Abstract apocalyptic background - burning and exploding planet Earth in red sky, hell, end of world. Elements of this image furnished by NASA

Nkhondo Yaikulu ndi Kugonjetsedwa kwa Istanbul

Mahdi atabwera, Allah Ta‘ala adzawapatsa Asilamu uysogoleri ndi mphamvu padziko lonse lapansi. Akristu adzazindikira kuti Asilamu akupeza thandizo ndipo akukula mphamvu tsiku ndi tsiku. Kenako adzakonza gulu lankhondo lalikulu kuti amenyane ndi Mahdi ndi Asilamu.

Zanenedwa mu Hadith kuti Akristu ochokera m’maiko onse adzasonkhanitsa asilikali awo ndikukonzekera kumenyana ndi Asilamu. Gulu lankhondoli lidzakhala ndi mbendera 80 ndipo padzakhala asilikali 12,000 pansi pa mbendera iliyonse, kotero chiwerengero chawo chonse chidzafika pa 960,000.

Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adalosera za kuchitika kwa nkhondo yayikuluyi ndipo adayitcha kuti “Malhamah-e-Kubra – Nkhondo Yaikulu”. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Akhristu onse adzagwirizana pa nkhondo yaikulu. Adzakumenyani pansi pa mbendera makumi asanu ndi atatu. Anthu zikwi khumi ndi ziwiri adzayenda pansi pa mbendera iliyonse.” (Ibnu Hibbaan #6708)

Nkhondo yaikuluyi idzachitika pamalo pafupi ndi A’maaq ndi Daabiq (malo onsewa ali kufupi ndi Halab ku Syria). Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzakhalapo kuti adzatsogolere Asilamu pankhondoyi. Makafiri onse adzagwirizana kutsutsana ndi Asilamu ndipo nkhondo yoopsa idzachitika.

Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Qiyaamah sidzachitika mpaka osakhulupirira atamanga msasa kuti amenyane nanu ku A’maaq kapena Daabiq. Panthawiyo, gulu lankhondo lochokera mumzinda, lomwe lidzakhale ndi anthu abwino kwambiri padziko lapansi panthawiyo (ngati gulu lankhondo la Mahdi [radhwiyallahu ‘anhu]), lidzatuluka kudzamenyana nawo.

“Mizere yankhondo ikadzakonzedwa, Aroma (Akhristu) adzauza Asilamu kuti, “Perekani okhulupirira amene amenyane nafe ndi kutenga anthu athu ngati akapolo (popeza sitinabwere kudzamenyana nanu nonse, koma tabwera kudzamenyana ndi amene amenyane nafe ndi kutenga anthu athu ngati akapolo).” Asilamu adzayankha kuti, “Ayi, sitipereka abale athu kwa inu!”

“Kenako nkhondo idzayamba pomwe gawo limodzi mwa magawo atatu a gulu lankhondo la Asilamu lidzagonjetsedwa (ndi kuthawa kunkhondo), ndipo Allah Ta’ala sadzawakhululukira. Gawo lina mwa magawo atatu a gulu lankhondo la Asilamu lidzaphedwa, ndipo adzakhala m’gulu la ophedwa abwino kwambiri panthawiyo pamaso pa Allah Ta’ala. Pomaliza, gawo limodzi mwa magawo atatu otsala a gulu lankhondo la Asilamu lidzagonjetsedwa. Sadzakumananso ndi mayesero omwe adzagonjetsedwe kwa moyo wawo onse.” (Muslim #2897)

Pambuyo pa chigonjetso cha Asilamu ichi, ma kuffaar sadzakhala ndi chiyembekezo cholamulira ndikugwiritsa ntchito mphamvu padziko lapansi. Pambuyo pake, Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzakonzekera kugonjetsa Istanbul. Panthawiyo, Istanbul idzakhala pansi pa ulamuliro wa ma kaffaar.

