12. Ngati mungadzukire pakati pa usiku, werengani dua yotsatirayi ya masnun ndipo pambuyo pake mutha kupempha kwa Allah Talaa. Insha Allah, dua yanu idzalandiridwa.
لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيْكَ لَهُ لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ وَهُوَ عَلٰى كُلِّ شَيْءٍ قَدِيْرْ اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ وَسُبْحَانَ اللهِ وَلَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ وَاللهُ أَكْبَرُ وَلَا حَوْلَ وَلَا قُوَّةَ إِلَّا بِاللهِ اَللّٰهُمَّ اغْفِرْ لِيْ
Palibe opembedzedwa mwachoonadi koma Allah Talaa yekha. Alibe mnzake. Kwa iye yekha ndikomwe kuli Ufumu, ndipo kutamandidwa konse ndi kwa Iye yekha, ndipo lye Ngolamulira chilichonse. Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu Talaa ndipo ulemelero ukhale kwa Allah ndipo palibe opembedzedwa mwachoonadi koma Allah. Ndipo Allah Talaa ndiye wamkulu, ndipo palibe mphamvu (yochitira zinthu zabwino) koma kupyolera mwa Allah Talaa!
Wina angathenso kubwereza dua iyi:
لَا إِلٰهَ إِلَّا أَنْتَ سُبْحَانَكَ اللّٰهُمَّ أَسْتَغْفِرُكَ لِذَنْبِيْ وَأَسْأَلُكَ رَحْمَتَكَ اَللّٰهُمَّ زِدْنِيْ عِلْمًا وَلَا تُزِغْ قَلْبِيْ بَعْدَ إِذْ هَدَيْتَنِيْ وَهَبْ لِيْ مِنْ لَدُنْكَ رَحْمَةً إِنَّكَ أَنْتَ الْوَهَّابُ
Palibe opembedzedwa mwachoonadi koma Inu. Ulemerero ukhale kwa Inu! O Allah Talaa ! Ndikukupemphani chikhululuko Pazolakwa zanga, ndipo ndikupemphani Chifundo Chanu! O Allah Talaa ! Mundichulukitsire kudziwa, ndipo musalore kuti mtima wanga usochere Pambuyo pondiongora, ndipo ndidalitseni kumbali Yanu ndi chifundo Chapadera, ndithu, Inu nokha Ndinu Opereka (madalitso ndi ubwino wonse)
13. Osagona m’malo amene anthu amadutsamo (monga mkolido kapena pakhomo) chifukwa izi zitha kupereka chipsinjo kwa ena ndipo zikhoza kukhala njira yoti muvulale kapena kuvulazidwa.
Olemekezeka Abu Hurairah (radiyalla anhu) akunena kuti Rasulullah (sawahalla alayhi wasallam) adati, “Mukamayenda m’malo obiriwira, chipatseni chiweto ufulu wake (kudzera mu kuyima m’malo osiyanasiyana kuti chiwetocho chidye). Mukayenda m’malo ouma nthawi ya chilala, malizitsani ulendo mwachangu (Musachedwetse ulendo wanu poyima m’malo osiyanasiyana kupewa kuchivutitsa chiwetocho). Paulendo, ngati muyenera kuima kuti mugone usiku pamalo ena ake, onetsetsani kuti simukugona pakati pa msewu chifukwa msewu ndi ufulu wa nyama (zokwera anthu apaulendo ndi anthu ake), komanso ndi malo opezekera tizilombo ndi zilengedwe zina zokhala ndi zapoizoni usiku (zomwe zingakupwetekeni). “
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu