M’chaka cha 13 cha nubuwwat, anthu 70 ochokera ku Ansaar anabwera ku Hajj ndipo analowa Chisilamu pamaso pa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam). Pakati pawo panali Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) yemwe anali ochokera ku fuko la Banu Salimah la Ansaar, ndipo anali m’gulu la anthu oyambilira ku fuko lawo kulowa Chisilamu.
Ma Ansaar atabwerera ku Madinah Munawwarah atatsiriza Hajj yawo, anayamba kuitanira anthu ku Chisilamu. Ambiri mwa mafuko a Banu Salimah anali atalowa Chisilamu, kupatulapo nkhalamba zina zomwe zinali zosakhulupirira. Pakati pawo panali Amr bin Jamuuh yemwe anali m’gulu la mafumu ndi atsogoleri a fuko la Banu Salimah Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) asanabwere ku Madinah Munawwarah.
Amr bin Jamuuh ankakonda kusunga fano lopangidwa kumatabwa lotchedwa Manaat, m’nyumba mwake. Ankalambira fanoli ndi kulilemekeza kwambiri. Tsiku lina, anyamata ena a fuko la Banu Salimah omwe analowa Chisilamu anaganiza zoponya fano la Amr bin Jamuuh m’chitsime mdzenje akapeza mpata ochita zimenezo. Choncho, usiku, Muaaz bin Amr (radhwiyallahu ‘anhu) – mwana wa Amr bin Jamuuh yemwe analowa Chisilamu, pamodzi ndi Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu), ndi gulu la achinyamata ena, analowa m’nyumba ya Amr bin Jamuuh mwachinsinsi, nachotsa fano lake, naliponya pansi mozondoka mchimodzi mwa zitsime za Banu Salimah chomwe anthu ankatayamo zinyalala zawo.
Amr bin Jamuuh atadzuka m’mawa ndikupeza kuti fano lake lasowa, anafuula kuti, “Tsoka kwa iwe! Ndani walakwira mulungu wathu (pomuba) usiku?” Kenako anatuluka kukafunafuna, mpaka analipeza m’chitsime cha zinyalala. Atalipeza, analitenga, kulitsuka, kulipaka mafuta onunkhira, ndikulilankhula nati, “Ndikulumbira mwa Mulungu, ndikamupeza amene wakuchitira izi, ndimuchititsa manyazi!”
Usiku ulionse omwe unkadutsa pambuyo pake, Amr bin Jamuuh ankagona, Muaaz bin Jabal ndi Muaaz bin Amr (radhwiyallahu ‘anhuma), pamodzi ndi gulu la achinyamata, ankachita zomwezo ku fano lake. M’mawa otsatira, akadzuka, Amr bin Jamuuh ankapeza fano lake lasowa, ndipo ankapitanso kukafunafuna. Akalipeza, ankalitsuka, ndikulipaka mafuta onunkhira.
Zimenezi zidapitirira kwa kanthawi, Amr bin Jamuuh anapachika lupanga lake pakhosi la fanolo nati, “Ndikulumbira mwa Mulungu, sindikudziwa amene akukuchita izi, koma ngati uli ndi ubwino ulionse, ndiye kuti utha kudziteteza! Nali lupanga ndikukupatsa (kuti udziteteze ku zoipa).”
Usiku umenewo, Muaaz bin Jabal ndi Muaaz bin Amr (radhwiyallahu ‘anhuma), pamodzi ndi gulu la achinyamata, anabwereranso kunyumba kwa Amr bin Jamuuh kukatenga fano lake. Anachotsa lupanga m’khosi mwa fanolo, anamanga galu wakufa, ndipo anaponya galuyo yemwe anali pa fanolo m’chitsime china mzitsime za fuko la Banu Salimah zomwe zinali zodzadza ndi zinyalala zotairamo anthu.
M’mawa otsatira, Amr bin Jamuuh adapezanso fano lake lasowa. Anapita kukafunafuna, mpaka analipeza m’chitsime litamangiriridwa ndi galu wakufa. Ataliona mmaonekedwe ochititsa manyaziwa anazindikira chowonadi ndipo analowa Chisilamu. Kenako analiyankhula nati:
تالله لو كنت إلها لم تكن أنت وكلب وسط بئر في قرن
Ukanakhala mulungu, iwe ndi galu simukanamangidwa pamodzi mchitsime!
أف لمصرعك إلها مستدن الآن فتشناك عن سوء الغبن
Tsoka kwa iwe kukhala mulungu onyozedwa pamene uli m’dothi ndi zinyalala! Popeza timakuganizirani mwina, takuzindikirani (kuti kukulambirani) inu ndi oipa!
فالحمد لله العلي ذي المنن الواهب الرزاق وديان الدين
Choncho kuyamikidwa konse ndi kwa Allah, Wapamwambamwamba, Mwini Ubwino uliwonse, Opereka madalitso Onse, Opereka riziki, Opereka zisankho, ndi Yemwe adatumiza Dini yoona (ya Chisilamu).
هو الذي أنقذني من قبل أن أكون في ظلمة قبر مرتهن
Iye ndi Yemwe adandipatsa chipulumutso (kudzera mu Imaan) ndisanatsekeredwe mumdima wa miyala.
بأحمد المهدي النبي المرتهن
Adandipulumutsa kudzera mwa Ahmed (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam), Nabiy owongoka yemwe ali oyang’anira chipembedzo cha Chisilamu. (Rawdhul Unuf 2/279)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu