
Nthawi ina,Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anatumiza ndalama zagolide mazana anayi kwa Abu ‘Ubaidah bin Jarraah (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo analamula mthumwiyi kuti ikadikire pang’ono kuti aone zomwe achite nacho chumacho.
Olemekezeka Abu Ubaydah (radhwiyallahu ‘anhu) atalandira ndalamazo, anati, “Allah amuchitire chifundo (kunena Umar).”
Kenako anauza kapolo wake wamkazi kuti, “Tenga ndalama zisanu ndi ziwirizi ukapereke kwa ujeniyo, ndipo zisanuzi kwa wakuti.” Mnjira imeneyi, anagawa chuma chonsecho. Kapoloyo anabwerera ndikumufotokozera Umar (radhwiyallahu ‘anhu).
Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kenako anatumiza ndalama yofanana nfi yomweyo kwa Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo anaiuza mthunwiyo malangizo omwewo.
Atalandira ndalamayo, Olemekezeka Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) anati, “Allah amuchitire chifundo (kunena za Umar).”
Olemekezeka Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) nayenso anagawa chuma chonse kupatula ma dinaar awiri omwe mkazi wake anamupempha kuti agwiritse ntchito pogula zinthu zomwe zinkafunikira. Mthumwi itamuuza Umar (radhwiyallahu ‘anhu) za zomwe anachita, Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anasangalala kwambiri ndipo anati, “Ndi abale omwe amachita ntchito zabwino.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu