Madua Ndi Azkaar Ogonera

Dua 1

اَللّٰهُمَّ بِاسْمِكَ أَمُوْتُ وَأَحْيٰى

Eh Allah! Talaa mdzina Lanu ndidzafa ndikukhala ndi moyo.

Dua 2

اَللّٰهُمَّ قِنِيْ عَذَابَكَ يَوْمَ تَبْعَثُ عِبَادَكَ

Eh, Allah! ndipulumutseni ku chilango Chanu tsiku limene Mudzaukitse akapolo Anu (m’manda).

Dziwani: Mtumiki (sallahu alayhi wasalam) ankawerenga dua iyi.

Duwa 3

اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ الَّذِيْ أَطْعَمَنَا وَسَقَانَا وَكَفَانَا وَآوَانَا فَكَمْ مِمَّنْ لَا كَافِيَ لَهُ وَلَا مُؤْوِيَ

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa yemwe adatipatsa chakudya, chakumwa, watikwaniritsa zofunika zathu ndi kutipatsa pogona. Achulukirenji amene alibe owakwaniritsira, ngakhalenso owasamalira.

Dua 4

أَسْتَغْفِرُ اللهَ الَّذِيْ لَا إِلٰهَ إِلَّا هُوَ الْحَيُّ الْقَيُّوْمُ وَأَتُوْبُ إِلَيْهْ

Ndikupempha chikhululukiro kwa Allah amene palibe wina olambieidwa kupatula Iye, amene ndi Wamoyo Wamuyaya, Osunga chilichonse chomwe chilipo, ndipo ndikutembenukira kwa Iye polapa.

Zindikirani: Ubwino owerenga dua iyi ndikuti machimo onse ang’onoang’ono a munthu amakhululukidwa.

Abu Sa’id (radhwiyallahu anhu) wafotokoza kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amawerenga istighfaar katatu asanagone Allah amamukhululukira machimo ake ngakhale atakhala ochuluka ngati thovu la m’nyanja, masamba a m’mphepete mwa nyanja, mchenga wa ku Aalij (malo opezeka m’chipululu omwe muli milu ya mchenga ochuluka), ndi masiku a dunya.

Check Also

Sunnati Ndi Adaab 1

1. Mukamaliza Swala ya Esha, musakhale kumacheza nkhani zopanda pake mmalo mwake yesetsani kugona mwachangu …