Munsnad Ahmed #4412, 3598 and Musnad Abu Ya’laa #5096)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu