Kutuluka kwa Dajjaal ndi Ma Fitnah Ake Osiyanasiyana

Dajjaal akadzaonekera padziko lapansi, adzayamba kutulukira ndi kum’mawa kwa dziko, pakati pa Syria ndi Iraq. Pambuyo pake, adzapita ku Isfahaan komwe Ayuda 70,000 adzakhale naye limodzi. (Muslim #2944)

Adzayenda padziko lonse lapansi, ndipo kulikonse komwe akupita, adzabweretsa fitnah yaikulu komanso ziphuphu zambiri. Malo awiri okha omwe sadzatha kulowamo ndi Makkah Mukarramah ndi Madinah Munawwarah.

Akadzafika ku Makkah Mukarramah, adzayesa kulowamo koma sadzatha kutero chifukwa Makkah Mukarramah idzatetezedwa ndi angelo. Kenako adzayesa kulowa ku Madinah Munawwarah, koma sadzatha kulowamo chifukwa idzatetezedwanso ndi angelo.

Mu Hadith inayake, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Palibe dziko lomwe lidzatsalire kupatura kuti Dajjaal adzalowamo ndi kulilamulira, kupatula Makkah Mukarramah ndi Madinah Munawwarah. Sadzayandikira mizinda iwiriyi kuchokera m’njira zawo zilizonse kupatula kuti angelo adzayang’anizana naye ndi malupanga osavindikira, mpaka atakakhala paphiri laling’ono lofiira komwe dziko lamchere limathera.” (Ibnu Maajah #4077)

Mu Hadith ina, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Kuopa Masiih Dajjaal sikudzalowa mu Madinah Munawwarah. Tsiku limenelo (pokhala nthawi imene Dajjaal adzatulukire ndikubwera ku Madinah Munawwarah,) kudzakhala zipata zisanu ndi ziwiri, ndipo pachipata chilichonse padzakhala angelo awiri (oteteza pakhomo).” (Bukhaari #1879)

Paulendo wake, adzasocheretsa anthu ndikuwapangitsa kutaya imaan yawo. Makuffaar adzagwirizana naye ndikumuthandiza, mpaka gulu lake lankhondo ndi omutsatira ake adzachuluka kwambiri. Poyamba adzadzitcha kuti ndi mneneri, koma pambuyo pake adzayamba kunena kuti ndi Allah. (Muslim #2937, Fathul Baari 13/97) Kukhala kwake konse padziko lapansi, akadzatuluka, kudzakhala masiku makumi anayi (40).

Madinah Munawwarah idzagwidwa ndi zivomerezi zitatu. Chifukwa cha zivomerezi, wachinyengo aliyense wamwamuna ndi wamkazi adzachoka ku Madinah Munawwarah. Atachoka ku Madinah Munawwarah, adzakhala nawo mgulu lankhondo la Dajjaal. Mwanjira imeneyi, Madinah Munawwarah idzathamangitsa anthu ake oipa, monga momwe zivomerezi zimatsukira nyasi zake. Tsiku limenelo lidzatchedwa “tsiku la khalaas” (tsiku loyeretsa). (Muslim #2943, Haakim #8631)

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Dajjaal adzatuluka m’njira pakati pa Shaam ndi Iraq ndipo adzafalitsa chisokonezo kulowera Kumpoto. Inu atumiki a Allah, khalani olimba mtima! Ndikukupatsani kufotokozera kwake komwe palibe Nabi amene adapereka (kwa anthu ake). Poyamba adzati, “Ine ndine Nabi,” pomwe palibe Nabi pambuyo panga. Kenako adzanenanso kachiwiri kuti, “Ine ndine Rabi wanu,” pomwe simudzamuona Rabi wanu mpaka mutamwalira. Ali ndi diso lofooka, pomwe Rabi wanu alibe diso lofooka (popeza Allah Ta‘ala alibe zilema zonse). Mawu oti ‘Kaafir’ adzalembedwa pakati pa maso ake. Okhulupirira aliyense, kaya ndi ophunzira kapena ayi, adzatha kuwawerenga.”

Moto ndi Munda Za Dajjaal

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Mwa ma fitnah ake ndi kuti adzakhala ndi munda ndi moto. Moto wake udzakhala munda, ndipo munda wake udzakhala moto. Munthu amene angadzakumane ndi mayesero a moto wake adzayenera kupempha thandizo kwa Allah Ta‘ala ndikuwerenga mavesi oyambilira a Surah Kahf. Motowo udzakhala ozizira komanso otetezeka kwa iye, monga momwe unalili kwa Nabi Ebrahim (‘alaihis salaam).

