6. Pangani ma dua komanso azkaar musanagone;
اللَّهُمَّ بِاسْمِكَ أَمُوْتُ وَأَحْيٰ
O, Allah Talaa mdzina Lanu ndikufa komanso ndiuka
7. Gonerani kumanja ndikuika dzanja lanu lamanja pansi pa tsaya lanu lakumanja.
Bibi Hafsah (radiyallahu anha) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akafuna kugona, ankaika dzanja lake lamanja pansi pa tsaya lake ndi kubwereza katatu mawu awa:
اللَّهُمَّ قِنِي عَذَابَكَ يَوْمَ تَبْعَثُ عِبَادَكَ
8. Osagona chafufumimba.
Olemekezeka Ya’eish Ghifaari (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina, ndinagona chafufumimba mu munzikiti chifukwa cha kuwawa kwa m’mimba. Mwadzidzidzi, munthu wina anabwera ndikundigwedeza ndi mwendo wake nati, “Kugona motere ( chamimba) n’kosasangalatsa kwa Allah Talaa) (ndinayang’ana kuti ndione amene ankandilankhula, kenako) ndinaona kuti ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam).
9. Musagone maliseche kapena kuonetsa maliseche M’malo mwake, gonani mutavala zovala zomwe zingabise umaliseche wanu.
Anas (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Abu Musah Ashari ankaphimba thupi lake (moyenera) akamagona kuonetsetsa kuti ziwalo zake zobisika sizikuonekera.
10. Gonani nthawi yabwino ndi cholinga choti mudzukire Tahajjud.
Olemekezeka Abud Dardaa (radiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati:Amene angagone usiku ndi cholinga chofuna choti adzukire Swala ya Tahajjud, ndipo maso ake ndikumugonjetsa mpaka nthawi ya Fajr, adzalandira mphotho ya Tahajjud kutengera Niyah yake ndipo tulo lake lidzatengedwa ngati sadaqah (madalitso) omwe walandira kuchokera kwa Mbuye Wake.
11. Musagone mutaswali swalah Maghrib popanda chifukwa, Ngati mukufuna kugona (chifukwa cha matenda kapena kutopa kwambiri) ndiye kuti mupeze wina kuti akudzutseni pa Esha kapena kutchera alamu.
Abu Barzah (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) sankasangalatsidwa kuti munthu agone swalah ya Esha isanapempheredwe (ngati pakutha pa Maghrib), ndikuchita zokambirana pambuyo pa Esha (ngati palibe chifukwa choyenerera).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu