Dongosolo la Allah Ta‘ala, kukamba momwe amalengedwera anthu, ndilakuti anthu awiri akakumana munthu amapangidwa. Chinthu choyamba ndi kudzera mwa makolo omwe mbewu ya mwamuna imabzalidwa m’mimba mwa mayi. Chinthu chachiwiri ndi mzimu omwe umalowa m’mimba mwa mwana yemwe sanabadweyo akakwanitsa miyezi inayi.
Munthu aliyense amene anabwera padziko lapansi adatsatira njira imeneyi. Komabe, Allah Ta‘ala adapanga kapezekedwe ka anthu atatu kukhala kosiyana ndi ndondomekoyi ngati Nabi Aadam, Hawwaa, ndi Nabi Isa (‘alaihimus salaam).
Kukamba za Nabi Aadam (‘alaihis salaam), Allah Ta‘ala adalenga thupi lake kuchokera ku dothi kenako n’kumuuzira. Ichi ndi chifukwa chake iye anabadwa popanda makolo.
Kukamba za Hawwaa (‘alaihas salaam), Allah Ta’ala adamulenga kuchokera ku nthiti yakumanzere ya Nabi Aadam (‘alaihis salaam). Choncho, anabadwa kudzera mwa munthu m’modzi yekha.
Kunena za Nabi Isa (‘alaihis salaam), Allah Ta‘ala adamulenga popangitsa mzimu kulowa m’mimba mwa amayi ake. Choncho, anabadwa kudzera mwa munthu m’modzi yekha.
Mu Qur’aan Yolemekezeka, Nabi Isa (‘alaihis salaam) adayerekezedwa ndi Aadam (‘alaihis salaam). Allah Ta’ala akuti:
Ndithudi, chitsanzo cha Nabi Isa (‘alaihis salaam) kwa Allah chikufanana ndi cha Nabi Aadam (‘alaihis salaam). Allah Ta‘ala adamulenga (Nabi Aadam [‘alaihis salaam]) kuchokera ku dothi, kenako nati kwa iye (chidaumbidwa kuchokera ku dothicho), “Khala!” ndipo anakhala.” (Surah Aal-e-Imraan v. 59)
Mu ayah iyi, Allah Ta‘ala akufotokoza kuti kulengedwa kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam) kunali kofanana ndi kulengedwa kwa Nabi Aadam (‘alaihis salaam) poyang’ana kuti Nabi Aadam (‘alaihis salaam) sanabadwe kudzera mwa makolo, koma analengedwa ndi mzimu omwe unalowetsedwa mwa iye.
chimodzimodzinso, Nabi Isa (‘alaihis salaam) sanabadwe kudzera mwa bambo, koma ruuh kulowetsedwa m’mimba mwa amayi ake, zomwe zinamupangitsa kukhala munthu.
Ndi chifukwa chake tikupeza kuti monga momwe Nabi Aadam (‘alaihis salaam) adalengedwera ndi Hawwaa (‘alaihas salaam) ndi mozizwitsa, momwemonso kulengedwa kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam) kunali kodabwitsa komanso kopatulika.
Zozizwitsa Za Nabi Isa (‘alaihis salaam)
Allah Ta‘ala adamudalitsa Nabi Isa (‘alaihis salaam) ndi mphamvu yochita zodabwitsa zambiri. Chozizwitsa chilichonse chomwe adachita chinachitika ndi chilolezo cha Allah Ta‘ala, ndipo kudzera mwa Allah Ta‘ala adamupatsa kuthekera ndi mphamvu zotha kuchichita.
Zina mwa zozizwitsa zomwe adachita, monga momwe zanenedwera mu Qur’aan Majiid, ndichakuti adachiritsa akhate ndi omwe anabadwa akhungu. Ankaumba mbalame kuchokera ku dothi kenako nkuziuzira mpweya, ndipo Allah Ta‘ala ankazipatsa moyo.
Allah Ta‘ala Amunyamura Nabi Isa (‘alaihis salaam) Kupita Kumwamba
Kukamba za Nabi Isa (‘alaihis salaam), Akristu amakhulupirira kuti adapachikidwa pamtanda ndipo adaphedwa ndi Ayuda. Komabe, chikhulupiriro ichi ndi chabodza ndipo chatsutsidwa momveka bwino mu Qur’aan Majiid.
Chiphunzitso cha Chisilamu ndichakuti Ayuda sanamuphe, koma Allah Ta‘ala anamupulumutsa ku mavuto awo ndipo anamunyamura kupita kumwamba mozizwitsa. Allah Ta‘ala akufotokoza momveka bwino izi mu Qur’aan Majiid. Allah Ta‘ala akuti,
“Ndipo iwo (Ayuda) sanamuphe, kapena kumupachika; koma adapombonezedwa ndi munthu wina. iwo amene akutsutsana za izi ndithudi ali mu chikaiko pa zimenezi, alibe uzindikiri ulionse otsimikizika ndipo amangotsatira maganizo awo, ndithudi zoona zake ndi zakuti iwo sadamuphe, koma kuti Allah adamunyamura kupita kwa iye, Allah ndiye mwini ulemelero mwini kuzindikira mwakuya.
(Surah Nisaa v. 157-158)
Kuchokera pamwambapa, taona kuti moyo wa Nabi Isa (‘alaihis salaam’) ndi chizindikiro chachikulu choonekera bwino cha Qudrat (mphamvu) ya Allah Ta’ala. Kuyambira momwe anabadwira ndi zozizwitsa zomwe adachita mpaka pomwe Allah Ta‘ala adamunyamulira kupita kumwamba – zonse zikuonetsa mphamvu ya Allah Ta‘ala.
Dajjaal akadzabwera padziko lapansi, adzakhala akupanga ma fitnah akuluakulu komanso zoipa zambiri padziko lapansi. Fitnah yake, monga momwe yatchulidwira mu Hadith, idzakhala fitnah yaikulu kwambiri yomwe dziko lapansi lidzakumane nayo kuyambira pamene dzikoli lidalengedwa. Panthawi yofunikira kwambiri ngati imeneyo, adzakhala Nabi ameneyu wa Allah Ta‘ala olemekezeka – Nabi Isa (‘alaihis salaam), yemwe ndi chizindikiro cha Qudrat ya Allah Ta‘ala, yemwe adzatumizidwe ndi Allah kudziko lapansi kuti adzapulumutse Ummah wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pomupha Dajjaal, amenewo adzakhala mathero a zoipa zake zonse.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu