Chikondi cha Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) kwa Sayyiduna Muaaz bin Jabal (radhiwyallahu ‘anhu)

Sayyiduna Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti nthawi ina, Nabi (Swallallahu alaihi wasallam) anagwira dzanja langa nati kwa ine, “O Muaaz!”, ndipo ine ndinayankha kuti, “Ndili pano kuti ndikutumikireni.”

Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) kenako anandiuza kuti, “Ndithudi, ndimakukonda (chifukwa cha Allah Ta’ala).” Muaaz bin Jabal (Radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Ndikulumbira mwa Allah, inenso ndimakukondani.”

Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) kenako anamuuza kuti, “Kodi ndikuphunzitse dua yoti udziwerenga pakutha pa swala iliyonse?”

Muaaz (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Inde, (chonde ndiphunzitseni oh Mtumiki wa Allah)”.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adati kwa iye: “E Muaaz! ndikukulangiza kuti osasiya kuwerenga duwa iyi ukamaliza Swalah iliyonse.

اللهم أعني على ذكرك وشكرك وحسن عبادتك

O Allah! Ndithandizireni kuti ndikhale okukumbukirani, kukuthokozani ndi kukupembedzani mwaubwino.

(Al Adabul Mufrad #690 & Sunan Abi Dawood #1522)

Check Also

Kusamalitsa kwakukulu Kwa Sayyiduna Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) Potulutsa mahadith a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam)

Ole.wkezeka ‘Amr bin Maimoon (rahimahullah) adafotokoza za kusamalitsa kwakukulu kwa Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) …