Dajjaal Kuukitsa Akufa

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Mkakati mwa ma fitnah ake ndi kuti azidzamuuza munthu wakumidzi, “Ndilore ndikuukitsire abambo ako ndi amayi ako, ngati ndingatero kodi ukhulupilira kuti ndine mbuye wako?” Munthuyo adzayankha kuti, “Inde.” Kenako mashaitani awiri adzaonekera pamaso pake owoneka ngati makolo ake ndipo adzati kwa iye, “Mwana okondedwa! Mutsatire, popeza iye ndiye mbuye wako!”

“Ma fitnah ake ena ndikuti adzakhala ndi mphamvu pa munthu wina amene adzamuphe ndikuligawa thupi lake pawiri . Kenako adzati, “Tamuona kapolo wangayu! Tsopano ndimuukitsa, yemwe pambuyo pake anenabe kuti sindine mbuye wake.” Allah Ta‘ala adzaukitsa munthu uyu. Dajjaal oipayo adzamufunsa kuti, “Kodi mbuye wako ndani?” Adzayankha kuti, “Mbuye wanga ndi Allah, ndipo iwe ndiwe mdani wa Allah! Ndiwe Dajjaal! Ndikumbira mwa Allah! Sindinakhalepo ndi chitsimikizo kuti Dajjaal ndiiwe kuposa momwe ndiliri lero!”

Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kenako adati, “Kapolo ameneyo adzakhala ndi mohamvu zapamwamba kwambiri mu ummah wanga ku Jannah (mwa anthu a nthawi imeneyo).” Sayyiduna Abu Sa’iid (radhwiyallahu ‘anhu) adati, “Ndikulumbira mwa Allah! Sitinkaganiza kuti munthu ameneyo ndi wina aliyense kupatula Umar bin Khattaab (radhwiyallahu ‘anhu), mpaka atamwalira (ndipo tinazindikira kuti sanali iyeyo).”

Dajjaal Achititsa Mvula Kugwa Ndipo Ziweto Zikhala Zonenepa Ndi Zathanzi

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adapitiliza kunena kuti, “Ena mwa ma fitnah ake ndi kuti adzadutsa mdera linalake ndipo anthu ake adzamukana. Pambuyo pomukana, palibe chiweto chawo chomwe chidzatsale pokhapokha zidzafa.

“Ena mwa ma fitnah ake ndi kuti adzadutsa mdera lina ndipo anthu ake adzamulandira. Pambuyo pomulandira, adzalamula ntambo kuti ugwetse mvula ndipo lidzatero, ndipo adzalamula nthaka kuti ibereke mbewu ndipo idzatero, mpaka ziweto zawo zidzabwerera madzulo a tsiku lomwelo zitanenepa komanso kukula kuposa momwe zinaliri.

“Palibe chomwe chidzatsale padziko lapansi popanda iye kuchigonjetsa ndi kuchilamulira, kupatula Makkah Mukarramah ndi Madinah Munawwarah. Sadzayandikira mizinda iwiriyi kuchokera m’njira zawo zilizonse kupatula kuti angelo adzaima naye ndi malupanga ochotsa kale mmalo mwake, mpaka atakhala pa phiri laling’ono lofiira komwe malo amchere athera.” (Ibnu Maajah #4077)

Zivomerezi Zitatu ku Madinah Munawwarah

Madinah Munawwarah idzakumana ndi zivomerezi zitatu m’kanthawi kochepa. Anthu onse omwe anali ofooka komanso osasamala mu Dini adzatuluka mu Madinah Munawwarah kuopa zivomerezi. Mwanjira imeneyi, Allah Ta‘ala adzayeretsa Madinah Munawwarah kwa ma munaafiqiin (onyenga). (Ibnu Maajah #4077) Akatuluka, adzagwidwa ndi Dajjaal.

Padzakhala munthu opembedza kwambiri amene adzatuluke mu Madinah Munawwarah ndikukangana ndi Dajjaal. Dajjaal adzakwiya ndikupha munthu opembedzayu. Akadzamupha, Dajjaal adzamuukitsa ndikumufunsa kuti, “Kodi tsopano ukukhulupirira kuti ndine Allah?” Adzayankha kuti, “Tsopano ndatsimikiza kuti ndiwe Dajjaal.” Dajjaal adzayesa kumumenya koma sadzatha kutero, komanso sadzakhala ndi mphamvu pa iye mwanjira iliyonse, chifukwa Allah Ta‘ala adzamuchotsera mphamvu zake. (Muslim #2937)

Check Also

Moyo Wa Nabi Issah Alaihis Salaam Akadzabweranso Padziko Lapansi Ndi Kuchuluka Kwa Madalitso Ndi Chitetezo Mnthawi Yake

Nabi Isa (‘alaihis salaam) akadzabwerera padziko lapansi, Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) adzakhala mtsogoleri otsogolera Asilamu. Mahdi …