Kugonjetsedwa kwa Istanbul

Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzanyamuka ndi anthu okwana 70,000 kuchokera ku Banu Ishaaq kupita ku Istanbul. Adzakwera zombo za Imam Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndikufika ku Istanbul. Akadzafika pa makoma a mzindawo, adzafuula kuti, “Laa ilaaha illallah Allahu Akbar!” mokweza. Kudzera mu barakah yopanga takbeer, makoma a mzindawo adzagwa. Asilamu adzalowa mumzindawo ndi kutenga ulamuliro.

Kuchuluka kwa nthawi ya pakati pa nkhondo yaikulu yolimbana ndi Akristu ndi Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) kugonjetsa Istanbul idzakhala pafupifupi zaka zisanu ndi chimodzi. Pambuyo pake, Dajjaal adzaonekera m’chaka chachisanu ndi chiwiri.

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adafunsa Maswahaabah (radhwiyallahu ‘anhum), “Kodi mwamvapo za mzinda omwe uli ndi gawo limodzi pamtunda ndi gawo lina panyanja (kunena Istanbul)?” Maswahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) anayankha movomereza.

Kenako Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Qiyaamah sidzachitika anthu okwana 70,000 ochokera kwa Bani Ishaaq atamenyana nawo (madera awiriwa). Akadzafika kumeneko, adzatsikira pamenepo. Sadzamenyana ndi zida kapena kuponyerana mivi. M’malo mwake, adzafuula kuti “Laa ilaaha illallah Allahu Akbar!” gawo lomwe lili m’nyanja lidzagwa. Kenako adzafuula kachiwiri kuti “Laa ilaaha illallah Allahu Akbar!” pamenepo gawo lina lidzagwaso. Kenako adzafuula kachitatu kuti “Laa ilaaha illallah Allahu Akbar!” ndipomweno padzatseguke malo ena ake. Kenako adzalowa mumzinda ndikutenga zofunkha. akadzagawa zofunkhazo, adzamva mfuu onena kuti, “Dajjaal watuluka!” Kotero adzasiya chilichonse ndikubwerera.” (Muslim #2920)

Mu Hadith ya Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) ndi Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) mu Saheeh Muslim, zatchuridwa kuti, “Pambuyo pogonjetsa Constantinople (Istanbul) pamene Asilamu akamadzagawana katundu olanda kunkhondo atapachika malupanga awo pamitengo ya azitona, shaitaan adzafuula pakati pawo, ‘Ndithudi Maseeh (Dajjaal) wabwera kwa mabanja anu inu kulibe.’ Kotero adzachoka ku Constantinople. Adzatumiza okwera pamahatchi ochepa patsogolo kuti akafufuze za nkhaniyo koma adzapeza kuti zinali mphekesera chabe ndipo Dajjaal sanatuluke. Komabe, nthawi ina yake akadzafika ku Shaam, Dajjaal adzatuluka. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, ‘Ndithudi, ndikudziwa maina a okwera pamahatchi, maina a makolo awo ndi mtundu wa akavalo awo. Adzakhala okwera pamahatchi abwino kwambiri padziko lapansi tsiku limenelo.’” (Muslim #2897, 2899)

Mu Hadith ina, Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Dela la Baytul Muqaddas lomwe likutukuka (ndi makafiri kutenga dzikolo) lidzayambilira, pambuyo pake Yathrib (Madinah Munawwarah) lidzakhala lopanda kanthu (pa nkhani ya hidaayat). Madinah Munawwarah lkukhala yopanda kanthu kudzachitika nkhondo yaikulu isanayambe. Nkhondo idzayamba Constantinople isanagonjetsedwe (ndi Mahdi komanso Asilamu). Constantinople idzagonjetsedwa Dajjaal asanafike.” (Abu Dawood #4296)

Check Also

Moyo Wa Nabi Issah Alaihis Salaam Akadzabweranso Padziko Lapansi Ndi Kuchuluka Kwa Madalitso Ndi Chitetezo Mnthawi Yake

Nabi Isa (‘alaihis salaam) akadzabwerera padziko lapansi, Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) adzakhala mtsogoleri otsogolera Asilamu. Mahdi …