Nkhani yotsatirayi ikuunikira kumvetsetsa kwakuya kwa dini ndi ma’rifat (kuzindikirika) ya Allah Talaa zomwe Allah Talaa adamudalitsa nazo Bishr Haafi (rahimahulla) zomwe zidachititsa kuti mpaka Imam Ahmad (rahimahulla) amutsanzire:
M’nthawi ya Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahulla) kunali dotolo wina yemwe ankatchedwa kuti Abdur Rahmaan At-Tabeeb.
Ankathandiza Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahulla) ndi Bishr Haafi (rahimahulla) akamadwala. Iye akulongosora:
Nthawi ina Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahulla) ndi Bishr Haafi (rahimahulla) onse anadwala.
Mkatikati mowathandiza onse awiriwo, ndinaona kusiyana kwa mayankho a onse awiri nditawafunsa za matenda awo.
Nthawi zonse ndikamufunsa Bishr (rahimahulla) momwe akumvera, poyamba amatamanda Allah Talaa kunena kuti “Alhamdulillah”, ndipo pambuyo pake amandiuza za mmene akumvera mthupi mwake.
Mbali inayi, ndikafunsa Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahulla) momwe akumvera, amangondiyankha kuti ali bwino. Sankandifotokozere vuto lenileni lomwe amakukumana nalo.
Tsiku lina ndidalankhula ndi Imaam Ahmad (rahimahulla) ndipo ndinati: “M’bale wako Bishr (rahimahulla) akudwala, ndipo ndikamufunsa momwe alili, akumayamba ndi kulemekeza Allah Talaa ndipo pambuyo pake amandiuza za mmene akumvera.
“Koma ndikakufunsani mumangonena kuti muli bwino.”
Imaam Ahmad (rahimahulla) atamva izi adati: “Mufunseni Bishr (rahimahulla) kuti adaphunzira kwa ndani?
Ndinamuyankha kuti, “Zimandivuta kumufunsa funso ngati limeneli.
Imaam Ahmad (rahimahulla) atamva zimenezi adati kwa ine: “Muwuze kuti, ‘M’bale wako Abu Abdillah Imaam Ahmad (rahimahulla) akuti ndikufunseni kuti mudaphunzira kwa ndani.”
Nditapita kwa Bishr (rahimahulla) ndidamufikitsira funso la Imaam Ahmad (rahimahulla).
Atamva funsolo adati: “Imam Ahmad (rahimahulla) safuna kutsatira kalikonse popanda kutsimikizira gwero lake.”
Ndipo Bishr (rahimahulla) adati: “Azhar (rahimahulla) anasimba kuchokera kwa Ibnu Awn (rahimahulla) yemwe wasimba kuti Ibnu Siiriin (rahimahulla) adati: “Kapolo akatamanda Allah Talaa asanene za vuto lake kudandaula kwake sikumatengedwa kuti ndikunyinyilika.”
Bishr anati, “Nthawi iliyonse mukandifunsa za vuto langa, ndikakuuzani za vuto lomwe ndikukumana nalo, ndimangochita izi kuti ndionetse kufooka kwanga ndikukuwonetsani mphamvu zomwe Allah Talaa ali nazo pa ine.”
Nditalandira yankho ili, ndinapita kwa Imam Ahmad ndikumuuza zomwe Bishr (rahimahulla) adanena.
Kuyambira tsiku limenelo, nthawi iliyonse ndikapita kwa Imam Ahmad (rahimahulla) ndikumufunsa za vuto lake, poyamba ankamutamanda Allah Talaa kenako ndikundidziwitsa za vuto lake.
Kuchokera pankhaniyi, tikuphunzirapo zinthu izi:
1. Maphunziro a dini ayenera kutsimikiziridwa kuchokera kwa ma Ulama owongoka bwino usanachitepo kanthu.
2. Ukakumana ndi vuto lililonse, umuyamike Mulungu Talaa ponena kuti Alhamdulillah, kumusonyeza Allah Talaa kuti ndiiwe osangalatsidwa ndi Mulungu Talaa pa chigamulo Chake.
3. Pamavuto, munthu anene kuti Alhamdulillah, potero akumbukire zabwino zosawerengeka za Allah Talaa ndikuthokoza kwa Allah Talaa ngakhale panthawiyi.
4. Munthu akanena kuti ‘Alhamdulillah’ asananene mavuto ake, n’zoonekeratu kuti sakudandaula za lamulo la Allah Talaa.
5. Ndi Sunnah kuti munthu agwiritse ntchito njira ya halaal pothandizika kumatenda ake.
Allah Talaa akudalitseni ndi kumvetsetsa koona kwa dini ndi tawfiiq yoyenda m’mapazi a anthu akale athu owopa Allah.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu