Masunnah Ndi Miyambo Ya Pakudya 2

Ma Sunnah ndi Miyambo Musanadye

5. Sambani m’manja musanayambe kudya.

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: Kusamba m’manja usanayambe kudya komanso ukamaliza kumachotsa umphawi, ndipo ndi zochokera mu sunnah ya Ambiya onse (alaihimus salaam).

6. Ndibwino kuti kuvula nsapato usanayambe kudya.

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Chakudya chikaikidwa (pa dastarkhaan – nsalu yodyera -), vulani nsapato zanu.”

7. Werengani bismillah kapena dua yotsatirayi musanayambe kudya. Ngati mukudya ndi banja lanu, mutha kuiwerenga motulutsa mawu kuti muwakumbutse ena.

بِسْمِ اللهِ وَبركة الله

M’dzina la Allah komanso madalitso a Allah

8. Mukamadya, khalani pansi ndi maondo onse awiri (ngati mene mumakhalira pa tashahhud pa swalah), kapena khalani moimika bondo lakumanja.

9. Dyerani ndi kumwera dzanja lamanja.

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati Aliyense akafuna kudya kapena kumwa, adyere dzanja lake lamanja ndi kumwera dzanja lomwelo.”

Check Also

Zul Hijjah

Mwezi wa Zul Hijjah uli mgulu la miyezi inayi yopatulika ya kalendala ya Chisilamu. Miyezi …