Ulamuliro wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) udzakhala wa chilungamo ndi barakah (madalitso). Popeza Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzasankhidwa ndi Allah Ta‘ala kuti autsogolere ummah isadafike Qiyaamah, adzatsogozedwa ndi Allah ndikuthandizidwa ndi Iye. Popeza, chisankho chilichonse chomwe adzachite chidzadzazidwa ndi zabwino ndi chilungamo. Nthawi ya ulamuliro wake, Allah Ta‘ala adzadalitsa Asilamu ndi ma barakah (madalitso) ambiri ndipo adzabwezeretsa mphamvu ndi ulemelero wa Chisilamu mu ummah.
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzaonekera kumapeto kwa ummah wanga. Allah Ta‘ala adzamupatsa barakah yambiri kudzera mu mvula yochuluka, zomwe zidzapangitse kuti nthaka ibare zipatso zambiri. Adzagawa chuma mwachilungamo pakati pa Asilamu, ziweto zidzachuluka ndikupezeka zambiri ndipo ummah udzapatsidwanso mphamvu ndi ulemu wake. Akadzasankhidwa ndi Allah Ta‘ala, adzakhala ndi moyo zaka zisanu ndi ziwiri kapena zisanu ndi zitatu.” (Mustadrak Haakim #8673)
Kuchuluka kwa Chilungamo ndi Kukhutira mu nthawi ya Ulamuliro wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu)
Mmahadith ena, zalembedwa kuti Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzalamulira mwachilungamo kotero kuti anthu okhala padziko lapansi ndi kumwamba adzakondwera naye, ndipo kulikonse kumene adzapite padziko lapansi, Allah Ta‘ala adzapangitsa kuti zabwino ndi baraka zipambane. Chilungamo chake chidzakhudza anthu onse ndipo adzawachitira zinthu motsatira Sunnah ya Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam).
Chifukwa cha chilungamo chake, akadzauza munthu kuti alengeze kuti, “Aliyense amene ali ndi chosowa abwere kwa ine,” munthu m’modzi yekha ndiye adzabwera (popeza zosowa za anthu ena onse zidzakwaniritsidwa kudzera mu ulamuliro wake olungama).
Olemekezeka Abu Sa’eed Khudri (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti nthawi ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adalankhula ndi ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) nati, “Ndikukupatsani uthenga wabwino wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) kubwera ku ummah uno (Qiyaamah isanafike)! Adzatumizidwa ku ummah uno panthawi yomwe kusemphana pakati pa ummah kudzakula ndipo zivomerezi zidzaonekera padziko lonse lapansi. Adzalamulira monena kuti dziko lapansi lizadzadza ndi chilungamo, monga momwe lidaliri kale, kuponderezana ndi nkhanza sizidzakhalako. Anthu okhala kumwamba ndi anthu okhala padziko lapansi adzakondwera naye. Adzagawa chuma moyenera.”
Kenako Sahaabah wina (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti: “E, Mtumiki wa Allah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) zikutanthauza chani kuti Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) adzagawa chuma moyenera?” Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Zikutanthauza kuti adzagawa chuma mwachilungamo ndi mosakondera pakati pa anthu.”
Kenako Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anapitiriza kunena kuti, “Pa nthawiyo, Allah Ta‘ala adzadzadzitsa mmitima ya anthu a Muhammad (swallallahu ‘alaihi wasallam) ndi chisangalalo ndi chimwemwe. Ulamuliro wa chilungamo wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) udzakuta anthu onse, mpaka anthu adzasangalala ndi madalitso akuluakulu kudzera mwa iye, kotero kuti munthu adzalankhula ndi anthu kuti, ‘Ndi munthu uti pakati panu amene akusowa chuma?’ Mwa anthu onse, munthu m’modzi yekha ndiye adzaimirira nati, ‘Ndikusowa chuma!’
“Munthuyo adzati kwa iye, ‘Pita kwa oyang’anira chuma ndipo ukamuuze kuti, ‘Mahdi wakuuza kuti upatsidwe chuma.’ Akadzafika kwa oyang’anira chuma, oyang’anira chuma adzati kwa iye, ‘Tenga ndi manja ako onse awiri, momwe ukufunira!’ Munthuyo adzatenga chuma ndi manja ake onse, akuchisonkhanitsa pamaso pake.
“Nthawi imeneyo, munthuyo adzadandaula nati, ‘Ndimalakalaka kwambiri chuma kuchokera ku ummah wa Muhammad (sallallahu ‘alaihi wasallam)! Kodi chomwe chinali chokwanira kwa iwo sichikanandikwanira?’ Akadzanena izi, adzabweza chumacho. Komabe, chuma chomwe adzafune kubweza kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) sichidzalandiridwa kwa iye, ndipo adzauzidwa kuti, ‘Chimene tapereka, sitikumatengaso.’
“ Barakah imeneyi idzapitirirabe kukhalapo kwa nthawi yonse ya Mahdi yomwe ndi zaka zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi zitatu kapena zisanu ndi zinayi.” (Majma’uz Zawaa’id #12393)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu