Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu)

Kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi chizindikiro choyamba mwa zizindikiro zikuluzikulu zomwe zidzawonekere Qiyaamah isadafike. M’mahadith odalitsika ambiri, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adalosera za kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ku ummah uno.

Allaamah Suyuuti (rahimahullah) wafotokoza kuti mahadith okhudzana ndi kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi ochuluka kwambiri kotero kuti adafika pa mlingo wa Tawaatur (chiwerengero chachikulu cha ofotokozera mahadith motsatizana, nthawi iliyonse). Choncho, ma Ulama ali ogwirizana kuti kukhulupirira kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi chimodzi mwa zikhulupiriro zikuluzikulu za Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah.

Qiyaamah isadafike, Asilamu adzaponderezedwa ndi kuzunzidwa ndi makafiri m’madera ambiri padziko lapansi. Nthawi imeneyo Allah Ta’ala adzatumiza Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ku gulu la anthu kuti akawapulumutse ndikubwezeretsa Dini padziko lapansi. Zanenedwa kuti Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzabwera Dajjaal asanaonekere padziko lapansi.

Kutsimikizika kwa Kubwera kwa Mahdi

Kunena za kutsimikizika kwa kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu), Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Zitakhala kuti kwatsala tsiku limodzi lokha kuti dziko lithe, Allah Ta’ala atha kulitalikitsa kufikira atatumiza munthu ochokera ku Ntundu wanga dzina lake lofanana ndi dzina langa, ndipo dzina la bambo ake lofanana ndi dzina la bambo anga.” (Sunan Abu Dawood #4282 & 4284)

Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) kuchokela mwa ana a Olemekezeka Faatimah (radhwiyallahu ‘anha)

Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) adzachokera mu m’bado wa Hasan (radhwiyallahu ‘anhu), mwana wa Faatimah (radhwiyallahu ‘anha). Dzina lake lidzakhala Muhammad ndipo dzina la bambo ake lidzakhala Abdullah.

Zanenedwa kuti tsiku lina, Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adamuyang’ana mwana wake Hasan (radhwiyallahu ‘anhu), nati, “Ndithudi mwana wanga uyu ndi mtsogoleri, malingana ndi momwe Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adanenera kuti Munthu adzachokera ku banja lake amene adzakhale ndi dzina lomwelo la Mtumiki wanu. Adzafanana ndi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) koma sadzafanana naye m’mawonekedwe ake.” (Sunan Abu Dawood #4290)

Kufotokoza Maonekedwe a Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu)

Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzakhala ndi chipumi chachitali ndipo padzakhala mpata pakati pa mano ake awiri akutsogolo. Mphuno yake idzakhala yaitali, komanso yoongoka. Adzakhala ndi kagawo kokongola pa tsaya lake lamanja. Adzakhala ndi khungu lachi Arabu. (Manaarul Muniif #335, Zakhiiratul Huffaaz #4645, Sunan Abu Dawood #4287 ndi Aqdud Durar tsamba 100-102)

Adzaonekera pakadzakhala kusemphana pakati pa ummah ndipo zivomerezi zidzachuluka. Adzakhala ndi zaka makumi anayi (40) akamadzaonekera. Pa kuonekera kwake mu ummah ngati Mahdi, adzakhala atavala nduwira. (Majma’uz Zawaa’id #12393, Fitan li-Nu’aim bin Hammaad #1067 ndi Zakheeratul Huffaaz #6506)

Allah Ta‘ala kumukonza Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi Kuika Mphamvu ya Utsogoleri mwa iye

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzachokera mwa ife, Ahl-e-Bayt. Allah Ta‘ala adzamukonzekeretsa mu usiku umodzi (Allah Ta‘ala adzaika mphamvu ya utsogoleri mkati mwake mu usiku umodzi).”  (Musnad Ahmed #645)

Pali mahadith ambiri omwe anenedwa okhudza chilungamo chomwe Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzalamulire nacho, ndi madalitso ochuluka omwe adzakhalepo mu ummah mu ulamuliro wake. Insha Allah, ena mwa mahadith amenewa afotokozedwa m’magawo otsatirawa.

Check Also

Maonekedwe a chithupithupi cha Dajjaal

M’mahadithi olemekezeka, Olekezeka Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adatsimikizira ummah za Maonekedwe a Dajjaal a umunthu. …