Zikhulupiliro Zokhudza Mtumiki Wa Allah Muhammad (Sallallah alayhi wasallam)

5. Allah Ta’ala adamudalitsa Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) ndi zabwino zapadera zimene Atumiki ndi aneneri a Mulungu sadapatsidwe. Mtumiki (salallah alayhi wasallama) akusimba kuti:

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن النبي صلى الله عليه وسلم قال: فضلت على الأنبياء بست: أعطيت جوامع الكلم، ونصرت بالرعب، وأحلت لي الغنائم، وجعلت لي الأرض مسجدا وطهورا، وأرسلت إلى الخلق كافة، وختم بي النبيون (رواه الترمذي، الرقم: ١٥٥٣ وقال: هذا حديث حسن صحيح)

(Ndadalitsidwa ndi zinthu zisanu ndi chimodzi (6), zimene atumiki akale sadapatsidwepo, Ndadalitsidwa popatsidwa jawaamil al kalaam (Mau amodzi koma amatanthauzo ochuluka, mwachitsanzo Quran yolemekezeka komanso mahadith olemekezeka muli matanthauzo akuluakulu kuchokera mu mau ochepa), Ndapulumutsidwa ndi mantha amene azilowa m’mitima ya ma kafir pondiopa ine kumenyana nawo ngakhale nditakhala pa mtunda oyenda mwezi wa tunthu, Chuma chotolatola kunkhondo chalorezedwa kwa ine kugwiritsa ntchito, Nthaka yonse yapangidwa kwa ine kukhala malo opemphereramo ndiponso yapangidwa kwa ine kukhala yodziyeretsera (twaharah) (mwachitsanzo kupanga tayammam ndi dothi ngati palibe madzi), Ndinatumizidwa kukhala Mtumiki ku zolengedwa zonse anthu ndi ziwanda ndiponso ndiine omaliza mwa atumiki a Allah.[1] 

6. M’dalitso waukulu kwambiri omwe Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adalandira kuchokera kwa Allah Ta’ala ndi Mi´iraj. Mi’raaj ndi ulendo odabwitsa umene Mtumiki (salallah alayhi wasallam) anatengedwa kuchokera ku Makkah kupita ku Baytul Maqdis. Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adatengedwa pa ulendo umenewu ndi thupi lake komanso asakugona. Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adalamuridwa kuti awapempheretse atumiki onse a Allah swalah zimene zikutanthauza kuti Iye Muhammad (sallallah alayhi wasallam) ndi mtsogoleri wa atumiki onse a Allah. Kuchokera pamenepa (Baytul Maqdis) Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) adatengedwa kupititsidwa ku mwamba ku mitambo seveni komanso adaposera (kumitambo 7) mpakana adadalitsidwa poiwona Jannah ndi Jahannam komanso adalemekezedwa poyankhulana ndi Allah Ta’ala. Mu ulendo umenewu ndi umene Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adapatsidwa mphatso ya swalah zisanu patsiku.[2] 


[1] عن أبي هريرة رضي الله عنه أن النبي صلى الله عليه وسلم قال: فضلت على الأنبياء بست: أعطيت جوامع الكلم، ونصرت بالرعب، وأحلت لي الغنائم، وجعلت لي الأرض مسجدا وطهورا، وأرسلت إلى الخلق كافة، وختم بي النبيون (رواه الترمذي، الرقم: ١٥٥٣ وقال: هذا حديث حسن صحيح)

[2]سُبْحٰنَ الَّذِىْ أَسْرٰى بِعَبْدِهِ لَيْلًا مِّنَ المَسْجِدِ الحَرَامِ إِلَى المَسْجِدِ الْاَقْصَا الَّذِىْ بٰرَكْنَا حَوْلَهُ لِنُرِيَهُ مِنْ اٰيٰتِنَا ج إِنَّهُ هُوَ السَّمِيْعُ البَصِيْرُ (سورة بني إسرائل: ١)

فالإسراء وهو من المسجد الحرام إلى بيت المقدس قطعي ثبت بالكتاب والمعراج من الأرض إلى السماء مشهور ومن السماء إلى الجنة أو على العرش أو غير ذلك آحاد (شرح العقائد النسفية صـ ١٧٠)

والمعراج حق وقد أسري بالنبي صلى الله عليه وسلم وعرج بشخصه في اليقظة إلى السماء ثم إلى حيث شاء الله من العلى وأكرمه الله بما شاء وأوحى إلى عبده ما أوحى (العقيدة الطحاوية صـ ٢٨)

والمعراج لرسول الله عليه السلام فى اليقظة بشخصه إلى السماء ثم إلى ما شاء الله تعالى من العلى حق (العقائد النسفية صـ ١٦٩)

Check Also

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti …