Gulu Lankhondo Lokhala ndi Mbendera Zakuda Lochokera ku Khurasaan

Pambuyo poti Mahdi waonekera pakati pa anthu ndipo nkhani ya kuonekera kwake yayamba kufalikira padziko lonse lapansi, gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda lidzachoka ku Khurasaan kupita ku Makkah Mukarramah ndikukhalira limodzi ndi Mahdi. Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adalimbikitsa ummah kuti udzakhale ndi gulu lankhondo limeneli pobwera kwa Mahdi.

Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Mukadzaona gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda likuchokera ku Khuraasaan (likupita ku Makkah Mukarramah kukagwirizana ndi Mahdi), ni ndi gulu lankhondo ili. Popeza ndithudi, mgulu lankhondo limeneli mudzakhala Khaleefah wa Allah Ta‘ala, Mahdi (kutanthauza kuti adzakhala mgulu lankhondo ili akadzagwirizana naye ku Makkah Mukarramah).” (Musnad-e-Ahmed #22387)

Mu nkhani ina, Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adanena kuti munthu aliyense adzayenera kuyesetsa kuti adzakhale nawo mgulu lankhondo la Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu), ngakhale atadzachita kudzikhukhuluza pansi mu sinowo kuyesa kukalifikira. (Sunan Ibnu Maajah #4084 ndi Al-Fitan li-Nu’aim #853 )_

M’ma Riwaayaat ena, pali magulu ena ankhondo omwe adzanyamure mbendera zakuda. Komabe, sadzakhala gulu lankhondo la Mahdi. kotero, ndikofunikira kuti ummah usadzasokonezeke kulizindikira gulu la Mahdi. Chinthu chodziwika bwino cha gulu lankhondo la Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) ndichakuti adzakhala anthu olungama, chifukwa adzakhala akusunga Sunnah ya Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) nthawi zonse.

Gulu lankhondo la Khurasaan likadzalowa m’gulu la Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) ku Makkah Mukarramah, Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) adzachoka ku Makka Mukarramah ndi asilikali kupita ku Madina Munawwarah.

Akadzafika ku Madinah Munawwarah, Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) adzabwera ku Rowdhah Mubaarak ndikupereka salaamu yake kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam). (Qiyaamat kub Aaegi pg. 90) Adzapulumutsanso anthu a ku Madina Munawwarah ndi ma Sayyid omwe adzakhale kuti adatsekeredwa m’ndende ndi kuzunzidwa ndi gulu lankhondo la Sufyaani. (Ishaa’ah tsamba 206)

Pochoka ku Madina Munawwarah, Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu), pamodzi ndi gulu lankhondo la Asilamu, adzamenya nkhondo zambiri. Zina mwa nkhondo zomwe adzamenyane ndi nkhondo yolimbana ndi gulu la Sufyaani. Pankhondoyi, Allah Ta ‘ala adzadalitsa gulu lankhondo la Mahdi ndi chigonjetso.

Akadzapambana, Mahdi adzagawa zofunkha pakati pa gulu lake lankhondo motsatira Sunnah ya Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), ndipo kuyambira pamenepo, Chisilamu chidzayamba kufalikira padziko lapansi.

Pofotokoza za nkhondo ndi Sufyaani ndi chigonjetso chimene Allah Ta‘ala adzamupatse Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu), Rasulullah (Swallallahu ‘alayhi wasallam) adati:

“Munthu ochokera mwa Aquraish, amene banja lake la amayi ake lidzachokera ku fuko la Kalb (Yemwe ndi Sufyaani), adzatuluka ndi kutumiza gulu lankhondo motsutsana ndi Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi omutsatira ake. Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi omutsatira ake adzagonjetsa gulu limeneli. Gulu lankhondo limenelo lidzakhala lochokera ku fuko la Kalb, ndipo amene sadzakhalapo nthawi imene zofunkha zomwe zidzatengedwe kuchokera ku fuko la Kalb zidzagawidwa adzakhala otaika (amene sadzakhala nawo m’gulu lankhondo la Mahdi, akumenyana ndi gulu lankhondo la Sufyaani mpaka kumapeto adzatayika). Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) adzagawa chuma ndipo adzathandiza anthu mogwirizana ndi sunnah ya Nabi wawo (Swallallahu alaihi wasallam). Kenako Chisilamu chidzakhala champhamvu ndi kukhazikika padziko lapansi.” (Abu Dawood #4286 )

Asilamu Agwirizana Pangano La Mtendere ndi Akristu

Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) asanabwere, Asilamu adzalowa mumgwirizano ndi gulu la Akristu. Pambuyo pake, Asilamu adzathandiza anzawo achikhristu polimbana ndi mdani wa Akristu. Pankhondoyi, Asilamu ndi anzawo achikhristu adzapambana. Akadzagonjetsa mdani, Asilamu ndi anzawo achikhristu adzagawana pakati pawo katundu yemwe adzapezeke pankhondoyi.

Panthawiyo, mkangano udzachitika pakati pa Asilamu ndi akhristu. Mkanganowo udzayamba pamene m’modzi mwa Akristu adzanena kuti kupambana komwe kwachitika ndi chifukwa cha mdalitso wa mtanda wachikhristu. Asilamu akadzamva izi adzakwiya ndipo adzanena kuti kupambanako kwachitika chifukwa cha thandizo la Allah Ta‘ala, osati mtanda.

Kenako Msilamu adzadzuka ndikuphwanya mtanda wa Akristu. Pobwezera, Akristu adzamupha, ndipo izi zidzayambitsa nkhondo pakati pa magulu awiriwa. Chifukwa cha kumenyanaku, mgwirizanowu udzathera panjira ndipo nkhondo idzayamba pakati pa Asilamu ndi Akristu.

Asilamu adzagonjetsedwa nkhondoyi ndipo Akristu adzapambana.

Mu Hadith ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anaifotokoza nkhondoyi ponena kuti, “(Asilamu) Mudzalowa mu pangano la mtendere ndi Akristu mpaka mudzathandizana nawo kumenyana ndi adani awo, Mudzawagonjetsa ndi kupeza chuma chawo, ndipo pobwerera, mukadzafika dera lokhala ndi zitunda zambiri, m’modzi mwa Akristu adzanena kuti, ‘Mtanda wapambana!’ M’modzi mwa Asilamu adzayankha kuti, ‘Ayi! Allah watipambanitsa!’ Asilamu adzathamangira ku mtanda wa Akristu, omwe udzakhale uli pafupi, ndi kuuswa. Akristu adzathamangira kwa Msilamu amene adzaswe mtanda wawo ndi kumupha. Kotero Asilamu adzathamangira pa zida zawo ndipo nkhondo idzabuka pakati pa magulu awiriwa. Asilamu adzagonja nkhondoyi ndipo Allah Ta ‘ala adzadalitsa gulu la Asilamu kudzera mu kuphedwa.” (Saheeh Ibnu Hibbaan #6708)

Pamapeto pa nkhondoyi, Allah Ta‘ala adzatumiza Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo likulu la Asilamu lidzakhala ku Ghootah pafupi ndi Damascus.

Olemekezeka Abu Dardaa (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adanena kuti, “Ndithudi gulu lankhondo la Asilamu panthawi ya nkhondo yaikulu lidzakhala ku Ghootah pafupi ndi mzinda otchedwa Damascus, omwe uli m’mizinda yabwino kwambiri ya Shaam.” (Sunan Abu Dawood #4298)

Check Also

Maonekedwe a Nabi Isah ‘alaihis salaam

Nabi Isa (‘alaihis salaam) anatumizidwa ndi Allah Ta‘ala kwa Bani Israa’eel. Limodzi mwa malamulo omwe …