Sheikh Abdul Qaadir Jeelani (rahimahullah) anali Aalim ndi Wali wa Allah Ta‘ala yemwe anakhalapo m’zaka za mma 600 A.H. Allah Ta‘ala adamudalitsa ndi kulandiridwa kwakukulu kotero kuti anthu ambiri adasintha miyoyo yawo ndi iye. Khalidwe limodzi lodziwika bwino lomwe lidawonekera m’moyo wake linali chilungamo (kuyankhula chilungamo). Pansipa pali nkhani yomwe ikuwonetsa khalidwe lokongola limeneli m’moyo wake lomwe linakopa mitima ya ochimwa akuluakulu a nthawi imeneyo:
Sheikh Abdul Qaadir Jeelaani (rahimahullah) ataganiza zoyenda kukasaka maphunziro, adapempha chilorezo kwa amayi ake kuti apite ku Baghdad komwe akaphunzire pansi pa ma Ulama otsogola a nthawiyo. Amayi ake adamulora kuti apite ndipo adamupatsa ma dinar makumi anayi omwe adasokelera mu kurta yake (nkanjo) kukhwapa kwake. Posiyana naye adamulangiza kuti awonetsetse kuti nthawi zonse azilankhula zoona ndipo osalankhula bodza. Sheikh Abdul Qaadir Jeelani (rahimahullah) anatsatira malangizo a amayi ake ndipo anawalonjeza kuti nthawi zonse adzakhala oyankhula zoona.
Kenako Sheikh Abdul Qaadir (rahimahullah) anatengana ndi gulu la anthu omwe ankapita ku Baghdad. Paulendowo, gululi lidakumana ndi achifwamba makumi asanu ndi limodzi (60) omwe anaba katundu yense wa anthuwa, Abdul Qaadir Jeelani (rahimahullah) akunena kuti, “Akubawa atatenga katundu yense wa anthu mmodzi mwa achifwamba anabwera kwa ine, ndipo poganiza kuti ndilibe ndalama, anandifunsa kuti, ‘Iwe osauka! Uli ndi ndalama zingati ‘ Ndinakumbukira uphungu wa amayi anga ndipo ndinayankha kuti, ‘ndiri ndi Madinari makumi anayi.’ Kenako anandifunsa kuti, ‘Ndalama zili kuti?’ Ndinayankha kuti, ‘Zasokedwa mu kurta yanga ku m’khwapa kwanga.’ Wakubayo sanakhulupirire ndipo anaganiza kuti ndikuseka ndipo anandisiya.
“Patapita mphindi zochepa, wakuba wina anabweranso nandifunsa funso lomwelo, lomwe ndinayankhanso chimodzimodzi. Wakuba uyu nayenso ankaganiza kuti ndikuseka ndipo anandisiya. Pambuyo pake, achifwamba onse awiri anapita kwa mtsogoleri wawo namuuza zomwe zinachitika ndipo anamuuza kuti atandifunsa, ndinawauza kuti ndiri ndi ma dinar makumi anayi, omwe ali mu kurta yanga. Mtsogoleriyo anawauza kuti, ‘Mubweretseni kuno.’
“Atandibweretsa kwa mtsogoleri wawo, anandifunsa kuti, ‘Iwe mnyamata! Uli ndi ndalama zochuluka bwanji?’ Ine ndinayankha kuti, ‘Ndiri ndi ma dinari makumi anayi.’ Kenako anandifunsa kuti, ‘Ziri kuti?’ Ine ndinayankha kuti, ‘Zasokedwa mu kurta yanga mumkono wanga.’ Anadabwa kwambiri ndipo anandifunsa kuti, ‘N’chiyani chinakupangitsa kulankhula zoona ndikuvomereza kuti uli ndi ndalamazi? (Mwanjira ina, ukanakhala kuti siunatiuze, sitikanadziwa.)’ Ine ndinayankha kuti, ‘Amayi anga anandilangiza kuti nthawi zonse ndikhale oayankhula chilungamo, ndipo ndinawalonjeza kuti nthawi zonse ndidzalankhula zoona ndipo sindidzanama. Ndi chifukwa chake, sindinafune kuswa lonjezo limene ndinapanga kwa amayi anga ponena zabodza mutandifunsa zandalamazo.’
“Atamva yankho ili, mtsogoleriyo anakhudzidwa kwambiri ndipo anayamba kulira. Iye anafuula kuti, ‘Ukukana kuswa lonjezo limene unalonjeza amayi ako, pomwe ine ndakhala ndikuswa lonjezo langa kwa Allah Ta‘ala kwa zaka zambiri potchingira anthu m’njira ndi kuchita machimo!’”
Sheikh Abdul Qaadir Jeelani (rahimahullah) akufotokoza kuti, “Kenako mtsogoleriyo analapa pamaso panga ndipo analumbira kuti sadzabwerera ku tchimo la kuba ndi kuba. Achifwamba ena ataona kulapa kwake, anauza mtsogoleri wawo kuti, ‘Tinakupangani kukhala mtsogoleri wathu pochita umbanda ndi kuba ndipo tinakutsatirani. Tsopano tikukupangani kukhala mtsogoleri wathu mu kulapa ndi kupanga taubah ndipo tidzakutsatiraninso mu izi.’ Kotero analapa ndikubweza chuma chonse chomwe anawabera anthu aja.”
Kudzera mnjira imeneyi, kukhanzikika pa chilungamo, Sheikh Abdul Qaadir (rahimahullah) anakhala njira ya achifwamba onse makumi asanu ndi limodzi kuti alape ndikusintha miyoyo yawo. (Bahjatul Asraar tsamba 186 ndi Qalaa-idul Jawaahir tsamba 9)
Mu Hadith yolemekezeka, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) watsindika kwambiri kufunikira koyankhula choonadi. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Gwiritsitsani mwamphamvu chilungamo, chifukwa choonadi chimamutsogolera munthu ku Taqwa, ndipo Taqwa imamutsogolera munthu ku Jannah. Munthu adzapitiriza kulankhula zoona ndikuyesetsa kukhalabe pa choonadi (nthawi zonse), mpaka atalembedwa kuti ndi munthu okhulupirika kwambiri ndi Allah Ta‘ala. Pewani bodza, popeza bodza limatsogolera munthu ku uchimo, ndipo tchimo limatsogolera munthu ku moto wa Jahannum. Munthu amapitiriza kunena bodza, ndipo amayesetsa kukhalabe ndi chizolowezi choyankhula bodza (nthawi zonse), mpaka Allah Ta‘ala atamulemba kuti ndi wabodza wamkulu.” (Saheeh Muslim #2607)
Tikuyenera kukumbukira kuti chilungamo ndi kukhulupilika sizili pa kulankhula kokha. M’malo mwake, zimagwira ntchito pa chilichonse cha deeni ya munthu ndi moyo wake wa padziko lapansi. Munthu akakhala wachilungamo, ndiye kuti adzakwaniritsa udindo uliwonse, kaya ukugwirizana ndi deeni yake kapena moyo wake wa padziko lapansi. Ndipotu, chilungamo zimapitirira malire a kungokwaniritsa malamulo ndipo zimaphatikizapo kuyesetsa kusonyeza chikondi ndi chifundo chapamwamba ku zolengedwa, motengera momwe Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaphunzitsira ummah.
Mwachidule, kapolo weniweni wa Allah Ta‘ala ndi munthu amene amakhala okhulupirika kwa Allah Ta‘ala nthawi zonse. Nthawi zonse amakhala ndi nkhawa yokhudza kukondweretsa Allah Ta‘ala ndikusamalira zolengedwa Zake momwe angathere, motero amasonyeza kukhulupirika kwake kwa Mlengi Wake. Kapolo amene amabweretsa makhalidwe amenewa m’moyo wake amalemekezedwa ndi kudalitsidwa ndi udindo wa siddeeq. Siddeeqeen wamkulu anali Olemekezeka Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu ‘anhu), amene Allah Ta‘ala adamusankha kukhala chitsanzo chabwino kwambiri chomwe anthu ayenera kutsatira pambuyo pa Ambiyaa (‘alaihimus salaam). Mawu ake onse ndi zochita zake zinkasonyeza khalidwe labwino kwambiri limeneli.
Polera mwana, ndikofunikira kwambiri kuti makolo aphunzitse mwana khalidwe lokhala wachilangamo nthawi zonse komanso kukhulupilika pa zochita zake. Khalidweli likakhanzikika mumtima mwa mwana, ndiye kuti m’moyo wake onse, mosasamala za nyengo zomwe angakumane nazo, adzaonetsetsa kuti akukwaniritsa ufulu wa Allah Ta‘ala komanso ufulu umene ali nawo ku chilengedwe. Komanso, khalidweli likakula m’moyo wake, nthawi iliyonse, adzakhala ndi chidwi chokhala ndi moyo oyera, mkati ndi kunja, ndipo adzakhala ndi nkhawa yokhudza kuima pamaso pa Allah Ta‘ala ndi kuyankha mlandu pa zochita zake pa Tsiku la Qiyaamah. Popeza, mawu alionse omwe adzanene ndi zochita zonse zomwe adzachite zidzakhala zogwirizana kwathunthu ndi kutsata miyezo yapamwamba ya sidq (chilungamo). Chifukwa choti, kulikonse komwe akupita, adzakhala nyali ya kuwala ndi gwero la chifundo ku zolengedwa zonse.
