Mmene Allah Taala Amazisamalilira Zolengedwa Zake

1. Allah Taala ndi wachisoni kwambiri kwa akapolo ake. Ndipo Iye Allah amakonda kwambiri akapolo, wodekha kwa akapolo ake komanso opilira kwambiri. Iye amakhululuka machimo ndiponso amalandila kulapa kwa akapolo ake.[1]

2. Allah Taala ndi mwini chilungamo chonse. Iye sapondereza akapolo ake ngakhale mpang´ono pomwe.[2]

3. Allah Taala anamupatsa munthu kukhala omvetsa komanso kukwanitsa kusankha pakati pachabwino ndi choipa. Allah Taala amasangalatsidwa ndi akapolo ake okhulupilira amene amagwira ntchito zabwino pofuna kusangalatsa Allah yekha. ndiponso samasangalatsidwa ndi akapolo omwe amagwira ntchito zauchimo.[3]

4. Allah Taala ndimwini ulemelero ndi ukulu onse. Allah Taala ndimwini mphamvu zonse kuposa china chilichonse. Palibe chilichonse chomwe chingaposere mphamvu zake ndi zofuna zake. Amapereka ulemerero kwa amene wamufuna ndiponso amapereka kunyozeka kwa amene wamufuna. Allah Taala amachita chomwe wafuna ndipo safunsa wina aliyense muzolengedwa zake.[4]

5. Allah Taala ndimwini kudyetsa ndipo amadyetsa zolengedwa zake zonse. Iye amachepetsa riziq kwa amene wamufuna ndipo amamuchulukitsira riziq amene wamufuna.[5]


[1] وَرَحْمَتىْ وَسِعَتْ كُلَّ شَىءٍ (سورة الاعراف: 156)

إِنَّ اللّٰـهَ يَغْفِرُ الذُّنُوْبَ جَمِيْعًا ۚ  إِنَّهُ هُوَ الغَفُوْرُ الرَّحِيْمُ  (سورة الزمر: 53)

(ويغفر ما دون ذلك لمن يشاء من الصغائر والكبائر) مع التوبة أو بدونها (شرح العقائد النسفية  صـ 142)

[2] إِنَّ اللّٰـهَ لا يَظْلِمُ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ (سورة النساء: 40)

إنه لا يظلم أحدا إثبات أنه عدل في حكمه (الأسماء والصفات للبيهقي 1/108)

[3] وللعباد أفعال اختيارية يثابون بها ويعاقبون عليها (العقائد النسفية صـ 113)

وَهَدَيْنٰهُ النَّجْدَيْنِ (سورة البلد: ١٠)

[4] مَنْ كَانَ يُرِيْدُ الْعِزَّةَ فَلِلّٰـهِ الْعِزَّةُ جَمِيْعًا (سورة فاطر: 10)

وَتُعِزُّ مَنْ تَشَاءُ وَتُذِلُّ مَنْ تَشَاءُ (سورة آل عمران: 26)

لا يُسْـَٔلُ عَمَّا يَفْعَلُ وَهُمْ يُسْـَٔلُوْنَ (سورة الأنبياء: 23)

إِنَّ رَبَّكَ فَعَّالٌ لِما يُريدُ (سورة هود: 107)

ذلك بأنه على كل شيء قدير وكل شيء إليه فقير وكل أمر عليه يسير لا يحتاج إلى شيء (العقيدة الطحاوية صـ 26)

[5] اللَّـهُ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَنْ يَشَاءُ وَيَقْدِرُ (سورة الرعد: 26)

خالق بلا حاجة رازق لهم بلا مؤنة (العقيدة الطحاوية صـ 25)

Check Also

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti …