Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) Amuitana Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) ku Moyo Osatha

Salamah bin Tammaam (rahimahullah) akufotokoza kuti:

Masiku angapo Abdullah bin Mas’ud (radhiyallahu ‘anhu) asanamwalire, munthu wina adabwera kudzakumana naye. Atakumana naye, munthuyo anamuuza kuti, “Oh Ibnu Mas’ud! Usiku watha, ndinakulota. M’maloto, ndinamuona Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) atakhala pa guwa pomwe iwe unali pansi pake.

“Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anakulankhula nanu nati, ‘Oh Ibnu Mas’ud, bwera kwa ine pooeza anthu sanakuchitire zabwino (nditachoka padziko lapansi).”

Maloto amenewa anali chizindikiro chakuti nthawi ya Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) kuchoka padziko lapansi inali pafupi.

Munthuyo atamuuza Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) za malotowo, Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa kuti, “Ndikulumbira mwa Mulungu, kodi walotadi malotowa usiku watha?” Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndalota malotowa usiku watha.”

Pamenepo Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) adati kwa munthuyo, “Ndikukupemphani kuti mukhalebe ku Madinah Munawwarah kwa kanthawi ndipo munyamuke ku Madinah mukatsiriza kuswaliraswala jenezah yanga.”

Patatha masiku angapo Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu ‘anhu) anamwalira ndipo swala ya Janaazah inapemphetedwa ku Madinah Munawwarah. (Usdul Ghaabah 285/3)

Check Also

Chitsimikizo Cha Sayyiduna Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) Pa Mawu a Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam)

Ulendo wina, nthawi ya khilaafat yake, Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallhu ‘anhu) anabwera kudzacheza ndi Olemekezeka Abdullah …