Ubwino ndi Kufunikira kwa Chilungamo ndi Kukhulupirika
Mu Hadith ya Rasulullah swallallahu alaihi wasallam yalimbiiitsa kwambiri kufunika ndi ubwino wa Chilungamo ndi kukhulupirika. Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anati, “Gwiritsitsani choonadi, chifukwa choonadi chimatsogolera munthu ku chiongoko, ndipo chiongoko chimamutsogolera munthu ku Jannah.
“Munthu adzapitiriza kuyankhula zoona ndikuyesetsa kukhalabe pa choonadi (nthawi zonse), mpaka atalembedwa kuti ndi munthu okhulupirika kwambiri kwa Allah.
“Pewani bodza, popeza bodza limamutsogolera munthu ku uchimo, ndipo uchimo umamutsogolera munthu ku moto wa Jahannum. Munthu adzapitiriza kuyankhula bodza, ndi kupitiliza kukhalabe ndi chizolowezi choyankhula bodza (nthawi zonse), mpaka atalembedwa pamaso pa Allah kuti ndi munthu wabodza kwambiri
Tiyenera kukumbukira kuti chilungamo komanso kukhulupilika sizikutanthauza kulankhula kokha. M’malo mwake, zimagwira ntchito pa gawo lililonse la munthu Dini ndi moyo wa dziko lapansi. Munthu akakhala wachilungamo, ndiye kuti adzakwaniritsa udindo uliwonse, kaya ukugwirizana ndi Dini yake kapena moyo wa dziko lapansi.
Ndipotu, chilungamo chimapitirira malire a kungokwaniritsa malamulo kokha ndipo zimaphatikizapo kuyesetsa kusonyeza chikondi ndi chifundo kuzolengedwa mmene Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adauphunzitsira ummah kuchita.
Kukhala Okhulupirika Pa Maso Pa Allah Nthawi Zonse
Kunena zoona, kapolo weniweni wa Allah Allah ndi yemwe ali okhulupirika nthawi zonse. Nthawi zonse amakhala odera nkhawa za momwe angamukondweretsere Allah ndi kulemekeza zolengedwa Zake momwe angathere kudzera mukuonetsa kukhulupirika kwake Pamaso pa Allah.
Kapolo yemwe angabweretse makhalidwe amenewa pa moyo wake adzalemekezedwa ndi kupeza mdalitso oikidwa mgulu la ma Siddiiqiin. Mkulu wama sidiiqiin anali olemekezeka Abu Bakr Siddiiq radhwiyallahu anhu amene Allah adamupanga kukhala chitsanzo chabwino kwambiri kuti Ummah utsatire pambuyo pa Ambiyaa alaihimus salaam. Liwu lirilonse lake ndi zochita zake zidaonekera kidzera mu khalidwe limeneri kufika patali.
M’katikati molera mwana, n’kofunika kwambiri kuti makolo aziphunzitsa mwana kukhala okhulupirika nthawi zonse ndi kuchita zinthu mokhulupirika. Khalidwe limeneli likakhanzikika kwambiri mumtima mwa mwanayo, ndiye kuti m’nthawi yonse ya moyo wake, mosaona nyengo yomwe iye angakumane nayo, adzapitirizabe kulemekeza malamulo a Allah ngakhalenso ufulu wa anthu ena.
Kuonjezera apo, khalidweri likadzakulilira m’moyo mwake, ndiye kuti nthawi iliyonse, adzakhala oyesetsa kukhala umoyo oyera, mkati ndi kunja kwake, ndipo adzakhala okhudzidwa pa zakuima pamaso pa Allah Ta’aala ndi kuyankha mlandu pa ntchito zake pa tsiku la Qiyaamah.
Choncho, liwu lirilonse limene adzalankhule ndi zochita zonse zimene adzachite zidzakhala zogwirizana kwathunthu ndi mbiri imeneyi yokhala siddiiq (okhulupirika). Kotero, kulikonse kumene angapite, iye adzakhala nyali ya kuunika ndi magwero a chifundo kwa zolengedwa zonse.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu