Ma Dua Onena Ukalota Zoipa

Ngati mukuchita mantha usiku chifukwa cholota maloto oipa, werengani ma dua awa:

Dua Yoyamba

أَعُوْذُ بِكَلِمَاتِ اللهِ التَّامَّاتِ الَّتِيْ لَا يُجَاوِزُهُنَّ بَرٌّ وَلَا فَاجِرٌ مِنْ شَرِّ مَا يَنْزِلُ مِنَ السَّمَاءِ وَمَا يَعْرُجُ فِيْهَا وَمِنْ شَرِّ مَا ذَرَأَ فِي الْأَرْضِ وَمَا يَخْرُجُ مِنْهَا وَمِنْ شَرِّ فِتَنِ اللَّيْلِ وَفِتَنِ النَّهَارِ وَمِنْ شَرِّ طَوَارِقِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ إلَّا طَارِقًا يَطْرُقُ بِخَيْرٍ يَا رَحْمٰنْ

Ndikudzitchinjiriza m’mawu athunthu a Allah Talaa omwe munthu owopa Allah ngakhale ochimwa angapose; kuchokera ku zoipa zimene zimatsika kumwamba ndi zimene zikukwera m’menemo, ndi zoipa zimene adazilenga m’nthaka ndi zotuluka m’menemo, ndi ku zoipa za mayeso a usiku ndi mayeso a usana, ndi kuopsya kwa zolengedwa zimene zimatuluka usiku ndi usana, kupatula zimene zimadza ndi zabwino, Wachifundo chambiri.”

Dua Yachiwiri

اَللّٰهُمَّ رَبَّ السَّمَاوَاتِ السَّبْعِ وَمَا أَظَلَّتْ وَرَبَّ الْأَرْضِيْنَ وَمَا أَقَلَّتْ وَرَبَّ الشَّيَاطِيْنِ وَمَا أَضَلَّتْ كُنْ لِيْ جَارًا مِّنْ شَرِّ خَلْقِكَ أَجْمَعِيْنَ أَنْ يَفْرُطَ عَلَيَّ أَحَدٌ مِّنْهُمْ أَوْ أَنْ يَّطْغٰى عَزَّ جَارُكَ وَتَبَارَكَ اسْمُكَ

O Allah wa mitambo isanu ndi iwiri ndi zomwe zimaphimba, ndi Mbuye wa dziko lapansi (nthaka isanu ndi iwiri) ndi cholengedwa chilichonse chomwe chimanyamula (pamwamba pake), ndi Mbuye wa mashayaatiin ndi omwe akuwasokeretsa, khalani mtetezi wanga (ndi kunditeteza) ku zoipa za zolengedwa Zanu zonse, kuti aliyense wa iwo apitirire malire pondichitira kapena kundivulaza. Chitetezo chanu ndi chachikulu, ndipo dzina lanu likwezedwe.

Duwa Yachitatu

أَعُوْذُ بِكَلِمَاتِ اللهِ التَّامَّاتِ مِن غَضَبِهِ وَعِقَابِه وَشَرِّ عِبَادِهِ وَمِنْ همَزَاتِ الشَّيَاطِيْنِ وَأَنْ يَحْضُرُوْنْ

Ndikupempha chitetezo kudzera m’mawu athunthu a Allah Talaa ku mkwiyo Wake, chilango Chake, kuipa kwa akapolo Ake, manong’onong’ono a ma shayaatiin ndi kupezeka kwa zoipa zawo.

Dua Yachinayi

لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ الْوَاحِدُ الْقَهَّارُ رَبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا الْعَزِيْزُ الْغَفَّارُ

Palibe wina opembedzedwa mwachoonadi koma Allah Talaa, (Mmodzi) Mwini mphamvu zoposa, Mbuye wakumwamba ndi pansi ndi zopezeka pakati pake, Mwini Mphamvu zoposa, Okhululuka.

Zindikirani: Dua imeneyi iyenera kuwerengedwa ukadzukira mkatikati mwa usiku.

Check Also

Sunnati Ndi Adaab 1

1. Mukamaliza Swala ya Esha, musakhale kumacheza nkhani zopanda pake mmalo mwake yesetsani kugona mwachangu …