Fuko lodalitsidwa ndi maphunziroo a Dini ndi kumvetsetsa komveka bwino komanso ndi fuko lopita chitsogolo komanso lachitukuko lomwe lili ndi tsogolo labwino.
Mbali inayi, mtundu opanda maphunziro a Dini ndi kuzindikira koyenera ndi mtundu omwe ukupita kuchiwonongeko ndi kulephera.
Ndichifukwa chake Nabi aliyense akatumizidwa ku fuko linalake, ndiye kuti imodzi mwa ntchito zoyambilira za Nabii inkakhala kukhanzikitsa mwa mphamvu maphunziro a Dini ndi uzindikiri, ndi kulowetsa m’mitima mwawo makhalidwe apamwamba.
Choncho, nkhawa za Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) nthawi zonse zinkalunjika pakuwaphunzitsa ma Swahaabah radhwiyallah anhum makhalidwe abwino ndikuwasonyeza momwe angayendere moyenera m’magawo osiyanasiyana a moyo.
Kufunika kopereka maphunziro a Dini kwa mwana kungamvetsetseke bwino kuti nthawi iliyonse munthu aliyense akalowa Chisilamu, ndiye kuti chimodzi mwazinthu zofunika kwambiri kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam chinali kumuphunzitsa za Dini. Choncho, asadasamukire ku Madinah Munawwarah, gulu loyamba la ma Answaar litalowa Chisilamu, Mtumiki swallalah alaihj wasallam adatumiza Mus’ab bin Umair radhwiyallah anhu ku Madina Munawwarah kuti akawaphunzitse chipembedzo.”
Kufunika kwa Maktab Madrasah
Umar radhwiyallahu anhu adamvetsetsanso kufunikira kwakukulu kopereka maphunziro a dini kwa ana. Choncho, kupatula kukhudzika komwe Umar radhwiyallahu anhu anaonetsa pophunzitsa Ummah Dini, iye adali ndi chidwi chenicheni pa maphunziro a dini a ana ang’ono ang’ono.
Choncho, zikunenedwa kuti Umar radhwiyallahu anhu ndi munthu oyamba amene adayambitsa dongosolo la madrasah a Maktab . Adasankha aphunzitsi oti aziphunzitsa anawo ndipo adawaikira malipilo kuchokera ku Baytul Maal.
Kukhudzika kwa Ma Swahaabah Kuti Ana Awo Azipezeka mgulu la anthu Oopa Allah.
Chimodzimodzinso, ma Swahaabah ambiri radhwiyallahu anhum ochokera mwa ma Muhaajiriin ndi Answaar adali okhudzika ndi ubwino wa dini ya ana awo ndi kulandira kwawo maphunziro olondola a dini ndi kuzindikira kwawo.
Choncho, ankawalimbikitsa ana awo kuti achite lonjezano ndi Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam ndi kupindula naye. Kotero adzapeza maphunziro ndi kumvetsetsa kwa dini kuchokera kwa iye.
Mwa ma swahaabah achinyamata amene adalonjeza anali olemekezeka Abdullah bin Zubair radhwiyallahu anhu Abdullah bin Ja’far radhwiyallahu anhu ndi Umar bin Abi Salamah radhwiyallahu anhu. Pa nthawi yolonjeza, Abdullah bin Zubair radhwiyallahu anhu adali ndi zaka pafupifupi 7 kapena 8.
Kumupatsa mwana maphunziro a dini ndikofunikira kwambiri kotero kuti Hadith ikufotokoza kuti pa tsiku la Qiyaamah munthu adzapatsidwa chilango chifukwa chonyalanyaza kumuphunzitsa mwana wake maphunziro a dini.
Kufotokozera Mwana Molingana ndi Kumvetsetsa Kwake
Mbali yachiwiri ndiyo kutsegula mtima ndi maganizo a mwana wamng’onoyo kudzera mu kumufotokozera phunziro mogwirizana ndi kumvetsetsa komanso kuganiza kwake.
Zanenedwa kuti nthawi ina, mnyamata wina adadza kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam napempha chilorezo chochita zina (chiwelewele). Ma Swahaabah (radhwiyallah anhum) adakhumudwa ndi kunyansidwa pazimenezi, koma Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adalankhula naye moleza mtima kuti: “Bwera kwa ine.”
Pambuyo pake Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamfunsa: “Kodi ungafune kuti wina achite chiwerewere ndi mayi ako?” Adayankha: “Ayi, 0 Mtumiki wa Allah! Ndipereka nsembe moyo wanga chifukwa cha Inu.”
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati mmene siungakondere iwe aliyenseso sangakonde kuti wina wake achite chiwerewere ndi mayi ake.”
Kenako Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adabwereza funso lomwelo ngati iye angakonde kuti wina wake achite chigololo ndi nchemwali wake ndi ana ake aakazi, azilongo ake komanso azakhali ake. Kenako Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamufotokozera kuti anthu enanso sangakonde kuti wina wake azichita chigololo ndi ana awo aakazi, alongo awo ndi azakhali awo.
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kenako adaika dzanja lake lodalitsika pa chifuwa cha Swahaabiyu ndikumupemphera duwa kwa Allah ponena kuti: “E, Allah! Mukhululukireni ndi kumuyeretsa ntima wake komanso yang’anirani maliseche ake kumuteteza ku tchimo la Zina.
Zotsatira za kalongosoredwe ka Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kumulongosolera Sahaabiyu mwachikondi chotere ndi kumuchitira duwa zidali choncho moti kuyambira tsiku limenelo ankanyansidwa kwambiri ndi nchitidwe ochita chigololo.
Kutsatira Njira Za Halaal Pomuphunzitsa Mwana Ndi Kumuika Kumalo a Chisilamu
Gawo lachitatu ndiloti njira za halaal ziyenera kutsatidwa kuti mwana aphunzire ndipo mwanayo akuyenera kudziwitsidwa malo achisilamu.
Kugwiritsa ntchito njia za haraam posakasaka maphunziro a mwana kapena kumuonetsera mwana malo olakwika kumangobweretsa zotsatira zolakwika ndikupangitsa mwanayo kukula ndi makhalidwe olakwika.
Kumuonetsa mwanayo ku maphunziro acjikunja kapena yunivesite, kapena kumusiya mwanayo m’manja mwa anthu omwe alibe makhalidwe a Chisilamu, kumabweretsa chionongeko ku makhalidwe a mwanayo.
Kukhala Ndi Nthawi Yokwanira Yocheza Ndi Ana
Chinthu chachinayi n’chakuti makolo ayenera kusonyeza chikondi ndi chimwemwe kwa ana awo ndikukhala nawo nthawi yokwanira. Munthawi yabwinoyi, ngati apeza kuti mwana wawo wasintha kuchoka pa khalidwe labwino ndi machitidwe, ndiye kuti ayenera kuwaongolera ndikuwatsogolera.
Momwemonso, munthawiyi, ayenera kugwirizana nawo, kukonza chikondi cha deen ndi Sunnah m’mitima yawo. M’malo mokambirana m’nyumba zokhudzana ndi zomwe zachitika padziko lapansi komanso kupeza chuma, makolo ayenera kukambirana za zomwe maSwahaabah radhwiyallahu anhum ankakwaniritsa ndi momwe adatsatirira Sunnah ya Rasulullah swallallahu alaihi wasallam m’miyoyo yawo.
Pochita izi, zolinga zomwe maSwahaabah anali nazo ndi kuzifera potumikira anthu, kusunga deen ndi chilungamo zidzapitirira kwa iwo ndikukhala zolinga zawo m’moyo.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu