
Mtumiki (swallallahu ‘alayhi wasallam) adati, “Munthu amene amamwalira ndi mliri, amakhala wamwalira imfa ya shahid.
Mu khilaafat ya Umar (radhwiyallahu ‘anhu), mliri wa Amwaas unakhudza Shaam m’chaka cha 17 pambuyo pa Hijrah. Mu mliriwu Abu Ubaidah (radhwiyallahu ‘anhu), mtsogoleri wa Asilamu ku Shaam, anakhudzidwa nawonso ndipo pambuyo pake anamwalira. Asanamwalire, adamusankha Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala mlowa m’malo wake.
Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) adalankhula ndi anthu ndipo adapereka ulaliki otsatirawu,
“Inu Anthu! Mliriwu ndi chifundo kwa inu! Ndi dua ya Nabi Mtumiki (Swallallahu ‘alayhi wasallam) ndipo inali njira ya anthu opembedza omwe anamwalira inu musanafike! Ndithudi Mu’aaz adapempha Allah Ta’ala kuti amupatse iye ndi banja lake gawo la mliriwu.”
Pasanapite nthawi yaitali, atabwerera kunyumba kuchokera ku Mzikiti, Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) adapeza kuti mwana wake wamwamuna wadwala ndipo akuvutika ndi mliriwu. Anapitiriza kumusamalira ndi kumuyang’anira mpaka pamapeto pake anamwalira.
Malinga ndi nkhani zina, ana ake aakazi awiri nawonso anamwalira ndi mliriwu.
Pambuyo pake, Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) mwiniwakeyo anadwalanso ndipo anamwalira. Poyambilira adaona zilonda zikuonekera padzanja lake, zomwe zinali zizindikiro za mliriwu, adati chifukwa cha chisangalalo ndi chimwemwe akuyang’ana dzanja lake, “Sindili okonzeka kusinthana (gawo la mliriwu lomwe likundivutitsa) ngakhale ndi ngamila zofiira (za ku Arabiya zomwe zinkatengedwa kuti ndiye chuma chamtengo wapatali malinga ndi Aarabu)!”
Pambuyo pake,Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) nayenso adachoka padziko lapansi.
(Kashful Astaar #3042, Al Bidaayah wan Nihaayah 10/43, At Tabaqaatul Kubra 3/441, Siyaru A’laamin Nubalaa 3/288)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu