Isa (‘alaihis salaam) ndi Mtumiki wa Allah Ta‘ala ndipo ali m’gulu la Aneneri apamwamba. Allah Ta‘ala adamuvumbulutsira Injeel (Baibulo) ndipo adamudaritsa ndi Shari’ah. Iye ndi Nabi amene anatumizidwa padziko lapansi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) asanabwere.
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ambiyaa onse (‘alaihimus salaam) ali ngati ana a bambo m’modzi. Amayi awo ndi osiyana, ndipo deen yawo ndi imodzi (onse amakhulupirira tauhiid – umodzi wa Allah, ngakhale kuti Shari’ah zawo ndi zosiyana). Ine ndine munthu wapafupi kwambiri ndi Nabi Isa bin Maryam (‘alaihis salaam) chifukwa palibe Nabi wina pakati pathu. Nabi Isa (‘alaihis salaam) adzatsika ndithu.” (Musnad Ahmed #9270)
Allah Ta‘ala anamutumiza Nabi Isa (‘alaihis salaam) kwa Bani Israa’eel, koma iwo sanamukhulupirire ndipo anamukana. Anayesera kumupha, koma Allah Ta‘ala adamuteteza ndikumukweza kumwamba ali wamoyo. Pakadali pano, Nabi Isa (‘alaihis salaam) ali moyo kumwamba, ndipo Qiyaamah ikamadzayandikira, Allah Ta‘ala adzamutsitsa kubwera padziko lapansi.
Mu Hadith yolemekezeka, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ndikulumbira Mwa amene moyo wanga uli m’manja mwake! Nthawi yayandikira kwambiri (Qiyaamah) pamene mwana wa Maryam (Nabi Isa (‘alaihis salaam) adzatsika kuchokera kumwamba, ndipo adzalamulira pakati panu ngati mtsogoleri olungama. Adzaphwanya mtanda ndikupha nkhumba…” (Sahiih Muslim #155)
Kutsika kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam) – Chizindikiro Chachikulu cha Qiyaamah
Kutsika kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam) kuchokera kumwamba kubwera padziko lapansi kumaikidwa mgulu la zizindikiro zikuluzikulu za Qiyaamah.
Mu Qur’aan Yolemekezeka, Allah Ta‘ala akuti, “Ndipo ndithudi iye (Nabi Isa [alaihis salaam]) ndi chimodzi mwa zizindikiro za Qiyaamah, choncho musakhale ndi kukaikira kulikonse pa kutha kwa dziko (kubwera kwa Qiyaamah)… (Surah Zukhruf v. 61)
Mu Hadith ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adanena kuti, “Zoonadi, Qiyaamah sidzachitika kufikira mutaona zizindikiro khumi zikuluzikulu zikuchitika. Utsi (mtundu wa nthunzi kapena utsi omwe udzatsike padziko lapansi kuchokera kumwamba Qiyaamah isanafike,ndi pomwe Asilamu adzagwidwe ndi chimfine ndipo ma kuffaar adzakomoka), kutuluka kwa Dajjaal, kutuluka kwa chilombo, kutuluka kwa dzuwa kuchokera kumadzulo, kutsika kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam), kubwera kwa Ya’juuj ndi Ma’juuj, kumira kwa nthaka kokwana katatu, Kumira kum’mawa, kumira kumadzulo ndi kumira ku Arabian Peninsula. Chizindikiro chomaliza chidzakhala moto omwe udzabuke ku Yemen ndikukusira anthu onse kupita ku bwalo la mahshar (Syria).” (Saheeh Muslim #2901)
Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah ponena za Nabiy Isa (‘alaihis salaam) Kupha Dajjaal.
Chikhulupiliro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa chokhudza Isa ‘alaihis salaam kupha Dajjaal.
Chimodzi mwa zifukwa zimene adzatumizidwire Isa ‘alaihis salaam ku dziko lapansi qiyaama isadafike ndi kudzapha Dajjaal. Isa ‘alaihis salaam kupha Dajjaal ndi zina mwa zikhulupiriro zikuluzikulu za Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah.
Allaamah Qadhi Iyaadh (rahimahullah) wafotokoza kuti Nabiy Isa (‘alaihis salaam) kubwereranso padziko lapansi kudzapha Dajjaal ndi zina mwa zikhulupiriro zikuluzikulu za Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah. Ma Muhadditheen, Fuqahaa ndi Ulamaa a Aqaa’id onse amavomereza chikhulupiriro ichi.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu