
Abu Muslim Khowlaani (rahimahullah) akufotokoza kuti:
“Ndinalowa mumzikiti wa Hims ndipo ndinaona gulu la anthu. Pakati pawo panali anzake makumi atatu ndi awiri a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) omwe ankakambirana za mahadith kuchokera kwa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam).
Munkumanowu munali mnyamata, amene maso ake anali atapakidwa surma ndipo mano ake anali owala. Anali atavala shawl. Nthawi iliyonse anthu pankumanowu akamasiyana kapena kukayikira za nkhani iliyonse ya deen, ankamutchula, ndipo ankavomereza mawu ake ngati omaliza.”
M’nkhani ina, zanenedwa kuti Abu Muslim (rahimahullah) anafunsa anthu omwe anali pafupi naye kuti, “Kodi mnyamata uyu ndani?” Iwo anayankha kuti, “Ndi Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu).”
Abu Muslim Khowlaani (rahimahullah) akupitiriza kufotokoza kuti:
“M’mawa kwambiri, ndinapita ku mzikiti ndipo ndinapeza Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) akupemphera pafupi ndi mzati. Ndinayamba kupemphera pafupi ndipo atatembenuka kuti apemphere, ndinakhala pafupi naye kwambiri kotero kuti chinthu chokhacho pakati pathu chinali mzati. Tinakhala chete kwakanthawi mpaka nditamuyang’ana ndikunena kuti, ‘Ee Mu’aaz! Ndikulumbira m’dzina la Allah, ndimakukonda kuchokera pansi pa mtima, osati ndi chiyembekezo chopeza phindu lililonse lapadziko lapansi, kapena chifukwa cha ubale wabanja ndi ubale pakati pathu.’
Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) anafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani umandikonda mumtima mwako?’ Ndinayankha kuti, ‘Chikondi chomwe ndili nacho mumtima mwanga pa iwe ndi cha Allah Ta’ala yekha.’ Muaaz (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha, Kodi ichi ndi chifukwa chokhacho (chondikondera), ndinati, ‘Inde, ndikulumbira mwa Allah (ichi ndi chifukwa chokhacho).’ Anandifunsanso kuti, “Ndikulumbira mwa Allah, kodi ichi ndi chifukwa chokhacho (chomwe umandikondera). Ndinati, ‘Inde,ndikulumbira mwa Allah ( chifukwa chake ndichokhacho).’
Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) anandiuza kuti, ‘Ngati ichi ndi chifukwa chokhacho chomwe umandikondera, landira uthenga wabwino;’ pakuti ndidamva Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) akunena mawu a Allah Ta’ala, “Allah Ta’ala akuti, ‘Chikondi changa chimakhala chokakamizidwa kwa anthu awiri omwe amakondana chifukwa cha Ine ndekha, amakhala nthawi atakhala pamodzi chifukwa cha Ine ndekha, amachezerana chifukwa cha Ine ndekha ndipo amagwiritsa ntchito chuma pa wina ndi mnzake chifukwa cha Ine ndekha (monga Allah Ta’ala akunenera kuti adzawakondadi ndipo adzakondwera nawo). (Pa tsiku la Qiyaamah,) adzakhala ndi maguwa a Nur (kuwala), adzasangalala ndi mthunzi wa Arsh wa Allah Ta’ala ndipo adzachitiridwa nsanje ngakhale ndi Ambiyaa (alaihimus salaam) ndi ma Siddiiqiin (Musnad Ahmad #22276 & 22030)
Zindikirani: Ngakhale Ambiyaa ndi Siddiiiqiin adzakhale apamwamba kwambiri paulemelero ndi mphotho, iwo (Ambiyaa ndi Siddiiqiin) adzasonyeza chisangalalo pa mphotho yayikulu yomwe Allah Ta’ala adzapereka jwa anthu awa. kukondana wina ndi mnzake chifukwa cha Iye yekha padziko lapansi.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu