Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachiwiri

4. Sambitsani m'manja katatu.

Sayyiduna Humraan (rahimahullah) kapolo omasuridwa wa Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: Sayyiduna Uthman (radhwiiyallahu anhu) anapempha madzi (kuti awaonetse anthu kapangidwe ka wudhu. kenaka anayama kupanga wudhu posambitsa manja ake (mpaka molumikizanirana dzanja) katatu (izi zafotokozedwazi zomwe zikupezeka mu sahihul bukhari sayyiduna Uthman (Radhwyallahu anhu) anati: ndidamuona Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) akupanga wudhu motere)."

Read More »

Ma Ubwino A Wudhu

1. Wudhu ndi chiyeretso chamachimo ang’ono ang’ono.

Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akuti; Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Amene angachite-wudhu, ndipo nawuchita wudhuwo mkachitidwe kabwino kwambiri, Machimo ake (ang´onoang´ono) amafudutidwa (ndipo amatsukidwa) kuchokera mthupi mwake mpakana amagwa machimo kudzera pansi pa-zikhadabo.

Read More »

Masaail (Nfundo) Zina Zokhudza Kuzithandiza Kuchimbudzi

1. Funso: kodi ndizoloredwa munthu kuwerenga mabukhu monga nyuzi ndi magazini, kapena kugwiritsa ntchito foni, kapenanso kuseweretsa intaneti pamene ali m’nchimbudzi?

Yankho: Chimbudzi ndi malo amene munthu amazithandizirako, Choncho sizabwino kwa munthu kugwiritsa ntchito foni yake kapena kuwerenga uthenga uliwonse kapena kuwerenga nkhani m'nchimbudzi.

Read More »

Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachinayi

11. Musayankhule pamene mukudzithandiza, pokhapokha patafunikira kuti mulankhule.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, anthu awiri asakadzithandizire malo amodzi komwe akakhale ndikumayankhulana maliseche awo ali pantetete (osavala) ndithudi Allah Ta'ala amadana ndi nchitidwe otelewu.’’

Read More »

Chenjezo Kwa Osasamala Za Ukhondo Akamapanga Istinja (Kutawasa)

Hadith yoyamba

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:"Chilango chachikulu (chomwe anthu ambiri amakumana nacho) m'manda ndi chifukwa cha nkodzo (kusasamala nkodzo omwe umadonthekera pathupi komanso unve wina. kotero, wudhu wawo, swalah ndi ibadah ina siidzalandiridwa chifukwa chosowekera ukhondo)"

Read More »