Abstract apocalyptic background - burning and exploding planet Earth in red sky, hell, end of world. Elements of this image furnished by NASA

Nkumano pakati pa Tamim Daari ndi Dajjaal

Mmahadith ambiri, Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adauza anthu za ma fitnah a Dajjaal ndi chisokonezo chomwe adzabweretse padziko lapansi akadzatulukira.

Poyamba, Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) sanadziwitsidwe ndi Allah Ta‘ala za nthawi yeniyeni yomwe Dajjaal adzaonekere padziko lapansi. Izi zitha kutsimikizika kudzera mu Hadith iyi pomwe Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adafotokoza kuthekera kwa Dajjaal kutulukira mnthawi ya moyo wake kapena pambuyo pa iye. Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ngati adzabwere ine ndiri moyo, ndiye kuti ndidzathana naye, ndipo ngati adzabwere ine nditamwalira, ndiye kuti munthu aliyense adzayenera kuyesetsa kudzipulumutsa ku ma fitnah ake, ndipo Allah Ta‘ala akhale ondiyimilira wanga kudzapulumutsa Msilamu aliyense.” (Saheeh Muslim #2937)

Komabe, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) asadachoke pa dziko lapansi, Allah Ta’ala adamudziwitsa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) za malo enieni a Dajjaal komanso nthawi yomwe idzabwere Qiyaamah. Kenako Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adauza ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kudzera mahadith ambiri kuti kubwera kwa Dajjaal padziko lapansi kudzachitika Qiyaamah isanafike, ndikuti Nabiy Isa (‘alaihis salaam) adzatumizidwa kuti akamuphe.

Komanso, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) asanachoke pa dziko lapansi, Tamim Daari (radhwiyallahu ‘anhu) adamudziwitsanso Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) za kukumana kwake ndi Dajjaal, ndipo Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adawadziwitsa ma Swahaabah za kukumana kwake ndi Dajjaal.

Tamim Daari (Radhwiyallahu ‘anhu) adalowa Chisilamu m’chaka cha chisanu ndi chinayi pambuyo pa hijrah, ndipo Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adachoka pa dziko lino kumayambiriro kwa chaka chakhumi ndi chimodzi pambuyo pa hijrah.  (Siyar A’laamin Nubalaa 2/442)

Atalowa Chisilamu, Tamim Daari (radhwiyallahu ‘anhu) anabwera kwa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) ndipo anamuuza kuti asanalowe Chisilamu, pamene iye ndi anzake anali paulendo wa panyanja, anakumana ndi chimphepo champhamvu chomwe chinapangitsa kuti sitima yawo ikankhidwe pachilumba china. Pachilumbachi, adamuona Dajjaal, atamangidwa unyolo, ndipo kukambirana komwe kudatenga nthawi yaitali kunayambika pakati pawo ndi Dajjaal.

Check Also

Kuwonekera kwa Nkhani Zikuluzikulu Mahdi Asanafike – Zizindikiro za Qiyaamah

Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) asanaonekere padziko lapansi, anthu ambiri padziko lonse lapansi adzakhala Akhristu. (Muslim #2898) …